Mavidiyo a Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso

Pezani luso lowerenga komanso kuphunzitsa pagulu.

PHUNZIRO 1

Mawu Oyamba Abwino

Kodi mungatani kuti anthu achite chidwi ndi zomwe mukufuna kunena?

PHUNZIRO 2

Kulankhula Mokambirana ndi Anthu

Kodi mungatani kuti omvetsera anu azisangalala ndi nkhani yanu?

PHUNZIRO 3

Kugwiritsa Ntchito Mafunso

Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mafunso pothandiza anthu kuti akhale ndi chidwi, aziganizira nkhaniyo komanso kuti amvetse mfundo zofunika zimene tikuwaphunzitsa?

PHUNZIRO 4

Kunena Mawu Oyenera Musanayambe Kuwerenga Lemba

Kodi tingathandize bwanji omvetsera athu kuti apindule kwambiri ndi zimene tikuwerenga m’Baibulo?

PHUNZIRO 5

Kuwerenga Molondola

Kodi ndi zinthu ziti zomwe zingakuthandizeni kuti muziwerenga molondola?

PHUNZIRO 6

Kufotokoza Bwino Malemba

Kodi muyenera kuchita chiyani mukawerenga lemba kuti muthandize omvetsera anu kumvetsa cholinga chimene mwawerengera lembalo?

Kulankhula Zoona Komanso Zofika Pamtima

Kodi mungatani kuti muzilankhula zoona pokamba nkhani?

PHUNZIRO 8

Mafanizo Abwino

Mofanana ndi Yesu, kodi mungatani kuti muzigwiritsa ntchito bwino mafanizo?

PHUNZIRO 9

Kugwiritsa Ntchito Bwino Zinthu Zooneka

Kodi mungagwiritse ntchito bwanji zithunzi komanso zinthu zina zooneka pothandiza omvetsera anu kumvetsa mfundo zazikulu?

PHUNZIRO 10

Kusinthasintha Mawu

Kodi tingatani kuti tizitha kusinthasintha mawu n’cholinga choti mfundo zimene tikufotokoza zizimveka bwino komanso ziziwafika omvetsera athu pamtima?

PHUNZIRO 11

Kulankhula ndi Mtima Wonse

Kodi mungatani kuti muzifotokoza mfundo m’njira yolimbikitsa omvera anu kuchita zinazake?

PHUNZIRO 12

Kulankhula Mwachikondi Komanso Mokoma Mtima

Kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinudi wachikondi komanso wokoma mtima mukamalankhula ndi omvera anu?

PHUNZIRO 15

Kulankhula Motsimikiza

Kodi mungatani kuti muzilankhula motsimikiza mukamakamba nkhani kapena mukakhala mu utumiki?

PHUNZIRO 16

Kulankhula Molimbikitsa

Kodi ndi zinthu zitatu zofunika ziti zomwe zingatithandize kuti tizilankhula mfundo zomwe zingalimbikitse anthu ena?

PHUNZIRO 17

Kulankhula Zomveka

Kodi muyenera kupewa zinthu ziti mukamayesetsa kuthandiza anthu kuti amvetse tanthauzo la zimene mukunena?

PHUNZIRO 18

Nkhani Yophunzitsadi Anthu

Kodi mungaphunzitse bwanji anthu kuti muziwathandiza kuganiza komanso kuphunzira mfundo zothandiza?

PHUNZIRO 19

Kuwafika Pamtima Anthu

Kodi mungathandize bwanji anthu kukhala ndi zolinga zabwino?

PHUNZIRO 20

Mawu Omaliza Abwino

Kodi mungatani kuti mawu anu omaliza akhale abwino, kaya mukukamba nkhani kapena mukulalikira?

Mwina Mungakondenso Kudziwa Izi

MABUKU

Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso

Kabukuka kakonzedwa kuti kakuthandizeni kukhala ndi luso lowerenga pagulu, lolankhula komanso lophunzitsa.