Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Ndinali Munthu Wodzikonda Kwambiri

Ndinali Munthu Wodzikonda Kwambiri
  • CHAKA CHOBADWA: 1951

  • DZIKO: GERMANY

  • POYAMBA: NDINALI WONYADA KOMANSO WOSAFUNA KUUZIDWA ZOCHITA

KALE LANGA:

Ndili mwana, banja lathu linkakhala kufupi ndi mzinda wa Leipzig ku East Germany. Mzindawu uli kufupi ndi malire a dziko la Czech ndi Poland. Ndili ndi zaka 6, tinasamukira ku Brazil komwe bambo ankagwira ntchito ndipo kenako tinasamukiranso ku Ecuador.

Ndili ndi zaka 14, ananditumiza kusukulu yogonera komweko m’dziko la Germany. Popeza makolo anga anali kutali, ndinkasankha ndekha zochita ndipo zimenezi zinapangitsa kuti ndiyambe kudzidalira kwambiri. Sindinkaganizira n’komwe mmene zochita zanga zinkakhudzira anthu ena, ndinkangoti bola zanga ziyende.

Ndili ndi zaka 17, makolo anga anabwereranso ku Germany ndipo ndinayamba kukhala nawo limodzi. Koma chifukwa choti ndinali nditazolowera kusankha ndekha zochita, zinkandivuta kuwamvera. Choncho ndili ndi zaka 18 ndinachoka panyumba.

Komabe zinthu sizinkandiyendera kwenikweni ndipo ndinkaona kuti moyo wanga ulibe phindu. Ndinayamba kuchita zinthu ndi anthu komanso magulu osiyanasiyana, komabe sizinandithandize kukhala wosangalala. Choncho ndinaganiza kuti ndiyambe kuyenda m’mayiko osiyanasiyana padzikoli n’kumaona zinthu zachilengedwe. Popeza zinthu zachilengedwe zikutha, ndinkaona kuti ndi bwino ndiyende m’malo osiyanasiyana n’kumaona zinthu zachilengedwezi, zisanatheretu.

Ndinagula njinga yamoto ndipo ndinasamuka ku Germany n’kupita ku Africa. Koma pasanapite nthawi njingayi inawonongeka ndipo ndinaganiza zobwereranso ku Europe kuti ndikaikonzetse. Koma nditafika pagombe lina ku Portugal, ndinaganiza zoti ndisiye kuyenda pa njinga yamoto n’kuyamba kuyenda paboti moti njingayo ndinaisiya komweko.

Ndinaganiza zoyenda limodzi ndi gulu lina la achinyamata omwe ankakonzekera kuwoloka nyanja ya Atlantic. Pagululi panali mtsikana wina, dzina lake Laurie, ndipo patapita nthawi tinakwatirana. Poyamba tinapita kuzilumba za Caribbean. Tinakhala kwa nthawi yochepa ku Puerto Rico, ndipo kenako tinabwereranso ku Europe. Tinkafuna titapeza boti loti tikhoza kulisintha n’kukhala nyumba yathu. Tinasakasaka botili kwa miyezi itatu, koma tisanalipeze asilikali a boma la Germany anandigwira n’kundilemba ntchito yausilikali.

 Ndinali m’gulu la asilikali apamadzi ndipo ndinagwira ntchitoyi kwa miyezi 15. Pa nthawiyi, ine ndi Laurie tinakwatirana ndipo tinakonza zoti tipitirize kuyenda m’mayiko osiyanasiyana. Pa nthawi imene ndinkagwira ntchito yausilikali, tinagula boti ndipo tinalikonza kuti likhalenso nyumba yathu. Tinkafuna kuti tizikhala m’botilo kwinaku tikupitiriza kuyenda m’mayiko osiyanasiyana n’kumaona zachilengedwe. Nditasiya ntchito yausilikali ndinapitiriza kukonza botilo. Botili lisanathe tinakumana ndi a Mboni za Yehova ndipo tinayamba kuphunzira Baibulo.

MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:

Poyamba ndinkaona ngati sindikufunika kusintha zambiri pa moyo wanga. Ndinkaganiza zimenezi chifukwa ndinkaona kuti mkazi amene ndinkakhala naye, ndinakwatirana naye mwalamulo komanson’kuti nditasiya kale kusuta. (Aefeso 5:5) Ndinkaonanso kuti zimene tinkachita, pomayenda m’mayiko osiyanasiyana, zinalibe vuto chifukwa zinkatithandiza kuti tiziona chilengedwe chokongola cha Mulungu.

Koma zoona zake n’zakuti, ndinkafunika kusintha zambiri pa moyo wanga makamaka khalidwe langa. Popeza ndinali wodzikonda komanso wosafuna kuuzidwa zochita, ndinkangoganizira kwambiri za luso langa komanso zimene ndinakwanitsa kuchita. Ndinali womva zanga zokha.

Tsiku lina ndinawerenga za ulaliki wa paphiri wa Yesu, womwe ndi wotchuka kwambiri. (Mateyu chaputala 5 mpaka 7) Poyamba sindinkamvetsa zimene Yesu ananena zokhudza kukhala osangalala. Mwachitsanzo, ananena kuti anthu anjala komanso aludzu amakhala osangalala. (Mateyu 5:6) Ndinkadabwa kuti zingatheke bwanji kuti munthu waludzu komanso wanjala akhale wosangalala. Nditapitiriza kuphunzira, ndinazindikira kuti tonse tili ndi njala komanso ludzu lauzimu. Koma kuti tipeze zinthu zauzimu zofunikazi, timafunika kuzindikira modzichepetsa kuti tikufunikira zimenezi pa moyo wathu. Izi n’zogwirizana ndi zimene Yesu ananena kuti: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”—Mateyu 5:3.

Titaphunzira Baibulo kwa kanthawi ku Germany, tinasamukira ku France, ndipo kenako tinasamukiranso ku Italy. Kulikonse kumene tinkapita tinkakumana ndi a Mboni. Chinthu chimene chinkandichititsa chidwi kwambiri n’choti anali ogwirizana komanso ankakondana kwambiri. Ndinazindikira kuti a Mboni za Yehova ali ngati banja limodzi ndipo amapezeka padziko lonse. (Yohane 13:34, 35) Patapita nthawi, ine ndi mkazi wanga tinabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova.

Nditabatizidwa, ndinkafunikabe kusintha zina ndi zina pa moyo wanga. Ine ndi mkazi wanga tinaganiza zopita ku United States kudzera m’nyanja ya Atlantic. Pa ulendowu, tili pakatikati pa madzi, ndinayamba kuganizira kwambiri za Mlengi wathu, yemwe ndi wodabwitsa kwambiri. Ndinazindikira kuti anthufe ndife otsika kwambiri poyerekeza ndi Mlengi. Chifukwa choti pa ulendowu ndinali ndi nthawi yambiri, ndinayamba kuwerenga Baibulo. Nkhani imene inandisangalatsa kwambiri inali yokhudza zimene Yesu anachita ali padziko lapansi. Yesu anali munthu wangwiro ndipo ankatha kuchita zinthu zogometsa kwambiri, koma ankapeza nthawi yothandiza anthu ena. Iye ankagwiritsa ntchito nthawi yake kuchita zofuna za Atate ake akumwamba.

Ndinaona kuti ndi bwino ndizigwiritsa ntchito nthawi yanga kuuza ena za Ufumu wa Mulungu m’malo momangochita zofuna zanga

Chitsanzo cha Yesu chinandithandiza kudziwa kuti ndinkafunika kugwiritsa ntchito nthawi yanga kuuza ena za Ufumu wa Mulungu m’malo momangochita zofuna zanga. (Mateyu 6:33) Choncho titafika ku United States, tinaganiza zokhazikika komweko kuti tizikhala ndi nthawi yokwanira yotumikira Yehova.

PHINDU LIMENE NDAPEZA:

Pa nthawi imene ndinali munthu wosafuna kuuzidwa zochita ija, nthawi zina ndinkalephera kudziwa zoyenera kuchita. Koma panopa, Mawu a Mulungu amandithandiza kusankha zinthu mwanzeru. (Yesaya 48:17, 18) Komanso panopa ndikuona kuti moyo wanga uli ndi phindu chifukwa ndikutumikira Mulungu ndipo ndimathandiza ena kudziwa za iye.

Kutsatira mfundo za m’Baibulo kwathandiza kuti banja lathu likhale lolimba komanso lokondana. Tilinso ndi mwana wamkazi wokongola kwambiri, ndipo nayenso amakonda Yehova.

Sikuti moyo wathu ndi wopanda mavuto. Komabe Yehova amatithandiza ndipo timaona kuti sitidzasiya kumukhulupirira—Miyambo 3:5, 6.