Kodi Anthu Adzasiya Kuchita Zachinyengo?
MAYI wina, dzina lake Panayiota, anakulira pa chilumba china cha m’nyanja ya Mediterranean. Ali mtsikana, ankafuna kudzakhala wandale, moti atakula anakhala mlembi wachipani china kudera limene ankakhala. Mayiyu ankapita kunyumba za anthu n’kumakapemphetsa ndalama zoti athandizire chipani chawo. Koma anakhumudwa kwambiri atazindikira kuti mamembala ambiri a chipani chawocho anali atambwali. Ankaona kuti akuluakulu a chipanicho anali atsankho moti ankangopereka maudindo kwa achibale ndi anzawo. Komanso anthu a m’chipani chawocho ankangokhalira kukangana komanso kuchitirana nsanje.
A Daniel omwe amakhala ku Ireland anakulira m’banja lokonda kwambiri zopemphera. Nawonso amakhumudwa kwambiri akakumbukira zimene atsogoleri a chipembedzo chawo ankachita. Amaona kuti anali achinyengo kwambiri chifukwa ankamwa mowa mwauchidakwa, ankatchova juga komanso ankaba ndalama za chopereka. Koma likangokwana Lamlungu, atsogoleriwo ankalalikira kuti Mulungu adzawotcha anthu omwe amachita zoipa.
A Jeffery akhala akugwira ntchito kwa nthawi yaitali pa kampani ina yoona za maulendo apanyanja yomwe ili ndi maofesi ake ku United Kingdom ndi ku United States. Ananena kuti anthu a pakampani yawo komanso anthu omwe ankawanyamulira katundu ankakonda kuchita zachinyengo akamakambirana ndi akuluakulu a boma. Nthawi zambiri ankalolera kunena bodza n’cholinga choti awine kontilakiti.
Nkhani ngati zimenezi si zachilendo masiku ano. Anthu akumachita zachinyengo m’boma, m’zipembedzo komanso akamachita bizinezi. Mawu achingelezi amene timawamasulira kuti “wachinyengo” akuchokera ku mawu achigiriki omwe amatanthauza munthu wodziwa kulankhula pagulu kapena wazisudzo amene amakonda kuvala chophimba kumaso kuti anthu asamuzindikire. Patapita nthawi, mawuwa anayamba kugwiritsidwanso ntchito ponena za munthu wachinyengo yemwe amafuna kupusitsa anthu ena n’cholinga choti zinthu zimuyendere.
Chinyengo chimabweretsa mavuto ambiri. Mwachitsanzo anthu amene amachitidwa zachinyengo, amakhala okwiya kwambiri ndipo amafunitsitsa zinthu zitasintha n’kuyamba kuyenda bwino. Nthawi zina anthu amenewa amadzifunsa kuti, “Kodi anthu adzasiya kuchita zachinyengo?” Tiyeni tione zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.
MULUNGU KOMANSO YESU AMADANA NDI CHINYENGO
Baibulo limasonyeza kuti chinyengo sichinayambe lero. Chinayamba kale kwambiri ndipo anayambitsa ndi mngelo wina woipa dzina lake Satana Mdyerekezi. Anthu atangolengedwa kumene, Satana anagwiritsa ntchito njoka popusitsa Hava. Anachita zimenezi kuti Havayo asamutulukire. (Genesis 3:1-5) Kungochokera nthawi imeneyo anthu ambiri amachita zinthu zofanana ndi zimene Mdyerekezi anachitazi. Amachita zimenezi kuti apusitse anthu ena komanso kuti akwaniritse zolinga zawo zadyera.
Nthawi ina m’mbuyomu Mulungu anachenjeza Aisiraeli mobwerezabwereza kuti adzakumana ndi mavuto Yesaya 29:13) Chifukwa choti Aisiraeli sanasinthe, Mulungu analola kuti mitundu ina iwononge mzinda wa Yerusalemu komanso kachisi wawo moti anawonongedwa ndi Ababulo mu 607 B.C.E. komanso ndi Aroma mu 70 C.E. Apatu n’zoonekeratu kuti Mulungu sagwirizana ndi anthu omwe amachita chinyengo.
ngati atapanda kusiya kuchita zachinyengo komanso kumulambira mwachinyengo. Mwachitsanzo anawachenjeza kudzera mwa mneneri Yesaya kuti: “Anthu awa ayandikira kwa ine ndi pakamwa pawo pokha, ndipo andilemekeza ndi milomo yawo yokha koma mtima wawo auika kutali ndi ine.” (Komabe Mulungu ndiponso Mwana wake Yesu amasangalala kwambiri ndi anthu omwe sachita zachinyengo. Mwachitsanzo Yesu ali padziko lapansi, anayamikira munthu wina dzina lake Natanayeli chifukwa choti anali wokhulupirika. Yesu atamuona ananena kuti: “Onani Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe chinyengo.” (Yohane 1:47) Kenako Yesu anasankha Natanayeli, yemwe ankadziwikanso kuti Batolomeyo, kuti akhale mmodzi wa atumwi ake 12.—Luka 6:13-16.
Yesu ankakonda kucheza ndi ophunzira ake ndipo nthawi zambiri ankawaphunzitsa zimene Mulungu amafuna ndiponso ankawachenjeza za kuopsa kwa chinyengo. Ankachita zimenezi chifukwa sankafuna kuti ophunzira akewo atengere zimene atsogoleri achipembedzo ankachita. Atsogoleriwa anali achinyengo kwambiri moti Yesu anawadzudzula chifukwa cha khalidwe loipali. Mwachitsanzo taonani zimene atsogoleri achinyengowo ankachita.
Ankachita zinthu ‘mwachilungamo’ pongofuna kuti anthu awaone. Yesu ananena kuti: “Samalani kuti musamachite chilungamo chanu pamaso pa anthu ndi cholinga chakuti akuoneni . . . muja amachitira onyenga.” Ndiyeno anawauza kuti azipereka mphatso zawo zachifundo ‘mwamseri.’ Anawauzanso kuti azipemphera ali kwaokha, osati n’cholinga choti anthu awaone. Anati ngati atamachita zimenezi adzasonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro chopanda chinyengo komanso Mulungu adzasangalala nawo.—Mateyu 6:1-6.
Ankakonda kupezera anthu ena zifukwa. Yesu anati: “Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtanda wa denga la nyumba uli m’diso lakowo, ndipo ukatero udzatha kuona bwino mmene ungachotsere kachitsotso m’diso la m’bale wako.” (Mateyu 7:5) Mpake kuti Yesu ananena zimenezi chifukwa ngati munthu amangokhalira kupezera ena zifukwa, chonsecho nayenso amalakwitsa zinthu zambirimbiri, amakhala akupusitsa anthu kuti azioneka wabwino kuposa ena. Pajatu ‘tonse ndi ochimwa ndipo ndife operewera pa ulemerero wa Mulungu.’—Aroma 3:23.
Anali ndi zolinga zolakwika. Pa nthawi ina, ophunzira a Afarisi komanso anthu ena a m’chipani cha Herode anafika kwa Yesu n’kumufunsa funso lokhudza msonkho. Anayamba ndi kumuyamikira koma akufuna kuti amutape m’kamwa. Anati: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti inu mumanena zoona ndipo mumaphunzitsa njira ya Mulungu m’choonadi.” Kenako pofuna kumukola anamufunsa funso lakuti: “Kodi n’kololeka kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?” Ndiyeno Yesu anawayankha kuti: “Onyenga inu! Bwanji mukundiyesa?” Mpake kuti Yesu anawanena kuti onyenga chifukwa sikuti ankafuna kudziwadi yankho la funsolo, koma ankangofuna “kuti am’kole m’mawu ake.”—Mateyu 22:15-22.
Akhristu oona amakhala ndi ‘chikondi chochokera mumtima woyera, chikumbumtima chabwino, ndiponso chikhulupiriro chopanda chinyengo.’—1 TIMOTEYO 1:5
Pa nthawi imene mpingo wachikhristu unkayamba pa Pentekosite mu 33 C.E., makhalidwe abwino amene atumwi anali nawo anathandiza kuti anthu ambiri akhale Akhristu komanso kuti asakhale achinyengo. Akhristuwa ankayenera kuyesetsa kuti asakhale ndi mtima wachiphamaso komanso kuti akhale anthu abwino. Mwachitsanzo, Petulo yemwe anali mmodzi wa atumwi 12 a Yesu, analimbikitsa Akhristu kuti ‘azikhala omvera choonadi komanso azikonda abale mopanda chinyengo.’ (1 Petulo 1:22) Nayenso mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti, ‘akhale ndi chikondi chochokera mumtima woyera, chikumbumtima chabwino, ndiponso chikhulupiriro chopanda chinyengo.’—1 Timoteyo 1:5.
MAWU A MULUNGU ANGATHANDIZE MUNTHU KUSIYA CHINYENGO
Zimene Yesu komanso atumwi ankaphunzitsa, n’zothandizanso masiku ano. N’chifukwa chake mtumwi Paulo analemba kuti: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu, ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse. Amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu, komanso mfundo za mafupa ndi mafuta a m’mafupa. Mawu a Mulungu Aheberi 4:12) Choncho Baibulo lingathandize munthu kusiya chinyengo. Ndipotu anthu ena omwe poyamba anali achinyengo, anasintha ataphunzira zimene Baibulo limanena ndipo amayesetsa kuchita zimene anaphunzirazo. Mwachitsanzo, tiyeni tione mmene kuphunzira Baibulo kunathandizira anthu amene tawatchula kumayambiriro aja.
amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.” (A Panayiota anasintha maganizo, wa Mboni za Yehova atawaitana kuti apite ku Nyumba ya Ufumu. Atafika kumeneko anadabwa kuona kuti anthu ake sanali achinyengo. Mayiwa anati: “Nditapita ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova, ndinaona kuti anthu ake anali achikondi komanso ankachita zinthu mondiganizira. Ndinali ndisanaonepo zimenezi pa nthawi yonse yomwe ndinkachita zandale zija.”
A Panayiota anayamba kuphunzira Baibulo ndipo kenako anabatizidwa n’kukhala a Mboni za Yehova. Panopa patha zaka 30 kuchokera nthawi imeneyo. Mayiwa anati: “Panopa ndimakhala moyo wosangalala. Ndimaona kuti ndinkataya nthawi yanga pamene ndinkapita m’makomo a anthu kukawauza kuti athandize chipani chathu. N’zoona kuti panopa ndimapitabe m’makomo a anthu, koma ndimapita kukawauza za Ufumu wa Mulungu womwe udzathetse chinyengo.”
Nawonso a Daniel anaphunzira Baibulo ndipo kenako anakhala a Mboni za Yehova. M’kupita kwa nthawi anapatsidwa udindo mumpingo. Koma kenako anachita zosayenera ndipo zimenezi zinachititsa kuti ayambe kudziimba mlandu kwambiri. A Daniel anati: “Ndinaona kuti ndisakhale ngati atsogoleri achinyengo omwe anali m’chipembedzo changa choyamba chija. Sindinkafuna kuti Akhristu anzanga aziona kuti ndine munthu wabwino, chonsecho ndikuchita zinazake zoipa. Ndinkaona kuti chimenechi chingakhale chinyengo chachikulu. Choncho ndinatula pansi udindo.”
Koma chosangalatsa n’choti patapita nthawi, a Daniel anayesetsa kusintha zochita zawo moti anayambiranso kutumikira pa udindo mumpingo. Panopa ndi osangalala ndipo samadziimbanso mlandu. Anthu omwe akufuna kusangalatsa Mulungu amayesetsa kupewa chinyengo. Amayamba achotsa kaye “mtanda wa denga” womwe uli m’maso mwawo asanachotse “kachitsotso” m’diso la anzawo.
Nawonso a Jeffery, omwe tawatchula kale aja anati: “Nditaphunzira zimene Baibulo limanena, ndinaona kuti sindingapitirizenso kumanena zinthu zabodza n’cholinga chongofuna kuwina kontilakiti. Mwachitsanzo, zinandikhudza kwambiri nditamva zimene lemba la Miyambo 11:1 limanena. Limati: ‘Sikelo yachinyengo imam’nyansa Yehova.’” Panopa a Jeffery anasiya kuchita zachinyengo. Zimenezitu n’zosiyana kwambiri ndi zimene ankachita anthu achinyengo omwe ankafuna kukola Yesu aja.
A Mboni za Yehova padziko lonse amayesetsa kutsatira zimene amaphunzira m’Baibulo pa moyo wawo. Nthawi zonse amayesetsa “kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndipo umatsatira zofunika pa chilungamo chenicheni ndi pa kukhulupirika.” (Aefeso 4:24) Tikukulimbikitsani kuti mufunse a Mboni za Yehova kuti akuuzeni zimene amakhulupirira komanso kuti akuthandizeni kudziwa zambiri za dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. M’dziko limenelo “mudzakhala chilungamo” ndipo simudzapezeka anthu achinyengo.—2 Petulo 3:13.