Kodi Mukudziwa?
Kodi anthu akale ankagwiritsa ntchito bwanji mphero?
Kale, anthu ankagwiritsa ntchito mphero popera ufa akafuna kupanga buledi. Pafupifupi nyumba iliyonse azimayi kapena a ntchito ankagwiritsa ntchito mphero. Moti tsiku lililonse kunkamveka phokoso losonyeza kuti munthu akupera ufa.—Ekisodo 11:5; Yeremiya 25:10.
Zithunzi zakale zojambulidwa kapena zoumbidwa, zimasonyeza mmene anthu a ku Iguputo ankagwiritsira ntchito mphero. Ankaika tirigu pa mwala wolowa mkati pang’ono womwe ankaumata pamwala wina waukulu komanso wafulati. Munthu woperayo ankagwada pafupi ndi mwalawo ndipo ankatenga mwala waung’ono woperera n’kumayendetsa pa mwala wolowa mkati pang’ono uja. Iye ankagwira mwala wopererawo ndi manja onse n’kumauyendetsa kupita kutsogolo ndi kumbuyo ndipo tiliguyo ankakhala ufa. Ena amanena kuti miyala yopererayi inkalemera makilogalamu awiri kapena 4, ndipo inali yoti munthu akhoza kufa ngati atamenyedwa nayo.—Oweruza 9:50-54.
Banja lililonse linkafunika kupera tiligu kuti lipeze chakudya. N’chifukwa chake lamulo la m’Baibulo linkaletsa munthu kutenga mwala woperera ngati chikole cha ngongole. Lemba la Deuteronomo 24:6 limati: “Munthu asalande mnzake mphero kapena mwala woperera monga chikole. Kumulanda zimenezi monga chikole ndiko kumulanda moyo.”
Kodi mawu akuti “pachifuwa”amatanthauza chiyani?
Baibulo limati Yesu “ali pachifuwa cha Atate.” (Yohane 1:18) Mawu amenewa akunena za ubwenzi wapadera umene Yesu ali nawo ndi Mulungu. Mawuwa amanenanso za zimene Ayuda ankachita akamadya.
M’nthawi ya Yesu, Ayuda akamadya ankakhala pamipando yokhala ngati sofa yomwe ankaiika mozungulira tebulo lodyera. Anthuwa ankatsamira mkono wamanzere papilo wa mpandowo ndipo mitu yawo inkaloza kutebulo. Zimenezi zinkachititsa kuti azigwiritsa ntchito bwinobwino dzanja lamanja. Buku lina linanena kuti, popeza onse ankatsamira mpandowo ndi mkono wamanzere ndipo wina ankakhala kumbuyo kwa mnzake, “mutu wa munthu amene ali patsogolo unkakhala pafupi ndi pamtima kapena kuti pachifuwa cha munthu amene wakhala pambuyo pake. Munthu amene wakhala pamenepa ankanenedwa kuti wakhala pachifuwa cha mnzakeyo.”
Anthu ankaona kuti ndi mwayi wapadera kukhala pachifuwa cha mutu wabanja kapena cha munthu amene wakonza phwando. N’chifukwa chake pa Pasika womaliza wa Yesu, mtumwi Yohane “amene Yesu anali kumukonda,” ndi amene anakhala pachifuwa chake. Iyi ndi nthawi imene Yohane “anatsamira pachifuwa pa Yesu ndi kumufunsa” funso.