Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Wailesi ya WBBR mu 1924

KALE LATHU

Kuulutsa Mawu a Uthenga Wabwino

Kuulutsa Mawu a Uthenga Wabwino

 Lamlungu madzulo pa 24 February 1924, wailesi yatsopano ya Ophunzira Baibulo a yotchedwa WBBR, inayamba kuulutsa mawu kwa nthawi yoyamba. Kodi zinayenda bwanji? Ndi anthu ati omwe anaimvetsera? Kodi a Mboni za Yehova akupitiriza bwanji kugwiritsa ntchito zipangizo zamakono pokwaniritsa ulosi wakuti “uthenga wabwino . . . wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi”?—Mateyu 24:14.

M’bale ali pamakina oulutsira mawu pa wailesi ya WBBR

“Tinayambapo Kuulutsa Mawu”

 Pulogalamu yoyambirira kuulutsidwa inayamba nthawi ya 8:30 madzulo. Tinkachitira musitudiyo yongomangidwa kumene, pachilumba china chotchedwa Staten Island ku New York. M’bale Ralph Leffler ndi yemwe anali injiniya wotsogolera zonse ndipo ananena kuti “aliyense musitudiyomo mtima unali dyokodyoko. Tinkadzifunsa kuti, ‘Koma zithekadi kuti anthu amve mawu athu pawailesiyi?’ Kenako ndinayatsa zipangizo zathu ndipo tinayambapo kuulutsa mawu tili ndi chikhulupiro choti zonse ziyenda bwino ndithu.”

 Amene ankalengeza mawu pawailesiyi anali mkulu woyang’anira wailesiyi M’bale Victor Schmidt. Iye anayamba pulogalamuyi potchula akatswiri oimba omwenso anali Ophunzira Baibulo. Choyamba m’bale ankaimba nyimbo pogwiritsa ntchito piyano. Kenako Cora Wellman, anaimba nyimbo yakuti “The Ninety and Nine,” yochokera mufanizo la Yesu la nkhosa yosochera. (Luka 15:4-7) Abale enanso anaimba nyimbo, monga Frederick W. Franz yemwe anaimba yamutu wakuti “The Penitent,” yofotokoza nkhani ya mwana wolowerera.—Luka 15:11-25.

Pulogalamu ya mwambo wotsegulira siteshoni ya WBBR

 Joseph F. Rutherford, yemwe pa nthawiyo ankatsogolera Ophunzira Baibulo anakamba nkhani yotsegulira wailesiyi “popititsa patsogolo ntchito za ufumu wa Mesiya.” Iye anati: “Ambuye walola kuti wailesiyi ikhalepo pa nthawi ino, ndipo sitikukayikira kuti akusangalala kwambiri kuona kuti ikugwiritsidwa ntchito pophunzitsa anthu zokhudza kukwaniritsidwa kwa maulosi ake ofunika.”

“Palibe Mawu Amene Tinawaphonya”

 Anthu ambiri akumpoto chakum’mawa kwa dziko la United States anamva uthenga womwe unaulutsidwa koyamba pawailesiyi. Munthu wina yemwe ankamvetsera wailesiyi pamtunda wa makilomita oposa 320 ku Morrisville, Vermont, anati: “Ndasangalala kukudziwitsani kuti . . . mawu onse amene M’bale Rutherford ananena ankamveka bwino. Palibe mawu amene tinawaphonya.” Ngakhale anthu a ku Monticello ku Florida, nawonso anakwanitsa kumvetsera wailesiyi. Anthu ambiri anasangalala atamvetsera wailesi yatsopanoyi ndipo anatumiza makalata oyamikira.

Joseph Rutherford ali pa maikolofoni musitudiyo ya WBBR. Victor Schmidt akuulutsa mawu

 Wailesiyi inapitiriza kufalitsa uthenga wa Ufumu kwa zaka 33, b makamaka kwa anthu akumpoto chakum’mawa kwa dziko la United States. Koma nthawi zina, wailesi ya WBBR, inkalumikizidwa ku manetiweki a mawailesi ena ndipo inkaulutsidwa m’dziko la United States, Canada ndi mayiko ena. Buku la Pachaka la Mboni za Yehova la 1975, linanena kuti: “Pofika mu 1933, wailesiyi inkagwiritsa ntchito mawailesi ena 408 kuulutsa uthenga m’zigawo 6 za padziko lapansi ndipo nkhani zofotokoza Baibulo zokwana 23,783 zinkaulutsidwa . . . M’masiku amenewo, munthu akamamvetsera wailesi, ankatha kumva nkhani zoulutsidwa ndi a Watch Tower zikuwulutsidwanso m’masiteshoni a mawailesi osiyanasiyana pa nthawi imodzi. Nthawi zambiri nkhani zimene anthu ankamvetsera pawailesi zinali zokhudza mawu a Mulungu.”

Ulaliki wa Pawailesi Unalowedwa M’malo ndi wa Nyumba ndi Nyumba

 Pamene wailesi ya WBBR inayamba kugwiritsidwa ntchito, ku United States kunali ofalitsa Ufumu okwana 1,064. Uthenga umene unkafalitsidwa pa wailesiyi unathandiza kuti ofalitsa ochepawa afikire anthu ambiri ndi uthenga wabwino. Komabe pofika mu 1957, ku United States avereji ya ofalitsa inali 187,762 ndipo padziko lonse inali 653,273. Chosangalatsa kwambiri n’choti zimene abale ndi alongo ankaphunzira pamisonkhano yampingo zinawathandiza kuti akulitse luso lawo lolalikira kunyumba ndi nyumba komanso mbali zina za utumiki.

 Kusintha kumeneku kunachititsa kuti abale audindo aganizirenso mosamala ubwino wa woulutsa mawu kudzera pawailesiyi poyerekezera ndi kulalikira kunyumba ndi nyumba. Ndiye anatani? Anasankha kugulitsa wailesi ya WBBR yomwe inali wailesi yokhayo ya bungwe Watchtower Society komanso yoyendetsedwa ndi bungweli. Kenako inagulitsidwa pa 15 April 1957. Kutangotsala tsiku limodzi kuti igulitsidwe, M’bale Nathan H. Knorr anaulutsa mawu komaliza. Iye anafunsidwa chifukwa chake ankaigulitsa. Iye anafotokoza kuti a Mboni za Yehova ankachuluka kwambiri chifukwa cha ulaliki wa kunyumba ndi nyumba. Iye anati: “Anthu ambiri aphunzira Baibulo kudzera pawailesiyi. Komabe, chiwerengero cha a Mboni za Yehova m’madera omwe anthu samvetsera WBBR chakwera kwambiri kuposa m’madera omwe amamvetsera wailesiyi.” Choncho abalewa anaona kuti kulalikira kunyumba ndi nyumba kukuthandiza anthu kumva uthenga wabwino poyerekezera ndi wailesi. Koma sikuti aka kanali komaliza kuulutsa mawu. Tinayambiranso kuulutsa mawu, koma mwa njira ina.

Kuulutsa Mawu Masiku Ano

 Pa 6 October 2014, gulu la Yehova linayamba kuulutsa mawu pogwiritsa ntchito TV ya pa intaneti yotchedwa JW Broadcasting. A Mboni za Yehova komanso anthu ena amakonda kuonera pulogalamu ya mwezi ndi mwezi imeneyi pogwiritsa ntchito intaneti, JW Library, zipangizo zoonera zinthu pa intaneti kapena kudzera pa setilaiti. c Ngakhale zili choncho, anthu a Yehova m’madera ena padziko lonse amagwiritsabe ntchito wailesi ndi TV pa ntchito yolalikira. Kodi amachita bwanji zimenezi?

Pulogalamu yoyamba ya JW Broadcasting, mu October 2014

 M’zaka zaposachedwapa, gulu la Yehova lagwiritsa ntchito wailesi ndi TV a anthu ena poulutsa misonkhano ya mlungu uliwonse komanso misonkhano ikuluikulu m’madera amene mulibe intaneti. Uthengawu wafikira anthu ambiri omwe si Mboni, kuphatikizapo omwe ali ndi chidwi chofuna kuphunzira Baibulo. Mwachitsanzo, kuyambira 2021 ndi 2022, akuluakulu oyang’anira mawailesi anauza ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya East Africa kuti anthu ambiri a zipembedzo zina anayamikira misonkhano yathu. Anthu ambiri omwe amamvera wailesi ku Kenya, South Sudan ndi Tanzania anapempha kuti aziphunzira Baibulo.

 Komabe, njira yaikulu imene a Mboni za Yehova amagwiritsa ntchito polalikira uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse ndi kunyumba ndi nyumba, mashelefu amateyala komanso webusaiti ya jw.org. Webusaiti yathu imathandiza anthu achidwi kuti aziwerenga Baibulo ndi mabuku ena ofotokoza Baibulo m’zinenero zoposa 1,080 popanda kulipira chilichonse. Anthu angathenso kupeza mayankho a mafunso okhudza Baibulo komanso kufufuza komwe timachitira misonkhano yathu. Chifukwa chogwiritsa ntchito njira zimenezi, a Mboni za Yehova akwanitsa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu kwa anthu ambiri padziko lonse kuposa kale lonse! Zoonadi, uthengawu ‘ukulalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.’​—Mateyu 24:14.

a Mu 1931, Ophunzira Baibulo anayamba kugwiritsa ntchito dzina lakuti Mboni za Yehova

b Kwa kanthawi, a Mboni za Yehova akhala ali ndi wailesi m’mayiko ena kuphatikizapo ku Australia ndi Canada.