MILTIADIS STAVROU | MBIRI YA MOYO WANGA
“Taona Yehova Akutisamalira Komanso Kutitsogolera”
Mofanana ndi ana ena a msinkhu wanga, ndili ndi zaka pafupifupi 13, ndinkachita chidwi ndi magalimoto omwe ankadutsa mumsewu pafupi ndi nyumba yathu ku Tripoli m’dziko la Lebanon. Koma panali galimoto ina yofiira yomwe inkandisangalatsa kwambiri. Galimotoyi inali yopangidwa ku America koma mwini wake anali bambo winawake wa ku Syria. Koma tsiku lina ndinadabwa kwambiri wansembe wa tchalitchi chathu cha Orthodox atatiuza kuti tikangoona galimotoyo tiziyigenda chifukwa mwiniwake ndi wa Mboni za Yehova.
Tinauza wansembeyo kuti tikuopa chifukwa tikhoza kudzapweteka dalaivala wa galimotoyo. Iye anatiyankha kuti: “Inde mumuphe kumene. Wina akakufunsani, mumuuze kuti ndakutumani ndine.” Ngakhale kuti tchalitchi cha Greek Orthodox chinali chobadwira ndipo chinkandisangalatsa, zomwe wansembeyu ananena, zinandichititsa kuti pamapeto pake ndisiye tchalitchichi. Ndimaona kuti zomwe zinachitika panthawiyi, zinandipatsa mwayi woti ndidziwe choonadi chokhudza Yehova.
Kudziwa Choonadi Chokhudza Yehova
Pomwe ndinkakula, ndinkaona anthu a zilankhulo, zipembedzo komanso zikhalidwe zosiyanasiyana akubwera mumzinda wathu wa Tripoli. Banja lililonse kuphatikizaponso lathu, linkanyadira kudziwika ndi chikhalidwe chathu. Ine ndi azikulu anga tinalowa kagulu kena kotsutsa a Mboni za Yehova kotchedwa Asilikali Oteteza Chikhulupiriro. a Komabe tinali tisanakumanepo ndi Wamboni aliyense, kungoti wansembe wathu anatiuza kuti Amboni ndi gulu lomwe limalimbana ndi tchalitchi cha Orthodox ndipo mtsogoleri wawo ndi munthu winawake dzina lake Yehova. Mobwerezabwereza wansembeyo ankatiuza kuti paliponse pomwe mungakumane ndi a Mboni za Yehova muziwamenya.
Azichimwene anga atatu anali atakumanapo kale ndi a Mboni za Yehova kungoti ine sindinadziwe. Koma m’malo mowachitira nkhanza, azichimwene angawo anavomera kuti aziphunzira nawo Baibulo kuti apezerepo mwayi wowatsutsa pa zomwe amalakwitsa. Tsiku lina madzulo nditafika kunyumba, ndinapeza pabalaza pathu patadzaza Amboni, anthu a m’banja mwathu ndi anthu ena apafupi, akukambirana nkhani za m’Baibulo. Zinandikhumudwitsa kwambiri kuti azichimwene anga akucheza ndi Amboni chonsecho iwowo ndi a Orthodox. Ndikutembenuka kuti ndizibwerera, Wamboni wina yemwenso anali dokotala wodziwika bwino woona za mavuto a mano, anandiuza kuti ndikhale pansi ndizimvetsera. Pamenepo n’kuti wachibale wathu wina akuwerenga mokweza Salimo 83:18 kuchokera m’Baibulo langa. Nthawi yomweyo, ndinazindikira kuti wansembe wathu anatinamiza. Ndinazindikira kuti Yehova si dzina la munthu winawake wotsogolera gulu lazigawenga, koma ndi dzina la Mulungu woona.
Ndinkafuna kudziwa zambiri zokhudza Yehova, ndiye ndinayamba kupezeka paphunziro lomwe M’bale Michel Aboud ankachititsa akabwera kunyumba kwathu. Tsiku lina, mnzanga wina yemwe anapezeka nawo paphunzirolo anafunsa funso lomwe inenso linkandivutitsa maganizo kuyambira ndili mwana. Anafunsa kuti: “Mungatiuze kuti Mulungu anamulenga ndi ndani?” M’bale Aboud anatilozera mphaka yemwe anali atagona pampando chapafupi n’kutiuza kuti amphaka samvetsa zinthu zomwe anthufe timalankhula komanso kuganiza. Chimodzimodzinso anthufe, pali zinthu zambiri zokhudza Mulungu zomwe sitizimvetsa. Chitsanzochi chinandigwira mtima ndipo ndinamvetsa chifukwa chake chilengedwechi chili ndi zinthu zina zokhudza Yehova zomwe sindinkazimvetsa bwinobwino. Pasanapite nthawi yaitali, ndinadzipereka kwa Yehova n’kubatizidwa mu 1946 ndili ndi zaka 15.
Utumiki wa Upainiya Unandithandiza Kudziwa Zomwe Ndingachite ndi Moyo Wanga
Mu 1948 ndinayamba kugwira ntchito limodzi ndi mchimwene wanga Hanna yemwe anali ndi bizinesi yojambula zithunzi. Shopu yake inali pafupi ndi shopu ina yogulitsa penti yomwe mwiniwake anali m’bale wina dzina lake Najib Salem. b M’bale Salem ankakonda kulalikira ndipo sankachita mantha. Iye ankalalikira mopanda mantha mpaka pomwe anamwalira ali ndi zaka 100. Ndikapita naye limodzi kokalalikira kumidzi, ndinkaona kuti anali munthu wolimba mtima ngakhale pomwe anthu akumutsutsa. Ankathanso kukambirana ndi aliyense nkhani za m’Baibulo posatengera kuti munthuyo ndi wachipembedzo chanji. Zomwe ndinaphunzira kwa m’baleyu zinandithandiza kwa nthawi yaitali.
Tsiku lina ndili kuntchito, kunabwera mlongo wina wamtundu wa Chilebanizi dzina lake Mary Shaayah. Mlongoyu anali wochokera ku United States. Ngakhale kuti mlongoyu ankatanganidwa ndi kusamalira ana, koma ankalalikira mwakhama. Zomwe mlongoyu anatiuza pa tsiku limeneli, zinasintha moyo wanga. Mlongo Shaayah anatha maola awiri akutiuza zomwe ankakumana nazo akalowa muutumiki. Asanachoke, anandiyang’ana n’kundifunsa kuti “Milto, poti iweyo sunakwatire, bwanji osayamba upainiya?” Ndinamuuza kuti sindingachite upainiya, ndimafuna ndizigwira ntchito kuti ndizipeza ndalama. Ndiye anandifunsa kuti: “Ineyo ndakhala nthawi yaitali bwanji chibwerereni ku shopu kuno?” Ndinayankha kuti: “Pafupifupi maola awiri.” Kenako ananena kuti: “Komatu pa nthawi imeneyi sindinakuone utatanganidwa kwambiri. Ngati utamatha nthawi yochuluka chonchi tsiku lililonse, ukhoza kuchita upainiya. Ungoyesera kwa chaka chimodzi, kenako udzaone ngati ungadzathe kupitiriza kapena ayi.”
Ngakhale kuti anthu a chikhalidwe chathu samvetsera malangizo a mzimayi, ndinaona kuti zomwe anandiuza zinali zothandiza. Pambuyo pa miyezi iwiri, mu January 1952, ndinayamba utumiki waupainiya. Patatha pafupifupi miyezi 18, ndinaitanidwa kuti ndikalowe kalasi ya nambala 22 ya Sukulu ya Giliyadi.
Nditamaliza maphunzirowo, ndinatumizidwa ku Middle East. Pambuyo pake, chaka chisanathe, ndinakwatira Doris Wood, m’mishonale wansangala wochokera ku England yemwenso ankatumikira ku Middle East.
Kulalikira Choonadi cha M’Baibulo ku Syria
Patangopita nthawi yochepa titakwatirana, tinatumizidwa ku Aleppo m’dziko la Syria. Chifukwa choti ntchito yolalikira inali italetsedwa pa nthawiyo, ambiri omwe tinkaphunzira nawo Baibulo, anali anthu omwe anauzidwa zokhudza ifeyo kuchokera kwa anzawo omwe tinkaphunzira nawo.
Tsiku lina tinapita kunyumba kwa mayi wina yemwe anasonyeza chidwi. Anatitsegulira chitseko ali ndi mantha n’kutiuza kuti: “Muyenera kusamala kwambiri, apolisi anali pompano. Amafunsa za komwe mumakhala.” Apa zinaonekeratu kuti apolisi achinsinsi anadziwa za komwe tinkachititsa maphunziro a Baibulo. Zitatero tinaimbira foni abale omwe ankayang’anira ntchito yathu ku Middle East ndipo anatiuza kuti tisamuke m’dzikolo nthawi yomweyo. Ngakhale kuti zinatikhudza kuti tinasiyana ndi anthu omwe tinkaphunzira nawo Baibulo, koma tinaona kuti Yehova anatiteteza mwachikondi.
Yehova Anatitsogolera Tili ku Iraq
Mu 1955, tinatumizidwa ku Baghdad m’dziko la Iraq. Ngakhale kuti tinkalalikira anthu onse mosamala, koma makamaka tinkalikira anthu azipembedzo zachikhristu.
Tinkayesetsanso kucheza mwansangala ndi Asilamu m’misika ndi m’misewu. Nthawi zambiri Doris ankalankhula zinazake kuti akope chidwi cha anthu omwe wakumana nawo. Mwachitsanzo, iye ankanena kuti: “Bambo anga ankakonda kutiuza kuti aliyense adzayankha yekha kwa Mulungu.” (Aroma 14:12) Kenako ankanenanso kuti: “Kukumbukira mawu amenewa kunandithandiza kwambiri pa moyo wanga. Inuyo munganenepo zotani zokhudza mawu amenewa?”
Tinachita utumiki wathu ku Baghdad kwa pafupifupi zaka zitatu ndipo tinathandiza abale ndi alongo a kumeneko mmene angamachitire zinthu mosamala polalikira. Tinkagwiritsa ntchito nyumba ya amishonale kuchitiramo misonkhano yomwe inkachitika m’Chiarabu. Tinasangalala kwambiri kulandira anthu a mitima yabwino a mtundu wa Asuri omwe ambiri mwa iwo anali Akhristu. Ataona kuti pamisonkhano yathu tinkachita zinthu mwachikondi komanso mogwirizana, anavomereza kuti ndifedi ophunzira a Yesu.—Yohane 13:35.
Munthu woyamba kuphunzira choonadi anali bambo wina wodzichepetsa wochokera ku Armenia koma wamtundu wa Asuri, dzina lake Nicolas Aziz. Nicolas ndi mkazi wake Helen anavomereza mwamsanga zomwe Baibulo limaphunzitsa zokhudza Yehova ndi mwana wake Yesu, kuti ndi anthu awiri osiyana. (1 Akorinto 8:5, 6) Ndimakumbukirabe tsiku lomwe Nicolas ndi anthu ena 20 anabatizidwa mumtsinje wa Firate.
Yehova Anatithandiza Kwambiri Tili ku Iran
Nthawi ina, anthu ena analanda boma la Iraq zomwe zinachititsa kuti pa 14 July 1958, mtsogoleri wa dzikolo Mfumu Faisal II aphedwe. Chifukwa cha zomwe zinachitikazi, tinathamangitsidwa m’dzikolo n’kupita ku Iran. Ku Iran, tinapitiriza kuchita utumiki wathu mosamala kwambiri kwa miyezi 6 ndipo tinkalalikira anthu ochokera m’mayiko ena.
Titangotsala pang’ono kusamuka ku Tehran, lomwe ndi likulu la dziko la Iran, ndinaitanidwa ndi apolisi kuti akandifunse mafunso. Zitatero ndinazindikira kuti apolisi akutifufuza. Apolisi atamaliza kundifunsa mafunso, ndinaimbira Doris foni n’kumuuza kuti apolisi akutilondalonda. Kuti tikhale otetezeka, ine ndi Doris tinagwirizana kuti ndisabwere kunyumba komanso kuti tisakumane kaye kwa kanthawi kochepa mpaka nthawi yotuluka m’dzikolo.
Doris anapeza malo ena komwe anakakhala mpaka tsiku lomwe tinakumana ku bwalo la ndege. Koma mwina mukufunsa kuti, kodi Doris anakwanitsa bwanji kupita ku bwalo la ndege popanda apolisi kudziwa? Iye anapemphera kwa Yehova kuti amuthandize.
Kenako mwadzidzidzi kunagwa mvula yamphamvu ndipo aliyense kuphatikizapo apolisi anafunikira kuthawira pamalo abwino. Mumsewu munalibe aliyense, ndipo zimenezi zinapereka mwayi kwa Doris kuti ayende mosavuta. Doris ananena kuti: “Mvula imene ija inali chozizwitsa chochokera kwa Yehova.”
Titachoka ku Iran, tinatumizidwa ku gawo lina komwe tinayamba kulalikira anthu azikhalidwe komanso zipembedzo zosiyanasiyana. Mu 1961, tinayamba utumiki woyang’anira dera ndipo tinkayendera Akhristu anzathu m’madera osiyanasiyana a ku Middle East.
Yehova Anatithandiza ndi Mzimu Wake
Tinali ndi mwayi woona mmene mzimu woyera wa Mulungu wathandizira anthu kukhala ogwirizana pomwe takhala tikuchita utumiki wathu ku Middle East. Ndimakumbukirabe mmene zinkakhalira pa nthawi yomwe tinkaphunzira ndi anthu awiri a ku Palestina, Eddy ndi Nicolas. Ankakonda kupezeka pa misonkhano, koma pasanapite nthawi yaitali, anasiya kuphunzira Baibulo chifukwa ankachita nawo zandale. Ndinapemphera kuti Yehova awathandize kuzindikira choonadi. Atazindikira kuti Mulungu adzathetsa mavuto a anthu onse kuphatikizapo mavuto a anthu a ku Palestina, anayambiranso kuphunzira. (Yesaya 2:4) Anasiya kukhala ndi maganizo okonda kwambiri dziko lawo ndipo anabatizidwa. Patapita nthawi, Nicolas anakhala woyang’anira dera wakhama kwambiri.
Pomwe tinkayenda m’mayiko osiyanasiyana, ine ndi Doris tinkasangalala kuona kuti abale ali ndi chikhulupiriro cholimba ngakhale atakumana ndi zotani. Chifukwa choti abale athu ankakumana ndi mavuto, ndinkayesetsa kuti ndiziwalimbikitsa ndikamayendera mipingo. (Aroma 1:11, 12) Kuti ndikwanitse kuchita zimenezi, ndinkafunika kukumbukira kuti ndine wofanana nawo ndipo sindiwaposa mwanjira iliyonse. (1 Akorinto 9:22) Ndinkasangalala kwambiri ndikalimbikitsa Akhristu anzanga amene akufunika thandizo.
Takhalanso tikusangalala kuona anthu ambiri omwe takhala tikuphunzira nawo Baibulo, akuyamba kutumikira Yehova mokhulupirika. Ambiri mwa anthuwa anasamukira ku mayiko ena ndi mabanja awo pothawa zipolowe zomwe zinkachitika m’mayiko awo. Komabe kumayiko omwe anathawira monga ku Australia, Canada, Europe ndi United States, akuthandiza kwambiri m’mipingo ya Chiarabu. M’zaka za posachedwa, ana ena akuluakulu a m’mabanja amenewa, anabwereranso ku Middle East kukathandiza ku madera omwe kukufunika olalikira Ufumu ambiri. Ine ndi Doris ndife osangalala kwambiri kuti timadziwana ndi abale ndi alongo ambiri omwe timawaona ngati ana komanso zidzukulu zathu.
Tinaphunzira kuti Tizidalira Yehova Mpaka Kalekale
Pa moyo wathu, taona Yehova akutisamalira komanso kutitsogolera m’njira zambiri. Ndimayamikira kuti anandithandiza kuthetsa maganizo atsankho komanso okonda kwambiri dziko langa ngati mmene zinalili ndili mwana. Komanso, maphunziro omwe ndinapatsidwa ndi Akhristu anzanga anandithandiza kuti ndizikhala wokonzeka kulalikira uthenga wa m’Baibulo kwa aliyense posatengera komwe munthuyo akuchokera. Pomwe tinkachita utumiki wathu m’mayiko osiyanasiyana, takumanapo ndi mavuto ambiri komanso zinthu zina zomwe sitinkaziyembekezera. Zimenezi zinatithandiza kuti tizidalira kwambiri Yehova Mulungu m’malo modzidalira.—Salimo 16:8.
Ndikaganizira zaka zambiri zomwe takhala tikutumikira Yehova, ndimaona kuti ndili ndi zambiri zoti ndipereke kwa Atate wathu wakumwamba. Ndikugwirizana ndi zomwe Doris amanena nthawi zambiri kuti, palibe chilichonse chomwe chingatilepheretse kupereka utumiki wopatulika kwa Yehova, ngakhale titaopsezedwa kuti tiphedwa. Sitidzasiya kuyamikira Yehova chifukwa chotilola kugwira ntchito yofalitsa uthenga wamtendere ku Middle East. (Salimo 46:8, 9) Sitikhala ndi nkhawa tikaganizira za m’tsogolo chifukwa timadziwa kuti Yehova adzapitiriza kutsogolera ndi kuteteza anthu omwe amamudalira.—Yesaya 26:3.
a Kuti mudziwe zambiri zokhudza kaguluka, werengani Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 1980, tsamba 186-188.
b Mbiri ya moyo wa Najib Salem inafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda ya September 1, 2001, tsamba 22-26.