Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZIMENE OWERENGA AMAFUNSA . . .

Kodi Cholakwika N’chiyani Ndi Miyambo Yomwe Imachitika pa Khirisimasi?

Kodi Cholakwika N’chiyani Ndi Miyambo Yomwe Imachitika pa Khirisimasi?

Kuyambira kale, Akhristu akhala akuchita Khirisimasi ndipo amati ndi chikondwerero chokumbukira kubadwa kwa Yesu. Komabe, miyambo yambiri imene imachitika pa Khirisimasi ndi yosagwirizana ndi kubadwa kwa Yesu. Ndipo zimadabwitsa kuti, n’chifukwa chiyani anthu anaganiza zomachita miyambo imeneyi pa tsiku la Khirisimasi?

Chitsanzo cha zimenezi, ndi nkhani yonena za Father Christmas, yemwe anthu amaganiza kuti amabweretsera ana mphatso pa Khirisimasi. Zithunzi za Father Christmas zinatchuka kwambiri mu 1931 pamene kampani ina yopanga zakumwa inajambula Father Christmas wonenepa atavala zovala zofiira komanso ali ndi ndevu zoyera. Zimenezi zinachititsa kuti malonda a kampaniyi ayende bwino kwambiri. Kenako anthu anayamba kuikonda kwambiri njira yoitanira malonda imeneyi moti m’ma 1950, anthu a ku Brazil nawonso anayamba kujambula Father Christmas akamaitanira malonda awo pa Khirisimasi. Ataona kuti zinthu zayamba kuyenda, anasiya kujambula zithunzi za Grandpa Indian, yemwe anali wotchuka kwambiri kwawoko. Pulofesa wina, dzina lake Carlos E. Fantinati, anati: “Sikuti Father Christmas anangolowa m’malo mwa Grandpa Indian. Koma anakhalanso chizindikiro cha chikondwerero cha Khirisimasi moti anthu anaiwaliratu zomajambula Yesu ali wakhanda, ndipo anayamba kumajambula Father Christmas.” Apatu n’zoonekeratu kuti palibe kugwirizana kulikonse pakati pa kubadwa kwa Yesu ndi Father Christmas. Koma kodi ndi mwambo wokhawu womwe uli wosagwirizana ndi kubadwa kwa Yesu? Kuti tidziwe yankho la funsoli, tiyeni tikambirane zimene zinkachitika m’nthawi ya atumwi.

Buku lina linanena kuti: “Akhristu a m’nthawi ya atumwi sankayerekeza n’komwe kukondwerera masiku a kubadwa. Ndipo palibe paliponse pamene pamasonyeza kuti ankakondwerera kubadwa kwa Yesu.” (Encyclopedia Britannica) Koma kodi n’chifukwa chiyani Akhristu sankakondwerera masiku a kubadwa? N’chifukwa choti ankaona kuti ndi mwambo wachikunja. Ndipotu m’Baibulo palibe pamene panalembedwa deti limene Yesu anabadwa.

Koma m’zaka za m’ma 300 C.E., tchalitchi cha Katolika chinayambitsa chikondwerero cha Khirisimasi. Chinachita zimenezi ngakhale chinkadziwa zoti Akhristu oyambirira sankagwirizana ndi zokondwerera masiku a kubadwa. Pa nthawiyi panali miyambo ina yotchuka kwambiri yomwe Aroma ankachita akamalambira milungu yawo. Wolemba mabuku wina, dzina lake Penne L. Restad, analemba kuti chaka chilichonse kungochokera pa 17 December kufika pa 1 January, “Aroma ankachita mapwando, masewera, ankaguba m’misewu komanso ankachita miyambo yosiyanasiyana akamalemekeza milungu yawo.” (Christmas in America) Ndipo pa 25 December, Aromawa ankakondwerera kubadwa kwa Dzuwa, yemwe anali mulungu wawo wosagonjetseka. Ndiye tchalitchi cha Katolika chinaona kuti kuyambitsa Khirisimasi pa 25 December, kukanakopa Aroma kuti azikondwerera kubadwa kwa Yesu m’malo momakondwerera kubadwa kwa dzuwa. Koma munthu wina, dzina lake Gerry Bowler, ananena kuti Aroma “ankachitabe zikondwerero zawo zija, kungoti ankazichita m’dzina lokondwerera kubadwa kwa Yesu. Ngakhale kuti Akatolika ankaona kuti athandiza anthu kusiya kuchita zikondwerero zachikunja, anaiwala kuti fisi amakhalabe fisi ngakhale atasintha tchire.”

Ndiyetu pamene pagona vuto ndi kumene kunachokera miyambo yomwe imachitika pa Khirisimasi. Wolemba mabuku wina, dzina lake Stephen Nissenbaum, ananena kuti Khirisimasi ndi “chikondwerero chachikunja chomwe chinangosinthidwa mwina ndi mwina kuti chikhale chachikhristu.” (The Battle for Christmas) Choncho, Khirisimasi ndi mwambo womwe umanyozetsa Mulungu komanso Mwana wake, Yesu Khristu. Monga taonera, Khirisimasi inachokera ku miyambo yachikunja. Baibulo limati: “Pali ubale wotani pakati pa chilungamo ndi kusamvera malamulo? Kapena pali kugwirizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima?” (2 Akorinto 6:14) Khirisimasi ili ngati mtengo wokhota womwe ‘sungawongoledwe.’—Mlaliki 1:15.