KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?
Maofesi a Omasulira Mabuku Omwe Akuthandiza Anthu Mamiliyoni
MARCH 1, 2021
Magulu omasulira oposa 60 peresenti, amagwirira ntchito m’maofesi a omasulira mabuku, (RTO) osati m’maofesi a nthambi. Kodi zimenezi ndi zothandiza bwanji? Kodi amene akugwira ntchito yomasulira m’ma RTO amafunika zipangizo zotani kuti azigwira bwino ntchito yawo? Nanga kodi dera limene omasulirawa amagwirira ntchito limakhudza bwanji ntchito imene amagwira?
Ma RTO amathandiza omasulira kuti azikhala m’dera limene anthu ambiri amalankhula chilankhulo chimene akumasuliracho. Karin yemwe ndi mmodzi wa omasulira a Chijeremini Chosavuta ananena kuti: “Kungochokera pamene tinasamukira ku RTO yomwe ili ku Cuauhtémoc, mumzinda wa Chihuahua ku Mexico, nthawi zonse timalankhula chilankhulochi tikakhala ndi omasulira anzathu, mu utumiki komanso tikamakagula zinthu. Panopa timagwiritsira ntchito kwambiri chilankhulo chathu. Timamva anthu akulankhula mawu amene tatenga nthawi osawamva komanso timamva mmene anthu akulankhulira masiku ano.”
James, yemwe ali m’gulu la omasulira chilankhulo cha Chifalafala ku Ghana, ananena kuti nthawi zina amasowana ndi anzake omwe ali m’banja la Beteli ku ofesi ya nthambi. Koma anawonjezeranso kuti: “Ndimasangalala kugwirira ntchito pa RTO. Kulalikira m’chilankhulo changa n’kumaona mmene uthenga wabwino ukuwafikira anthu pamtima kumandisangalatsa kwambiri.”
Kodi abale athu amasankha bwanji malo oti amangepo RTO? Joseph yemwe ali mu Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga Padziko Lonse ku Warwick, New York, U.S.A, ananena kuti: “Vuto limodzi limene timakumana nalo ndi lakuti m’madera ena mulibe magetsi ndiponso madzi odalirika komanso muli vuto la intaneti yomwe ndi yofunika kuti abale athe kulandira nkhani zoti amasulire. Choncho tikamasankha malo oti kukhale ma RTO, timaganizira za malo angapo a m’madera omwe chilankhulocho chimalankhulidwa.”
Kunena zoona njira yachidule komanso yosawononga ndalama zambiri ndi kukhazikitsa RTO pa malo amene pali Nyumba ya Msonkhano, Nyumba ya Ufumu kapena nyumba ya amishonale kumene omasulira angamayendere kukagwira ntchito yawo. Ngati malo oterewa palibe abale angapatsidwe chilolezo kuti agule nyumba komanso maofesi oti omasulira azikhalako komanso azigwirirako ntchito. Ngati zinthu zimene omasulira akufunikira zitasintha, nyumbazi zikhoza kugulitsidwa ndipo ndalamazo zingagwiritsidwe ntchito pa zinthu zina.
Anapatsidwa Zipangizo Kuti Apitirize Ntchito
M’chaka cha utumiki cha 2020 ma RTO anagwiritsa ntchito ndalama zokwana madola 13 miliyoni a ku America. Magulu omasulira a m’ma RTO amafunika makompyuta, mapulogalamu apadera a pakompyuta, zipangizo zojambulira mawu, intaneti komanso zinthu zina zofunika pa ntchito yawo. Mwachitsanzo, kompyuta imene omasulira mmodzi amagwiritsa ntchito imafunika ndalama pafupifupi madola 750 a ku America. M’makompyutawa amaikamo mapulogalamu ena ochita kugula komanso pulogalamu ya Watchtower Translation System, imene imathandiza omasulira kuti azigwira bwino ntchito yawo komanso kupeza mosavuta zinthu zowathandiza pogwira ntchitoyi.
Omasulirawa amapatsidwanso zipangizo kuti azitha kujambula mawu ali m’maofesi. Zipangizo zimenezi zinathandiza kwambiri mliri wa COVID-19 utayamba, chifukwa omasulira ambiri anatenga zipangizozi n’kupita nazo kunyumba zawo kuti akapitirize kujambula zinthu zimene amasulira kuphatikizaponso mavidiyo.
Nthawi zambiri abale ndi alongo ongodzipereka a m’dera lomwe muli RTOyo amathandiza kuona ngati zinthu zimene amasulirazo zikumveka bwino komanso kusamalira zinthu zina pa RTOpo. Cirstin yemwe amatumikira pa RTO ya Chiafirikana ku Cape Town, ku South Africa, ananena kuti: “Ofalitsa ambiri komanso apainiya okhazikika ali ndi mwayi wodzagwira ntchito kuno.”
Abale ndi alongo omwe amadziperekawa amasangalala kwambiri. Mlongo wina yemwe amathandiza ntchito pa RTO ina ananena kuti kugwira ntchito ku RTO kuli ngati “kupuma kampweya kabwino.” Abale ndi alongo enanso amadzipereka kudzawerenga mawu a m’mavidiyo komanso zinthu zongomvetsera. Juana yemwe amagwira nawo ntchito yomasulira mabuku athu m’Chitotonaki m’dera la Veracruz, ku Mexico, ananena kuti: “Popeza kuti tsopano tili pafupi ndi madera omwe anthu ake amalankhula chilankhulo chathu, n’zosavuta kupeza abale ndi alongo ambiri omwe angamatithandize kuwerenga tikamajambula zinthu zongomvetsera komanso mavidiyo.”
Koma kodi ma RTO athandizadi kuti zomasulira zathu zizikhala zomveka bwino? Anthu ambiri amene amawerenga zimene timamasulira akuvomereza kuti athandizadi. Cédric yemwe amagwira nawo ntchito yomasulira mabuku anthu m’Chikongo ku Democratic Republic of Congo anati: “Abale ndi alongo ena ankanena kuti tikamamasulira timagwiritsa ntchito ‘Chikongo cha m’mabuku a Watch Tower,’ chifukwa chinkakhala chosiyana ndi Chikongo chimene anthu amalankhula. Koma panopa iwo amanena kuti timamasulira zinthu zathu m’Chikongo cha masiku ano chimene anthu amalankhula tsiku ndi tsiku.”
Andile yemwe amamasulira nawo m’chilankhulo cha Chikhosa ku South Africa, anamvanso zofanana ndi zimene anthu olankhula Chikongo ananena. Iye anati: “Anthu ambiri amatiuza kuti zimene tikumasulira zikumakhala zomveka bwino. Ngakhalenso ana amene ankakonda kuwerenga Nsanja ya Olonda ya Chingelezi panopa akumawerenga ya Chikhosa. Amakondanso kwambiri Baibulo la Dziko Latsopano Lokonzedwanso chifukwa limamveka bwino akamaliwerenga.”
Ndalama zimene anthu amapereka mwa kufuna kwawo zothandizira pa ntchito yapadziko lonse, kuphatikizaponso zomwe amapereka kudzera pa donate.pr418.com, ndi zimene zimagwiritsidwa ntchito pokhazikitsa ndi kukonza ma RTO komanso kusamalira abale ndi alongo amene amatumikira m’malo amenewa.