Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Anateteza Ufulu wa Kulambira wa Anthu Akumidzi

Anateteza Ufulu wa Kulambira wa Anthu Akumidzi

MAY 1, 2021

 Ku Latin America, kuli anthu mamiliyoni ambiri komanso zilankhulo ndi zikhalidwe zambirimbiri. Kulinso abale ndi alongo athu ambiri omwe amakonda zikhalidwe zawo. Pofuna kuthandiza anthu kuti adziwe Mulungu, iwo amamasulira komanso kufalitsa mabuku a Mboni za Yehova m’zilankhulo za anthu akumidzi ya ku Latin America zoposa 130. * Koma ena amatsutsidwa chifukwa chosankha kutumikira Yehova komanso kukana kuchita nawo miyambo ina ya kumudzi kwawo yomwe ndi yosagwirizana ndi Malemba. Kodi zopereka zanu zagwiritsidwa ntchito bwanji pothandiza abale ndi alongowa?

Anawathandiza Kubwerera Kwawo

 Ku Mexico, abale ndi alongo am’mudzi wa anthu amtundu wa Huichol kumapiri am’dera la Jalisco anakana mwaulemu kuchita zinthu zachipembedzo zomwe anaona kuti n’zosemphana ndi Malemba. * Koma ena am’mudziwo anakwiya ndipo pa 4 December 2017, gulu la anthu achiwawa linaukira a Mboni limodzi ndi anthu ena amene anali nawo. Gululi linathamangitsa a Mboniwo, kuwononga zinthu zawo komanso kuwaopseza kuti awapha akabwerera kumudziwo.

 A Mboni am’matauni apafupi anasamalira abale ndi alongowa. Koma kodi zikanatheka bwanji kuti abwerere kwawo? M’bale wina dzina lake Agustín anati: “Tinalibe ndalama zokwanira kuti tipeze loya ndipo sitinkadziwa amene angatithandize pankhaniyi.”

 Koma popeza ufulu wa abalewa wolambira Mulungu unaphwanyidwa, abale a ku nthambi ya ku Central America anawathandiza mwamsanga. Poyamba, anapempha akuluakulu a boma kuti afufuze zimene zinachitika. Kenako Komiti ya Ogwirizanitsa ya Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova inavomereza kuti abale a ku nthambiyi agwire ntchito ndi a mu Dipatimenti ya Zamalamulo ku likulu la dziko lonse posumira kukhoti anthu amene anachitira nkhanza abale ndi alongo amtundu wa Huichol amenewa. Mlanduwu unafika mpaka kukhoti lalikulu kwambiri la ku Mexico.

 Maloya ochokera m’mayiko osiyanasiyana anakonzekera mfundo zoti akanene kukhoti. Ndiye kukhotiko anafotokoza kuti mofanana ndi mmene anthu ena ayenera kulemekezera chikhalidwe cha anthu amitundu ina, anthu amtundu umodzi ayeneranso kulemekezana komanso kuteteza ufulu wa aliyense wamtundu umenewu. Aliyense ayenera kukhala ndi ufulu wake kulikonse kumene amakhala.

 Pa 8 July 2020, oweruza onse am’khoti lalikululi anagwirizana pogamula mokomera a Mboni za Yehova. Anagamula kuti onse amene anathamangitsidwa kwawowo aloledwe kuti abwerere kumudzi kwawo. M’bale Agustín, yemwe tamutchula kale uja, anafotokoza mmene iye ndi abale ndi alongo ena akumvera. Iye ananena kuti: “Tikusangalala komanso kuthokoza kwambiri zimene abale atichitira. Ngati akanapanda kutithandiza, palibe zimene tikanachita.”

“Kuchita Zambiri Pongofuna Kuthandiza Anthu Ochepa”

 Nakonso kumudzi wa San Juan de Ilumán, umene uli m’dziko la Ecuador, abale athu anakumananso ndi mavuto ofanana ndi amenewa. Kumudzi umenewu kumakhalanso anthu ambiri amtundu winawake omwe amakhala m’chigwa cha Otavalo. Abalewa anapeza chilolezo kuti amange Nyumba ya Ufumu ndipo anayamba kuimanga mu 2014. Koma wansembe wina anatsogolera anthu oposa 100 ndipo anakakamiza abale kuti asiye kumanga. Kenako anthu amumudziwo analamula kuti a Mboni za Yehova asiye kusonkhana kuti alambire Mulungu.

 Abale am’madipatiment azamalamulo kunthambi ya ku Ecuador komanso kulikulu anagwira ntchito limodzi kuti ateteze ufulu wa kulambira wa abale ndi alongo amumpingowu. Abalewa anakasuma mlanduwu kukhoti. Izi zinachititsa kuti anthu am’mudziwo asiye kutsutsa abalewa n’kuwalola kuti ayambenso kusonkhana komanso kumanga Nyumba ya Ufumu. Koma pofuna kuteteza ufulu wa abale athu m’tsogolo, maloya athu anapempha makhoti aakulu kuti agamule pa nkhani yakuti: Kodi anthu akumidzi ayenera kutsatira malamulo apadziko lonse okhudza ufulu wa anthu?

 Pa 16 July 2020, Khoti loona za malamulo ku Ecuador, lomwe ndi lalikulu kwambiri m’dzikoli, linamvetsera mlanduwu. Abale amene ndi maloya ku Ecuador anaimira mpingowo. Komanso abale 4 amene ndi maloya akumayiko ena analankhulanso kukhoti. Chifukwa cha mliri wa COVID-19, iwo analankhula kuchokera kumayiko ena pavidiyokomfelensi. Aka n’koyamba kuti khoti lilole kuti maloya oimira a Mboni za Yehova padziko lonse alankhule kukhoti pogwiritsa ntchito njira imeneyi. * Maloyawa anagwira mawu a akuluakulu azamalamulo am’mayiko ena kuti apereke umboni wosonyeza kuti anthu sayenera kulandidwa ufulu wawo chifukwa choti amakhala kumudzi kwawo.

Maloya ochokera kumayiko ena anateteza ufulu wa abale athu pavidiyokomfelensi

 Abale akuchigwa cha Otavalowo akuyembekezera mwachidwi chigamulo cha khotili. Iwo akuthokoza kwambiri chifukwa chowathandiza mwanjira imeneyi. Mkulu wina wamumpingo wa Chikichuwa cha Ilumán, dzina lake César, anati: “Ndi Yehova yekha, kudzera m’gulu lake, yemwe angalolere kuchita zambiri pongofuna kuthandiza anthu ochepa.”

 Maloya onse amene akuimira Mboni za Yehova nawonso ndi a Mboni ndipo akusangalala kuthandiza popanda kulipiridwa. Komabe kusuma pa milanduyi, kuikonzekera komanso kupita kukhoti kumafuna nthawi komanso ndalama zambiri. Maloya athu komanso abale ena anagwiritsa ntchito maola oposa 380 pokonzekera zokanena kukhoti komanso maola 240 pomasulira zinthu m’chilankhulo china kuti zikagwiritsidwe ntchito m’khoti la ku Mexico. Maloya pafupifupi 40 apadziko lonse anatha maola ambirimbiri pokonzekera mlandu wa ku Ecuador. Kodi tinapeza bwanji ndalama zimene tinagwiritsa ntchito poteteza ufulu wa abale athuwa? Zimenezi ndi ndalama zimene munapereka pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zimene zafotokozedwa pa donate.pr418.com. Tikukuthokozani kwambiri chifukwa cha mtima wanu wopatsa.

^ A Mboni za Yehova amamasuliranso mabuku athu m’zilankhulo zina zambiri za ku Latin America, kuphatikizapo zinenero zamanja za kumeneko.

^ Anthu amtundu wa Huichol amadziwikanso kuti amtundu wa Wixáritari ndipo chilankhulo chawo nthawi zambiri chimadziwika kuti Chiwisheka.

^ Ngakhale kuti gulu lathu lapadziko lonse silinakhudzidwe ndi mlanduwu, oweruza analola abale athu kulankhula kukhoti monga “mabwenzi a khoti” (kapena kuti amicus curiae).”