Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Nkhani Zodalirika Komanso Zolimbitsa Chikhulupiriro

Nkhani Zodalirika Komanso Zolimbitsa Chikhulupiriro

1 DECEMBER, 2021

 A Mboni za Yehova amakonda kwambiri abale ndi alongo awo. (1 Petulo 2:17) Ambiri tingavomereze zomwe mlongo wina wa ku Kenya dzina lake Tannis ananena. Iye ananena kuti: “Ndimafunitsitsa kuti ndizidziwa zomwe zikuchitikira abale ndi alongo anga padziko lonse.” Koma kodi Tannis ndi Amboni ena amadziwa bwanji zomwe zikuchitikira abale awowa? Kuyambira mu 2013, takhala tikulandira nkhani zokhudza a Mboni za Yehova kudzera pa Malo a Nkhani a pa webusaiti yathu ya jw.org.

 Pa Malo a Nkhani a pawebusaiti yathu pamapezeka nkhani ndi malipoti okhudza Mboni za Yehova. Nkhanizi zimakhala zokhudza kutulutsidwa kwa Baibulo m’zilankhulo zosiyanasiyana, ntchito yothandiza anthu pa nthawi ngozi zadzidzidzi, ntchito zomangamanga komanso zochitika zina zapadera. Pamalowa pamapezeka nkhani zokhudza abale ndi alongo athu omwe anamangidwa chifukwa chotsatira zomwe amakhulupirira. Pamapezekanso nkhani zolimbikitsa zofotokoza za ntchito yapadera yolalikira komanso za anthu omwe anapezeka pamwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Kodi ndi ndani amene amafufuza nkhani zimenezi, nanga amagwira bwanji ntchitoyi?

Kufufuza Komanso Kulemba Nkhani

 Dipatimenti Yoona Zofalitsa Nkhani, ndi imene imayang’anira ntchitoyi. Dipatimentiyi ili ku likulu lapadziko lonse ndipo imayang’aniridwa ndi Komiti ya Ogwirizanitsa ya Bungwe Lolamulira. Mu Dipatimenti ya Zofalitsa Nkhani muli abale ndi alongo oposa 100. Ambiri amagwira ntchitoyi ali kunyumba kwawo mongodzipereka. Ena mwa abale ndi alongowa amagwira ntchito ngati olemba nkhani, ochita kafukufuku, ojambula zithunzi komanso omasulira nkhani. Palinso ena omwe amalankhula ndi akuluakulu aboma, oona za maphunziro komanso atolankhani. Dipatimenti Yoona Zofalitsa Nkhani imagwira ntchito mothandizana ndi madipatimenti a zofalitsa nkhani a m’maofesi a nthambi oposa 80 padziko lonse.

 Akafuna kulemba nkhani ina yake, abale a mu Dipatimenti Yoona Zofalitsa Nkhani ya ku likulu, amagwira ntchito limodzi ndi abale a mu Dipatimenti ya Zofalitsa Nkhani ya ku nthambi imene kwachokera nkhaniyo. Abale a ku likulu akaona kuti nkhaniyo ndi yoyenera kufalitsidwa, amafufuza zina ndi zina zokhudza nkhaniyo. Pofufuzapo amatha kufunsa anthu ena komanso kulankhula ndi akatswiri osiyanasiyana. Akapeza mfundo zonse zofunika, amalemba nkhaniyo. Kenako amatsimikizira kuti palibe zolakwika zilizonse komanso amaikamo zithunzi. Zonse zikatha amaitumiza ku Komiti ya Ogwirizanitsa kuti akaone ngati ingafalitsidwe.

Mawu Othokoza

 Kodi abale ndi alongo athu amamva bwanji akawerenga nkhanizi? Mlongo wina wa ku Philippines dzina lake Cheryl ananena kuti: “Kukangocha ndimayamba kaye ndawerenga nkhani zokhudza gulu la Yehova ndi anthu ake.”

 Ambiri anaona kuti pali kusiyana pakati pa nkhani za pa jw.org ndi nkhani zopezeka m’malo ena. Mayi wina wa ku Kazakhstan dzina lake Tatiana ananena kuti: “Ndimakhulupirira nkhani za pa jw.org chifukwa zimakhala zodalirika.” Mlongo wina wa ku Mexico dzina lake Alma ananena kuti, “Nkhani za pawebusaiti yathu zimakhala zolimbikitsa kwambiri tikaziyerekezera ndi nkhani zochititsa mantha komanso zokhumudwitsa zomwe zimapezeka m’malo osiyanasiyana ofalitsira nkhani.”

 Nkhani za pawebusaiti yathu ndi zodalirika komanso zimalimbitsa chikhulupiriro. Bernard amene amakhala ku Kenya ananena kuti: “Nkhani za pawebusaiti yathu zandithandiza kuti ndiziona abale ndi alongo padziko lonse ngati anthu a m’banja langa, posatengera komwe amakhala. Ndikamapemphera, ndimatha kuwatchula mayina awo komanso zomwe zikuwachitikira.” Mlongo wina dzina lake Bybron amene amakhalanso ku Kenya ananena kuti: “Ndimasangalala kwambiri ndikawerenga nkhani yofotokoza kuti Baibulo la chilankhulo chinachake latuluka. Nkhanizi zimandithandiza kuona kuti Yehova ndi wopanda tsankho.”

Nkhani za pawebusaiti yathu zimatithandiza kuti tikamapemphera, tizitchula zochitika zenizeni zomwe abale ndi alongo athu akukumana nazo padziko lonse

 Ngakhalenso nkhani zofotokoza za abale omwe akuzunzidwa, zikhoza kutilimbikitsa. Jackline yemwe amakhala ku Kenya ananena kuti: “Chikhulupiriro changa chimalimba ndikaganizira za kulimba mtima kwawo.” Iye ananenanso kuti: “Ndimafunitsitsa nditadziwa zomwe zimawathandiza kuti apirire. Ndaphunzira kuti zinthu zosavuta monga kupemphera, kuwerenga Baibulo komanso kuimba, ndi zimene zimathandiza abale athu kuti akhale olimba.”

 Mlongo wina wa ku Costa Rica dzina lake Beatriz, anayamikira kwambiri nkhani zofotokoza za ngozi za m’chilengedwe zomwe zimaikidwa pamalo a nkhani. Iye ananena kuti: “Nkhani za pa webusaiti yathu zimandithandiza kuona mmene gulu lathu likuthandizira abale kupeza zinthu zofunika m’njira yofulumira, yodalirika komanso yachikondi. Zimenezi zimanditsimikizira kuti gulu la Yehova ndi limeneli basi.”

 Timathokoza kwambiri kuti timalandira nkhani zongochitika kumene zokhudza Akhristu anzathu padziko lonse. Zimenezi zikutheka chifukwa cha ndalama zomwe mumapereka ku ntchito yapadziko lonse. Zambiri mwa ndalama zimenezi mumapereka kudzera pa donate.pr418.com. Tikukuthokozani kwambiri chifukwa cha zopereka zanu komanso mtima wanu wopatsa.