Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Kodi anthu adzakhala ndi moyo wotani m’tsogolo?
N’zodziwikiratu kuti asayansi apitirizabe kupanga zinthu zamakono zomwe zisinthe mmene timachitira zinthu ndi ena. Koma kodi zimenezi zidzathandiza kuti anthu padzikoli ayambe kuchita zinthu moganizirana? Ayi. Anthu ambiri m’dzikoli ndi odzikonda komanso adyera. Koma cholinga cha Mulungu n’choti anthu adzakhale osangalala padzikoli.—Werengani 2 Petulo 3:13.
Baibulo limanena kuti m’tsogolomu anthu padziko lonse adzakhala ogwirizana komanso okondana kwambiri. Anthu adzakhala otetezeka chifukwa palibe adzawachitire zoipa.—Werengani Mika 4:3, 4.
Kodi Mulungu adzathetsa bwanji kudzikonda?
Mulungu analenga anthu opanda mtima wodzikonda. Koma chifukwa chosamvera Mulungu, Adamu yemwe anali munthu woyamba, anataya mwayi wokhala wangwiro. Anthufe tinatengera mtima wodzikonda kuchokera kwa Adamu, yemwe ndi kholo lathu. Komabe Mulungu adzagwiritsa ntchito Yesu kuti athandize anthu kukhalanso angwiro.—Werengani Aroma 7:21, 24, 25.
Kuti zimenezi zidzatheke, Yesu anatifera kuti alipire kusamvera kwa Adamu. (Aroma 5:19) Imfa ya Yesu idzathandiza kuti anthu onse okhala padzikoli asamadzachite zoipa chifukwa cha mtima wodzikonda.—Werengani Salimo 37:9-11.