Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukudziwa?

Kodi Mukudziwa?

Kodi kapitawo wa asilikali achiroma ankagwira ntchito yotani?

Chipilala cha Marcus Favonius facilis yemwe anali kapitawo

M’Malemba Achigiriki kapena kuti m’Chipangano Chatsopano, muli mavesi ambiri amene amatchula za akapitawo achiroma. Woyamba ndi munthu amene anaimirira pafupi, nthawi imene Yesu ankapachikidwa. Wina anali Koneliyo, yemwe anali munthu woyamba wa mtundu wina kukhala Mkhristu. Winanso ndi Yuliyo amene anaperekeza Paulo ku Roma. Ndipo munthu wina amene anali kapitawo, ndi munthu amene anali ndi udindo woonetsetsa kuti Paulo wakwapulidwa.—Maliko 15:39; Machitidwe 10:1; 22:25; 27:1.

Kapitawo ankatsogolera gulu la asilikali oyenda pansi okwana 100 kapena kucheperapo. Ntchito yake inali kuphunzitsa asilikali, kuwatsogolera akamamenya nkhondo komanso kuwapatsa malangizo. Ankaonetsetsanso kuti zovala ndi zida za gulu la asilikali ake zili bwino.

Kukhala kapitawo wa asilikali unali udindo waukulu moti msilikali aliyense ankalakalaka atakhala pa udindowu. Asilikali omwe ankapatsidwa udindowu ankakhala oti agwira ntchitoyi kwa nthawi yaitali ndipo ali ndi luso lotsogolera ena. Kuti gulu la asilikali ake likhale losunga mwambo komanso kuti lizigwira bwino ntchito, zinkadalira kapitawo wa gululo. Buku lina linanena kuti akapitawo “ankakhala anthu odziwa kwambiri ntchito yawo komanso anzeru kuposa asilikali ena onse.”

Kodi magalasi odziyang’anira akale anali osiyana bwanji ndi a masiku ano?

Chithunzi cha galasi lakale la ku Iguputo

Magalasi odziyang’anira akale anali osiyana kwambiri ndi a masiku ano. Magalasi akalewa nthawi zambiri ankapangidwa ndi buronzi. Koma nthawi zina ankawapanga ndi mkuwa, siliva, golide kapena golide wosakaniza ndi siliva. Baibulo limatchula koyamba za magalasi odziyang’anira oterewa pamene limanena za zinthu zomwe anagwiritsa ntchito pomanga chihema, malo omwe Aisiraeli ankakalambirirako. Azimayi anapereka magalasi awo kuti awasungunule n’kupangira beseni losambira la mkuwa ndi choikapo chake.—Ekisodo 38:8.

Ku Israel ndi m’madera ozungulira, anafukulako magalasi a ngati amenewa. Pamalo omwe anapezapo magalasiwa, anapezaponso zinthu zina zimene azimayi amavala podzikongoletsa monga zibangiri. Nthawi zambiri magalasiwa ankakhala ozungulira ndipo ankakhala ndi chogwirira chathabwa, chachitsulo kapena chanyanga ya njovu. Chogwirirachi kawirikawiri chinkakhala chooneka ngati kamzimayi. Nthawi zambiri kuseri kwa magalasiwa sankakukongoletsa.

Magalasi akalewa sanali oonetsa bwino chithunzi cha munthu tikayerekezera ndi a masiku ano. Mwina n’chifukwa chake mtumwi Paulo ananena za magalasi amenewa kuti: “Pa nthawi ino sitikuona bwinobwino chifukwa tikugwiritsa ntchito galasi losaoneka bwinobwino.”—1 Akorinto 13:12.