Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI N’ZOTHEKA KUMVETSA ZIMENE BAIBULO LIMANENA?

Baibulo Ndi Buku Lomveka Bwino

Baibulo Ndi Buku Lomveka Bwino

Baibulo linayamba kulembedwa zaka 3,500 zapitazo ku Middle East. Pa nthawi imene linkayamba kulembedwa n’kuti ufumu wa Shang wa ku China uli wamphamvu kwambiri. Komanso panali patatsala zaka 1,000 kuti chipembedzo chachibuda chiyambe ku India.—Onani bokosi lakuti, “ Mfundo Zachidule Zokhudza Baibulo.”

Baibulo lili ndi mayankho a mafunso ofunika kwambiri amene anthu amakhala nawo

Koma mwina mungaganize kuti, ‘Ngati Baibulo lili lakale chonchi, ndiye kuti linatha ntchito.’ Komabe dziwani kuti ngakhale kuti linalembedwa kalekale, ndi lothandizabe kwambiri masiku ano. Ndi lomveka bwino komanso limayankha mogwira mtima mafunso ofunika kwambiri amene anthu amakhala nawo.

Mwachitsanzo, kodi munayamba mwadzifunsapo kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu anatilenga?’ Funso limeneli lakhala likuvutitsa maganizo anthu ambiri. Komatu mungadabwe kudziwa kuti m’Baibulo muli yankho la funsoli ndipo limapezeka m’machaputala awiri oyambirira a buku la Genesis. Mwachidule, machaputala awiriwa amafotokoza zimene zinachitika zaka mabiliyoni apitawo. Baibulo limanena kuti “pa chiyambi,” Mulungu analenga dziko lapansi, nyenyezi komanso zinthu zina za m’mlengalenga. (Genesis 1:1) Kenako anayamba kukonza dzikoli kuti pakhale zamoyo. Atachita zimenezi analenga zamoyo zosiyanasiyana. Pamapeto pake Mulungu analenga anthu n’kuwaika padziko lapansi. Baibulo limafotokozanso cholinga chimene Mulungu anali nacho pamene ankalenga anthu.

LINALEMBEDWA MOMVEKA BWINO

M’Baibulo muli malangizo abwino amene angatithandize tikamakumana ndi mavuto. Malangizo ake ndi osavuta kuwatsatira. Tikunena zimenezi pa zifukwa ziwiri.

Choyamba, Baibulo limanena zinthu momveka bwino komanso mosapita m’mbali. Lili ndi mawu osavuta kumva ndipo likamafotokoza zinthu zovuta, limagwiritsa ntchito mawu omwe anthu amawadziwa bwino.

Mwachitsanzo, Yesu anagwiritsa ntchito zitsanzo komanso mafanizo a zinthu zimene anthu ankazidziwa bwino ndipo zimenezi zinkawagwira mtima kwambiri. Zitsanzo zina komanso mafanizo amenewa anazitchula pa ulaliki wake wa paphiri ndipo m’Baibulo zimapezeka m’buku la Mateyu, machaputala 5 mpaka 7. Munthu wina ananena kuti zimene Yesu ananena pa ulalikiwu “zingatithandize kuti tikhale ndi moyo wabwino.” Mukhoza kuwerenga zimene Yesu ananena pa ulalikiwu, mwina kwa maminitsi 15 kapena 20 okha. Koma mungagome ndi mfundo zake chifukwa n’zomveka bwino komanso zothandiza kwambiri.

Chifukwa chachiwiri chimene chimapangitsa kuti Baibulo likhale lomveka bwino n’choti limafotokoza zochitika zenizeni. Baibulo ndi losiyana kwambiri ndi mabuku a nthano omwe amangofotokoza zinthu zam’maluwa. Buku lina linanena kuti nkhani zambiri za m’Baibulo “zimanena za anthu otchuka komanso ngakhale za anthu wamba.” Limanenanso mavuto amene anthuwo “ankakumana nawo, zimene ankayembekezera, zimene ankalakwitsa ndiponso zimene anachita bwino.” (The World Book Encyclopedia) M’Baibulo mulinso nkhani za anthu komanso zochitika zenizeni zomwe ifeyo tingaphunzirepo kanthu.—Aroma 15:4.

NDI BUKU LIMENE ALIYENSE AKHOZA KULIPEZA

Kuti munthu amvetse zimene buku likunena, bukulo liyenera kukhala m’chinenero chimene munthuyo amachimva bwinobwino. Masiku ano, Baibulo likupezeka m’zinenero zambiri zimene anthu amalankhula padzikoli. Koma kodi zimenezi zimatheka bwanji?

Ntchito yomasulira. Baibulo linalembedwa m’Chiheberi, Chiaramu komanso Chigiriki. Choncho, anthu amene sankadziwa zinenerozi sankamva uthenga wake. Ndiye pofuna kuthandiza anthu amenewa, anthu ena omasulira mabuku anayamba ntchito yomasulira Baibulo m’zinenero zina. Ntchito imene anthuwa anachita ndi yotamandika zedi, chifukwa panopa Baibulo lonse kapena mbali yake, likupezeka m’zinenero pafupifupi 2,700. Zimenezi zikusonyeza kuti pa anthu 100 alionse, anthu 90 akhoza kuwerenga Baibulo m’chinenero chawo.

Ntchito yosindikiza. Poyamba, Baibulo linkalembedwa pa zinthu zosachedwa kuwonongeka monga zikopa komanso pamapepala opangidwa ndi gumbwa. Chifukwa cha zimenezi, nthawi zonse akatswiri okopera mabuku ankayenera kumakopera Baibulo pamanja. Mabuku amenewa ankakhala odula kwambiri moti ndi anthu ochepa chabe amene ankapezeka nawo. Koma zaka zoposa 550 zapitazo, munthu wina dzina lake Gutenberg, anapanga mashini osindikiza mabuku ndipo zimenezi zinathandiza kuti Baibulo lizipezeka mosavuta. Kafukufuku wina anasonyeza kuti kungochokera nthawi imeneyo, Mabaibulo oposa 5 biliyoni kapena mbali yake, afalitsidwa.

Palibenso buku lina lachipembedzo limene limafalitsidwa kuposa Baibulo. Baibulo ndi losiyananso ndi mabuku amenewa chifukwa ndi losavuta kumva komanso limapezeka mosavuta. Ngakhale zili choncho, anthu ena amavutikabe kumvetsa zimene Baibulo limanena. Ngati nanunso mumavutika kulimvetsa, dziwani kuti anthu ena akhoza kukuthandizani. Koma kodi ndi ndani amene angakuthandizeni? Nanga mungapindule bwanji ngati mutamvetsa zimene Baibulo limanena? Werengani nkhani yotsatirayi kuti mudziwe mayankho a mafunso amenewa.