BAIBULO LIMASINTHA ANTHU
Baibulo Linandithandiza Kupeza Mayankho a Mafunso Anga
-
CHAKA CHOBADWA: 1987
-
DZIKO: AZERBAIJAN
-
POYAMBA: BAMBO ANGA ANALI MSILAMU POMWE MAYI ANGA ANALI MYUDA
KALE LANGA:
Ndinabadwira mumzinda wa Baku ku Azerbaijan. M’banja mwathu tilipo ana awiri ndipo ineyo ndi womaliza. Bambo anga anali Msilamu pomwe mayi anga anali Myuda. Ngakhale kuti anali osiyana zipembedzo, ankakondana kwambiri ndipo aliyense ankalemekeza zimene mnzake ankakhulupirira. Mwachitsanzo, bambo akamasala m’mwezi wa Ramadan, mayi ankawathandiza. Nawonso mayi akamachita pasika, bambo ankawathandiza. Tinali ndi Korani, Tora komanso Baibulo.
Ineyo ndinkadzitenga kuti ndine Msilamu. Ngakhale kuti sindinkakayikira kuti kuli Mulungu, panali mafunso ena omwe ankandizunguza mutu. Mwachitsanzo, ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu analengeranji anthufe? Kodi anatilenga kuti tizivutika kenako n’kudzatilanga kumoto kwamuyaya?’ Anthu ambiri amanena kuti chilichonse chomwe chimachitika, n’chifuniro cha Mulungu. Ndiye ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu amagwiritsa ntchito anthu ngati zidole zake, ndipo akamavutika iye amasangalala?’
Ndili ndi zaka 12, ndinayamba kupemphera mapemphero achisilamu ka 5 tsiku lililonse. Pa nthawiyi, bambo anatitumiza kusukulu yachiyuda. Kusukuluku tinkaphunzira Chiheberi komanso miyambo ya m’buku la Tora. Tisanayambe kuphunzira, tinkapemphera mogwirizana ndi miyambo yachiyuda. Choncho, m’mawa ndinkapemphera mapemphero achisilamu kunyumba, ndipo ndikapita kusukulu ndinkapemphera mapemphero achiyuda.
Ndinkalakalaka nditapeza mayankho ogwira mtima a mafunso anga. Nthawi zambiri ndinkafunsa arabi kuti: “Kodi Mulungu analengeranji anthufe? Kodi Mulungu sasangalala ndi bambo anga chifukwa choti ndi Msilamu? Bambo anga ndi munthu wabwino, ndiye n’chifukwa chiyani anthu ena amawaona kuti ndi odetsedwa? Nanga n’chifukwa chiyani Mulungu anawalenga?” Koma zimene ankandiyankha zinali zosagwira mtima.
MMENE BAIBULO LINASINTHIRA MOYO WANGA:
Zimene zinachitika mu 2002 zinachititsa kuti ndisiye kukhulupirira Mulungu.
Pa nthawiyi tinali titasamukira ku Germany ndipo patangotha mlungu umodzi, bambo anga anadwala matenda ofa ziwalo. Kuyambira pa nthawiyi ankangokhala chikomokere. Kwa zaka zambiri ndinkapemphera kwa Mulungu kuti aziteteza banja lathu. Popeza ndinkakhulupirira kuti Mulungu ali ndi mphamvu zochita chilichonse, ndinkapemphera kwa iye tsiku ndi tsiku kuti bambo anga achire. Ndinkaganiza kuti, ‘Kapempho kangaka n’kakang’ono, Mulungu sangalephere kundiyankha.’ Koma n’zomvetsa chisoni kuti bambo anga anamwalira.Ndinadabwa kwambiri kuti n’chifukwa chiyani Mulungu sanayankhe pemphero langa. Ndinkadzifunsa kuti, ‘Kodi n’chifukwa choti sindipemphera bwino? Kapena Mulungu kulibe?’ Ndinakhumudwa kwambiri moti ndinasiya kupemphera. Komanso ndinkaona kuti zipembedzo zina siziphunzitsa zolondola, choncho ndinasiya kukhulupirira zoti kuli Mulungu.
Patatha miyezi 6, kunyumba kwathu kunabwera a Mboni za Yehova. Popeza tinkaona kuti Akhristu saphunzitsa zoona, ine ndi mchemwali wanga tinaganiza kuti tiwathandize mwaulemu kudziwa kuti amakhulupirira zabodza. Choncho, tinawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani Akhristunu mumalambira Yesu, mtanda, Mariya ndi mafano ena, zomwe n’zosagwirizana ndi Malamulo Khumi?” A Mboniwa anatisonyeza kuchokera m’Baibulo umboni woti Akhristu sayenera kulambira mafano komanso kuti ayenera kupemphera kwa Mulungu basi. Zimenezi zinandidabwitsa kwambiri.
Kenako tinawafunsa kuti: “Nanga mumakhulupirira zotani pa nkhani ya Utatu? Ngati Yesu ndi Mulungu, zinatheka bwanji kuti abwere padziko lapansi n’kudzaphedwa ndi anthu?” Apanso anagwiritsa ntchito Baibulo ndipo anatiuza kuti Yesu si Mulungu komanso mphamvu zake si zofanana ndi za Mulungu. Anatifotokozeranso kuti chifukwa cha zimenezi, sakhulupirira kuti pali Mulungu Atate, Mulungu Mwana ndi Mulungu Mzimu Woyera. Ndinadabwa kwambiri kuti, ‘Akhristu amenewa ndiye atinso?’
Komabe ndinkafuna nditadziwa kuti n’chifukwa chiyani anthu amafa komanso n’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti anthufe tizivutika. A Mboniwa anandionetsa buku lakuti, Chidziwitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. * M’bukuli muli mitu yomwe ili ndi mayankho a mafunso angawa. Ndinasangalala ndi zomwe ndinaphunzira ndipo kenako ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboniwa.
Tikamaphunzira, ndinkapeza mayankho ogwira mtima a mafunso anga. Ndinaphunzira kuti dzina la Mulungu ndi Yehova ndipo khalidwe lake lalikulu ndi chikondi. (Salimo 83:18; 1 Yohane 4:8) Ndinazindikira kuti Mulungu analenga anthu chifukwa ankafuna kuti azisangalala ndi moyo. Ndinadziwanso kuti ngakhale kuti Mulungu amalola kuti zoipa zizichitika, amadana nazo ndipo posachedwapa adzathetsa mavuto onse. Ndinaphunzira kuti mavuto onse, kuphatikizapo imfa, anayamba chifukwa cha kusamvera kwa Adamu ndi Hava. (Aroma 5:12) Zimenezi zinandithandiza kumvetsa chifukwa chake bambo anga anamwalira. Koma ndinalimbikitsidwa nditadziwa kuti m’dziko latsopano, Mulungu adzaukitsa anthu omwe anamwalira.—Machitidwe 24:15.
Apatu Baibulo linandithandiza kupeza mayankho a mafunso anga onse. Choncho ndinayambanso kukhulupirira Mulungu. Ndinadziwanso kuti a Mboni za Yehova amapezeka padziko lonse, ndi ogwirizana komanso amakondana. Zimenezi zinandichititsa chidwi kwambiri. (Yohane 13:34, 35) Nditaphunzira zambiri zokhudza Yehova, ndinaganiza zoyamba kumutumikira. Choncho pa 8 January 2005, ndinabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.
PHINDU LIMENE NDAPEZA:
Zimene ndaphunzira m’Baibulo zandithandiza kuti ndiyambe kuona zinthu moyenera. Zandithandizanso kuti ndizikhala ndi mtendere wamumtima. Ndimasangalalanso kwambiri ndikaganiza kuti ndidzawaonanso bambo anga akadzaukitsidwa.—Yohane 5:28, 29.
Ndinakwatiwa ndi mwamuna woopa Mulungu, dzina lake Jonathan, ndipo takhala m’banja za 6. Banja lathu ndi losangalala ndipo timaona kuti zimene Baibulo limaphunzitsa zokhudza Mulungu ndi zosavuta kumvetsa. Timaona kuti chimenechi ndi chuma cha mtengo wapatali. N’chifukwa chake timakonda kuuza anthu zomwe timakhulupirira. Poyamba paja sindinkadziwa zambiri zokhudza Mboni za Yehova, koma panopa ndimadziwa kuti a Mboni ndi Akhristu oona.
^ ndime 15 Bukuli ndi lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova, koma anasiya kulisindikiza.