Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kumanzere: Mphepo yamkuntho ya Ian, ku Florida, USA, mu September 2022 (Sean Rayford/Getty Images); pakati: Mayi ali pa ulendo wothawa ndi mwana wake wamwamuna, ku Donetsk, Ukraine, mu July 2022 (Alex Chan Tsz Yuk/SOPA Images/LightRocket via Getty Images); kumanja: Anthu akuyezetsa COVID, ku Beijing, China, mu April 2022 (Kevin Frayer/Getty Images)

KHALANI MASO

M’chaka cha 2022 Tinakumana Ndi Mavuto Ambiri​—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

M’chaka cha 2022 Tinakumana Ndi Mavuto Ambiri​—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 M’chaka cha 2022, sizinali zachilendo kumva nkhani zokhudza nkhondo, mavuto azachuma komanso kuwonongeka kwa chilengedwe. Baibulo lokha ndi limene lingatiuze zolondola zokhudza tanthauzo la zimene zinachitikazi.

Kodi zochitika za mu 2022 zikutanthauza chiyani kwenikweni?

 Mavuto ambiri amene tinakumana nawo chaka chatha, ndi umboni wakuti tikukhaladi munthawi imene m’Baibulo imatchedwa “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1) Nthawi imeneyi inayamba mu 1914. Taonani mmene zochitika za masiku ano zikugwirizanirana ndi zimene Baibulo linaneneratu kuti zidzachitika m’nthawi yathu ino:

 “Nkhondo.”​—Mateyu 24:6.

  •   “2022 Chinali Chaka Chimene Anthu ku Europe Anakumana Ndi Mavuto Ambiri Chifukwa cha Kuyambiranso kwa Nkhondo.” a

 “Njala.”​—Mateyu 24:7.

  •   “2022 Chinali Chaka Chimene Kunali Njala Yoopsa.” b

 “Miliri.”​—Luka 21:11.

  •   “Matenda a poliyo anayambiranso, matenda a monkeypox anakhala vuto lalikulu ndipo COVID-19 ikupitirizabe kuvutitsa anthu. Zimenezi zinasonyezeratu kuti matenda opatsirana ndi oopsa kwambiri komanso kuti anthu angapatsirane mosavuta.” c

 Onani nkhani yakuti, “Anthu 6 Miliyoni Anamwalira ndi Matenda a COVID.”

 “Zoopsa.”​—Luka 21:11.

  •   “Kunachitika chilala, moto wolusa, kusefukira kwa madzi komanso dziko lapansi linatentha kwambiri. Kusintha kwa nyengo kunapangitsa kuti nyengo yotentha ya mu 2022 ikhale yosaiwalika chifukwa zinthu zambiri zinawonongeka, anthu masauzande ambiri anafa komanso anthu mamiliyoni padziko lonse anasowa pokhala.” d

 Onani nkhani yakuti, “Kunja Kukutentha Modetsa Nkhawa.”

 “Zipolowe”​—Luka 21:9.

  •   “Chifukwa cha mavuto azachuma makamakanso chifukwa cha kukwera mitengo kwa zinthu, mu 2022 anthu ambiri anali okwiya zomwe zinachititsa kuti pakhale ziwonetsero zambiri zodana ndi maboma.” e

 Onani nkhani yakuti, “Kukwera Mitengo kwa Zinthu Padziko Lonse.”

Kodi chaka chamawa kuchitika zotani?

 Palibe akudziwiratu zimene zitachitike m’chaka cha 2023, koma chomwe tikudziwa n’chakuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu kapena kuti boma lakumwamba libweretsa kusintha kwakukulu padziko lapansili. (Danieli 2:44) Boma limeneli lidzachotsa zinthu zimene zimapangitsa kuti anthu azivutika ndipo lidzaonetsetsanso kuti cholinga cha Mulungu chakwaniritsidwa padziko lapansi.​—Mateyu 6:9, 10.

 Tikukulimbikitsani kuti muzitsatira malangizo a Yesu Khristu komanso kuti ‘muzikhala maso’ kuona mmene zinthu zimene zikuchitika padzikoli zikukwaniritsira ulosi wa m’Baibulo. (Maliko 13:37) Lankhulani nafe kuti mudziwe mmene Baibulo lingakuthandizireni panopa, komanso mmene lingathandizire inuyo ndi banja lanu kukhala ndi chiyembekezo chenicheni cha tsogolo labwino.

a Nkhani ya Chingelezi yolembedwa ndi Jill Lawless yakuti, “2022 Chinali Chaka Chimene Anthu ku Europe Anakumana Ndi Mavuto Ambiri Chifukwa cha Kuyambiranso kwa Nkhondo.” (AP News, “2022 Was Year the Horror of War Returned to Europe,” by Jill Lawless, December 8, 2022.)

b Nkhani yakuti, “Kusowa kwa Chakudya Padziko Lonse,” (Bungwe la World Food Programme, “A Global Food Crises.”)

c Nkhani yakuti, “Living in an Age of Pandemics​—From COVID-19 to Monkeypox, Polio, and Disease X,” JAMA Health Forum, yolembedwa ndi Lawrence O. Gostin, JD, September 22, 2022.

d Nkhani yakuti, “What’s Behind the Record-Breaking Extreme Weather Events of Summer 2022?” Earth.Org, yolembedwa ndi Martina Igini, October 24, 2022.

e Nkhani yakuti, “Economic Anger Dominated Global Protests in 2022,” Carnegie Endowment for International Peace, yolembedwa ndi Thomas Carothers ndi Benjamin Feldman, December 8, 2022.