Nehemiya: “Chimwemwe Chimene Yehova Amapereka Ndicho Malo Anu Achitetezo”—Mbali Yachiwiri
Ntchito yomanganso mpanda wa Yerusalemu yatha, koma Nehemiya akukumananso ndi vuto lina. N’kupita kwa nthawi, anthu ambiri akufunika kuthandizidwa kuti ayambirenso kulambira Yehova m’njira yoyenera. Tsopano Nehemiya mothandizidwa ndi Ezara komanso Malaki, akuyamba ntchito yobwezeretsa kulambira koona.