Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KALE LATHU

Ankakondabe Yehova pa Nthawi Zovuta

Ankakondabe Yehova pa Nthawi Zovuta

 Nkhondo Yachiwiri Yapadziko Lonse itangotha, mayiko ambiri a ku Europe anawonongeka kwambiri. Komabe, a Mboni za Yehova ndi anthu ena anatulutsidwa kumakampu omwe chipani cha Nazi chinkazunzirako anthu. Ngakhale zinali choncho, moyo unali wovuta kwambiri. Anthu a Yehova nawonso ankasowa chakudya, zovala, nyumba ndi zinthu zina zofunika. Mlongo Karin Hartung, ananena kuti, “Chifukwa cha vuto losowa nyumba, aliyense ankafunika kukhala ndi achibale ake kapenanso kuchititsa lendi zipinda zina za nyumba yawo.” Kwa nthawi yaitali ndithu, Mlongo Gertrud Poetzinger, yemwe anali kundende zozunzirako anthu kwa zaka 7 ndi miyezi 6, ankakhala m’kanyumba kosungiramo zipangizo ndipo ankagona pampando. a

 Kodi gulu la Yehova linachita zotani pofuna kuthandiza abale ndi alongo omwe ankakhala m’madera omwe anali atawonongedwa chifukwa cha nkhondo? Nanga ifeyo tingaphunzire chiyani kwa abale amene anakumana ndi mavuto pa nthawi ya nkhondoyi komanso itatha?

Kuthandiza Abale Ndi Zinthu Zofunika pa Moyo

 Gulu la Yehova linachita zinthu mwachangu pothandiza anthu a Mulungu ku Europe. M’bale Nathan Knorr ndi M’bale Milton Henschel a ku likulu la dziko lonse la Mboni za Yehova anapita ku Europe kuti akaone zomwe abale akufunikira. Mu November ndi December 1945, iwo anayendera mayiko a England, Switzerland, France, Belgium, Netherlands, Denmark, Sweden, Finland ndi Norway. M’bale Knorr ananena kuti, “Aka n’koyamba kuti tione mmene dziko limawonongekera chifukwa cha nkhondo.”

M’bale Nathan Knorr akukamba nkhani pamsonkhano wa Mboni za Yehova ku Helsinki, Finland, pa 21 December 1945

 Pa nthawiyi, M’bale Knorr sanapatsidwe chilolezo choti alowe m’dziko la Germany. Komabe, Erich Frost amene ankayang’anira ofesi ya nthambi ku Germany, anakwanitsa kukakumana ndi M’bale Knorr. b M’bale Erich ananena kuti, “M’bale Knorr anatipatsa malangizo othandiza komanso anatilonjeza kuti akatitumizira zinthu zofunikira monga chakudya ndi zovala. Posakhalitsa, tinalandira zakudya zochuluka monga ufa wa mitundu yosiyanasiyana, mafuta ndi zakudya zina. Abale a m’mayiko ena anatumizanso mabokosi akuluakulu a zovala zosiyanasiyana komanso nsapato.” Abale ndi alongo anasangalala kwambiri kulandira katundu ameneyu ndipo analira chifukwa cha chisangalalo. Malinga ndi lipotili, “aka sikanali komaliza kutumiza chithandizochi. Anapitiriza kutumiza zinthuzi kwa zaka ziwiri ndi hafu!” c

A Mboni a ku United States akulongedza zovala zimene anthu apereke kuti zitumizidwe ku Europe

Sanasiye Kutumikira Yehova

 Pang’ono ndi pang’ono, zinthu zinayamba kuyenda bwino ndipo abale ankakhala bwino koma sanasiye kutumikira Yehova. Kodi n’chiyani chinawathandiza?

Jürgen Rundel (kutsogolo chakumanzere) mu 1954 ali ndi abale amumpingo wa Spittal an der Drau ku Austria

 Nthawi zonse ankachita zinthu monga kuwerenga Baibulo, kupita kumisonkhano komanso kugwira ntchito yolalikira. (Aefeso 5:15, 16) Pa nthawi ya nkhondo, zinali zovuta kuti abale azipeza mabuku ofotokoza Baibulo komanso kuti nthawi zonse azichita zinthu zokhudza kulambira. Komabe nkhondo itatha, anayambiranso kusonkhana momasuka komanso kugwira ntchito yolalikira. Jürgen Rundel yemwe amakhala ku Austria, anati: “Kuwerenga buku la Informant d komanso kulimbikitsidwa ndi oyang’anira oyendayenda kunatithandiza kwambiri kuti tipitirize kukonda Yehova. Tinkaganizira kwambiri za Yehova, Yesu, kuphunzira Baibulo komanso kugwira ntchito yolalikira. Kunalibe zinthu zotisokoneza monga ma TV.”

 Mlongo Ulrike Krolop anafotokoza kuti: “Ndikukumbukira kuti ndinasangalala kwambiri nditafufuza mozama nkhani ina ya m’Baibulo. Mwamuna wanga ankasonyeza chitsanzo chabwino pa nkhaniyi. Tikangolandira magazini atsopano a Nsanja ya Olonda, ankasiya chilichonse chomwe ankachita pa nthawiyo n’kuyamba kuwerenga.” Karin yemwe watchulidwa kumayambiriro uja, anati: “Pa nthawi ya nkhondo, tinaona chuma chathu chakuthupi chikutha mwachangu kwambiri. Koma sitinasiye kulandira mabuku ofotokoza Baibulo omwe ankatithandiza kukhalabe olimba mwauzimu, ngakhale kuti ankapezeka ochepa. Yehova anadalitsa atumiki ake okhulupirika.”

Ulrike Krolop

 Anayambiranso kulalikira. (Mateyu 28:19, 20) Nkhondo inachititsa kuti atumiki a Yehova azigwira movutikira ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa. M’bale wina dzina lake Friedhelm akukumbukira kuti nkhondo itangotha, “aliyense anayambiranso kulalikira.” Mlongo Ulrike ananena kuti: “Munthu wa Mboni woyamba kudzalalikira banja la mwamuna wanga anali akuvalabe yunifolomu yomwe ankavala kundende. Zikuonekeratu kuti anayamba kulalikira nkhondo itangotha.” Jürgen anati, “Nkhondo itangotha, aliyense anali ndi mtima wofunitsitsa kugwira ntchito yolalikira. Abale ndi alongo ambiri anayamba utumiki wanthawi zonse.”

 Mlongo Ulrike ananena kuti: “Zinali zovuta kukhala m’mizinda yomwe munaphulitsidwa mabomba pa nthawi ya nkhondo. Anthu ambiri ankakhala m’nyumba zoti mbali ina zinaphulitsidwa ndi mabomba. Ndiyeno kodi a Mboni anatani kuti azipeza anthuwo n’kumawalalikira? Mlongo Ulrike yemwe banja lawo linaphunzira Baibulo pa nthawi ya nkhondo akufotokoza zomwe zinkachitika, kuti: “Tinkasakasaka komwe kukuoneka kuwala kwa nyale kapena komwe kukuoneka utsi.”

 Ankalimbikitsana. (1 Atesalonika 5:11) A Mboni za Yehova ambiri ankachitiridwa nkhanza pa nthawi ya nkhondo. Komabe nkhondo itatha, iwo sankangoganizira mavuto omwe ankakumana nawo, koma ankalimbikitsana. Iwo ankasangalala kwambiri kuti chikhulupiriro chawo chinayesedwa. (Yakobo 1:2, 3) M’bale Johannes wa ku United States, ananena kuti: “Woyang’anira dera wathu yemwe anakhalako kundende ankatifotokozera nkhani zolimbikitsa zambiri zosonyeza mmene Yehova ankathandizira abale ndi alongo. Zimenezi zinalimbitsa kwambiri chikhulupiriro chathu.”

 M’bale Johannes anafotokoza kuti nkhondo itatha, abale anapitiriza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova chifukwa ankakumbukira “mmene ankawathandizira kundende komanso mmene ankayankhira mapemphero awo.” Tsopano a Mboniwa anali ndi ufulu wochita zinthu zonse zokhudza kulambira monga kuwerenga Baibulo tsiku lililonse, kusonkhana komanso kugwira ntchito yolalikira. Elisabeth, yemwe anapezeka nawo pamsonkhano wa ku Nuremberg mu 1946 ananena kuti, a Mboni omwe anatulutsidwa m’ndendewo “anali akuonekabe owonda komanso ofooka. Komabe, anali ‘oyaka ndi mzimu’ pa nthawi imene ankatifotokozera zomwe zinawachitikira.”​—Aroma 12:11.

Karin Hartung

 Sanasiye kugwirizana ndi Akhristu anzawo. (Aroma 1:11, 12) Pa nthawi ya nkhondo, a Mboni sankatha kuchitira zinthu limodzi ndi Akhristu anzawo chifukwa ankazunzidwa kwambiri. Karin ananena kuti, “Sankayenderana pafupipafupi chifukwa sankafuna kuti akuluakulu a boma awazindikire n’kuika pangozi moyo wa Akhristu anzawo.” Koma nkhondo itangotha zonsezi zinathanso. M’bale Friedhelm ananena kuti: “Abale ankachitira zinthu zonse limodzi. Ankaona kuti kusonkhana komanso kugwira ntchito yolalikira ndi kofunika kwambiri pa moyo wawo.”

 Mkulu wina wa ku Germany dzina lake Dietrich, anati: “Nkhondoyi itatha ndi a Mboni ochepa okha amene anali ndi magalimoto. Choncho popita kumisonkhano tinkayenda wapansi koma tinkakhala m’magulu. Kuchita zimenezi kunkatithandiza kuti tizilimbikitsana komanso kugwirizana kwambiri. Tinkangokhala ngati anthu a m’banja limodzi.”

Zimene Tikuphunzirapo

 Masiku ano, atumiki a Yehova ambiri akupirira mavuto osiyanasiyana obwera chifukwa cha ngozi zam’chilengedwe, matenda, nkhondo, kuzunzidwa komanso kukwera mitengo kwa zinthu. (2 Timoteyo 3:1) Ngakhale zili choncho, sitikufunikira kumada nkhawa kwambiri. N’chifukwa chiyani tikutero? Chitsanzo chabwino cha abale ndi alongo athu a ku Germany pa nthawi ya ulamuliro wa Nazi, chikutitsimikizira kuti Mulungu wathu adzapitiriza kutithandiza m’masiku otsiriza ovutawa. Choncho, tiyeni tikhale ngati mtumwi Paulo yemwe analemba kuti: “Tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?’”​—Aheberi 13:6.

a Werengani mbiri ya moyo wa Mlongo Poetzinger m’Chingelezi pa mutu wakuti, “Putting the Kingdom First in Postwar Germany.

b Werengani mbiri ya moyo wa M’bale Frost m’Chingelezi pa mutu wakuti, “Deliverance From Totalitarian Inquisition Through Faith in God.

c Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene ntchito yopereka chithandizo inkayendera pambuyo pa Nkhondo Yachiwiri Yapadziko Lonse, werengani nkhani yakuti “Anapereka Zinthu Zawo Zabwino Kwambiri,” komanso mabokosi pamasamba 211, 218 ndi 219 m’buku lakuti Ufumu wa Mulungu Ukulamulira.

d Panopa mipingo imagwiritsa ntchito Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu​—Kabuku ka Msonkhano.