Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KALE LATHU

Anthu Akuphunzitsidwa Kulemba Ndi Kuwerenga Padziko Lonse

Anthu Akuphunzitsidwa Kulemba Ndi Kuwerenga Padziko Lonse

 A Agostinho omwe amakhala ku Brazil anati: “Ndinakulira pafamu inayake ndipo banja lathu linali losauka kwambiri. Chifukwa cha zimenezi ndinasiya sukulu kuti ndipeze ntchito n’cholinga choti ndizithandiza banja lathu.” A Agostinho anaphunzira kuwerenga ndi kulemba atakwanitsa zaka 33. Iwo anati: “Kuphunzira kuwerenga ndi kulemba kwandithandiza kuti ndisiye kudzikayikira.”

 Kwa zaka zoposa 70, a Mboni za Yehova akhala akuphunzitsa anthu ambirimbiri kudziwa kuwerenga ndi kulemba ndipo a Agostinho ndi mmodzi mwa anthu amenewa. N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amathandiza anthu kuwerenga ndi kulemba? Kodi anthu amenewa amapindula bwanji ndi maphunzirowa?

Kuphunzira Zinthu Kumavuta Ngati Munthu Sadziwa Kuwerenga ndi Kulemba

 Pofika mu 1935, a Mboni za Yehova anali atagwira ntchito yolalikira m’mayiko ndi m’madera 115. Pofuna kulalikira kwa anthu olankhula zinenero zosiyanasiyana amishonale ankagwiritsa ntchito nkhani za m’Baibulo zochita kujambulidwa pophunzitsa anthu ndipo nthawi zina ankagawira mabuku ndi magazini azinenero za anthuwo. Ngakhale kuti anthu ambiri anali ndi chidwi chofuna kuphunzira Baibulo, zinali zovuta kuti aphunzire zambiri chifukwa chakuti sankatha kuwerenga ndi kulemba.

 Anthu ankavutika kutsatira mfundo za m’Baibulo chifukwa chakuti paokha sankatha kuwerenga Baibulo. (Yoswa 1:8; Salimo 1:2, 3) Ankavutikanso kukwaniritsa maudindo awo monga Akhristu. Mwachitsanzo, ngati makolo satha kuwerenga ankafunika kuchita khama kwambiri kuti aziphunzitsa ana awo mfundo za m’Baibulo. (Deuteronomo 6:6, 7) Komanso a Mboni omwe sankatha kuwerenga, ankavutika kugwiritsa ntchito Baibulo mwaluso pophunzitsa ena.

Kuyamba Ntchito Yophunzitsa Kuwerenga ndi Kulemba

 Kuyambira m’chaka cha 1940 mpaka 1950, Nathan H. Knorr ndi Milton G. Henschel, omwe anali m’gulu la abale amene ankatsogolera zinthu m’gulu la Mboni za Yehova, anayenda m’mayiko osiyanasiyana n’cholinga choti akathandize kukonza dongosolo logwirira ntchito yolalikira. M’madera amene ankapeza kuti anthu ambiri satha kuwerenga ndi kulemba, abalewa ankalimbikitsa maofesi a nthambi kuti akhazikitse makalasi ophunzitsa kuwerenga ndi kulemba m’mipingo.

Buku lothandiza anthu kuwerenga linatulutsidwa m’Chinyanja pamsonkhano wadera womwe unachitikira ku Chingola, ku Zambia, mu 1954

 Maofesi a nthambi ankatumiza m’mipingo malangizo okhudza mmene sukuluyi izichitikira. M’mayiko ena, maboma anali kale ndi mabuku ophunzitsa anthu kuwerenga ndi kulemba. Mwachitsanzo, ku Brazil a ku ofesi ya nthambi analandira mabuku ndi zinthu zina kuchokera kuboma ndipo anazitumiza kumipingo. Pomwe m’mayiko ena, a Mboni ankafunika kupanga okha zinthu zothandiza pophunzira.

 Kenako makalasiwa anayambika ndipo anthu akuluakulu ndi ana omwe anali ndi mwayi wolowa nawo makalasiwa. Cholinga chake chinali choti anthu azitha kuwerenga m’zilankhulo zawo. Ndipo nthawi zina, mumpingo umodzi anthu ankalankhula zinenero zosiyanasiyana.

Maphunziro Amene Amathandiza Anthu

 Kodi maphunzirowa athandiza bwanji anthu? Wa Mboni wina wa ku Mexico anati: “Panopa ndikutha kumvetsa bwinobwino zimene ndimaphunzira m’Baibulo ndipo zikumandifika pamtima. Kudziwa kuwerenga kwandithandiza kuti ndizicheza momasuka ndi anzanga. Komanso ndikutha kuuza anthu ambiri uthenga wa m’Baibulo.”

 Kuphunzira kuwerenga ndi kulemba kwathandiza anthu m’njira zinanso zambiri. A Isaac a ku Burundi akuti: “Kudziwa kuwerenga ndi kulemba kwandithandiza kuti ndiphunzire ntchito yomanga. Ntchito yomanga ndayamba kuikonda kwambiri ndipo panopa ndimayang’anira mapulojekiti akuluakulu a zomangamanga.”

Akuphunzitsa anthu Chichewa m’Nyumba ya Ufumu ku Lilongwe, ku Malawi, mu 2014

 A Jesusa a ku Peru anayamba kuphunzira kuwerenga ndi kulemba ali ndi zaka 49. Iwo akuti: “Monga mayi wapakhomo, ndikamapita kumsika ndimafunika kudziwa mitengo ndi mayina a zinthu zimene ndikufuna kugula. Poyamba zimenezi zinali zovuta kwambiri. Koma chifukwa chakuti ndinaphunzira kuwerenga ndi kulemba, panopa ndikamapita kumsika sindimadera nkhawa. Ndimatha kukagula zinthu bwinobwino.”

 Kwa zaka zambiri, akuluakulu a boma m’mayiko osiyanasiyana akhala akuthokoza a Mboni za Yehova chifukwa cha ntchito yophunzitsa anthu kuwerenga ndi kulemba. A Mboni za Yehova akhala akupitiriza kuphunzitsa anthu kuwerenga ndi kulemba ndipo akugwiritsa ntchito mabuku ndi zinthu zimene akhala akuzikonza kwa nthawi yaitali. Iwo apanganso ndi kusindikiza timabuku pafupifupi 224 miliyoni m’zilankhulo 720 n’cholinga chofuna kuthandiza anthu kudziwa kulemba ndi kuwerenga. a

a Mwachitsanzo, kabuku kakuti Dziperekeni pa Kuwerenga ndi Kulemba kakupezeka m’zinenero 123. Ndipo kabuku ka Mverani Mulungu kakupezeka m’zinenero 610.