Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KODI ZOPEREKA ZANU ZIMAGWIRITSIDWA NTCHITO BWANJI?

Nyimbo Zomwe Zimatithandiza Kuyandikira Mulungu

Nyimbo Zomwe Zimatithandiza Kuyandikira Mulungu

1 NOVEMBER 2021

 Nyimbo ndi mphatso yosangalatsa kwambiri yomwe Yehova anatipatsa. Zimakhudza mmene timaganizira, zimatithandiza kukhala osangalala tikakhumudwa komanso zimatilimbikitsa kuchita zinazake. Mmenemu ndi mmene zililinso ndi nyimbo zathu za broadcasting. Koma chofunika kwambiri n’chakuti nyimbozi zimatithandiza kuti tiyandikire Yehova.

 Kuyambira mu 2014, tatulutsa nyimbo za broadcasting zoposa 70. Panopo, nyimbo imodzi kapena zingapo zikupezeka m’zilankhulo zoposa 500. Koma mwina munadzifunsapo kuti, ‘kodi ndi ndani amagwira ntchito yokonza nyimbozi, nanga zimakonzedwa bwanji?’

Zimene Zimachitika Pokonza Nyimbozi

 Nyimbo za broadcasting zimakonzedwa ndi gulu la abale ndi alongo oona zanyimbo. Gululi lili Muofesi Yojambula Mavidiyo ndi Zinthu Zongomvetsera yomwe imayang’aniridwa ndi Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa ya Bungwe Lolamulira. M’gulu loona limeneli muli abale ndi alongo okwana 13 omwe amathandiza popeka nyimbo, kuchuna zipangizo zokonzera nyimbo, kukonza ndandanda komanso ntchito zina zofunika. Kuwonjezera pa gululi, Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa inavomereza kuti abale ndi alongo ongodzipereka padziko lonse azithandiza popeka, kulemba komanso kuimba nyimbo ali kunyumba kwawo. Abale ndi alongowa ndi odzichepetsa chifukwa safuna kuti azitamandidwa chifukwa cha lawo.

 Kodi nyimbo ya broadcasting imakonzedwa bwanji? Choyamba, Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa imaganizira kaye mfundo za m’Malemba zomwe akufuna kuti zikhale munyimbo komanso mmene idzakhudzire anthu. Kenako gulu loona za nyimbo limapeka nyimboyo ndi kulemba mawu ake. Akatero, amajambula nyimbo yongoyeserera. Abale a m’Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa, amamvetsera nyimboyo n’kuperekapo malangizo ena. Pambuyo pake, a gulu loona za nyimbo amasintha nyimbo ija mogwirizana ndi zomwe auzidwa. Kenako amajambulanso nyimbo yomaliza. Nyimbozi amazijambulira m’malo osiyanasiyana monga m’maofesi a nthambi komanso kunyumba za abale omwe ali ndi zipangizo zojambulira.

 Nyimbozi zimajambulidwa pogwiritsa ntchito makompyuta, mapulogalamu apakompyuta ndi zinthu zina. Pamafunikanso zipangizo zoimbira, masipika, mamaikolofoni ndi zina. Mtengo wogulira maikofoloni omwe amagwiritsidwa ntchito, umayambira madola 100 mpaka kuposa madola 1000 maikolofoni imodzi. M’chaka cha 2020, tinagwiritsa ntchito ndalama zokwana madola 116,000 pogula zipangizo zojambulira nyimbo.

 Kodi pamachitika zotani kuti ndalama zizigwiritsidwa ntchito moyenera? M’malo mokhala ndi gulu lalikulu loona za nyimbo pa Beteli, gulu likugwiritsa ntchito abale ndi alongo ambiri ongodzipereka omwe amagwirira ntchitozi kunyumba kwawo. Komanso m’malo mokhala ndi zida zambiri zoimbira, timagwiritsa ntchito mapulogalamu apakompyuta omwe amatulutsa mawu a zida zosiyanasiyana.

“Nyimbozi Zimandilimbitsa Chikhulupiriro”

 Abale ndi alongo amakonda kumvetsera nyimbo za broadcasting. Tara amene amakhala ku Germany ananena kuti: “Nyimbozi zimandithandiza ndikakhala ndi nkhawa. Ndikamamvetsera nyimbozi m’chilankhulo changa, ndimamva ngati Yehova wandikumbatira.” M’bale wina wa ku Kazakhstan dzina lake Dmitry anati: “Chimene chimandisangalatsa kwambiri ndikamamvetsera nyimbozi n’chakuti siudera kuti mwina nyimboyo ili ndi mawu ena osemphana ndi mfundo za m’Baibulo. Komanso, nyimbozi zimandithandiza kwambiri kuti ndiziganizira zinthu zauzimu.”

 Delia wa ku South Africa, anafotokoza mmene amasangalalira ndi nyimbo za broadcasting. Iye ananena kuti : “Nyimbozi zimandilimbitsa chikhulupiriro. Ndikakhala ndi nkhawa kapena ndikakumana ndi vuto linalake, pamakhala nyimbo yogwirizana ndi zomwe zandichitikira. Ndipo ngakhale zida zake zokha, zimakhala zokwanira kuti ndimve bwino.”

 Pali nyimbo zina zomwe anthu amazikonda kwambiri. Lerato yemwenso amakhala ku South Africa ananena kuti: “Nyimbo ngati ya ‘Dziko Latsopano Lili Pafupi’ komanso ya ‘Dziko Latsopano Lomwe Likubwera,’ zimandipangitsa kuganizira nthawi imene ndidzalandirenso mayi anga akamadzaukitsidwa. Nthawi iliyonse ndikamamvetsera nyimbozi, ndimakhala ngati ndikuwaona akundithamangira kuti andikumbatire.”

 Nyimbo ina inathandiza kwambiri mtsikana wina ku Sri Lanka. Iye ananena kuti: “Aphunzitsi anga a Sayansi anandinyoza pamaso pa azinzanga chifukwa choti ndine wa Mboni za Yehova. Ndinachita mantha ndipo ndinasowa chonena. Nditabwerera kunyumba, amayi anandilimbikitsa kuti ndimvetsere nyimbo yakuti: ‘Muziphunzira Kuti Mukhale Olimba.’ Nyimboyi inandilimbikitsa kuti ndizifufuza ndikukonzekera zoti ndiyankhe. Tsiku lotsatira ndinakakumana ndi aphunzitsi anga aja. Iwo anamvetsera ndipo ananena kuti ‘asangalala kumva zomwe a Mboni za Yehova timakhulupirira.’ Ndimayamikira gulu la Yehova potikonzera nyimbo zolimbikitsa ngati zimenezi.”

 Kodi ndalama zogwirira ntchito yokonza nyimbozi zimachokera kuti? Ndalamazi zimachokera ku zopereka za ntchito ya padziko lonse zomwe zimaperekedwa kudzera m’njira zingapo zopezeka pa donate.pr418.com. Tikukuthokozani kwambiri chifukwa cha mtima wanu wopatsa.