Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

JenkoAtaman/stock.adobe.com

KHALANI MASO

Yambani Chaka cha 2023 Muli Ndi Chiyembekezo—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Yambani Chaka cha 2023 Muli Ndi Chiyembekezo—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Pamene tangolowa kumene m’chaka cha 2023, tonsefe tili ndi chiyembekezo chakuti zinthu zizitiyendera bwino limodzi ndi mabanja athu. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi chiyembekezo?

Baibulo limatipatsa chiyembekezo

 Baibulo limatiuza uthenga wabwino wakuti mavuto amene tikukumana nawo panopa ndi akanthawi ndipo posachedwapa athetsedwa. Ndipotu Baibulo ‘linalembedwa kuti litilangize. Malembawa amatipatsa chiyembekezo . . . ndiponso amatilimbikitsa.’Aroma 15:4.

Chiyembekezo chomwe chingakuthandizeni panopa

 Chiyembekezo cha m’Baibulo “chili ngati nangula wa miyoyo yathu.” (Aheberi 6:19, mawu am’munsi) Chiyembekezo chimenechi chingatithandize kuti tisamatekeseke. Chimatithandiza kuti tizitha kupirira mavuto, tiziona zinthu moyenera ndiponso kuti tidzakhale osangalala mpaka kalekale. Mwachitsanzo:

Muzilimbitsa chiyembekezo chanu

 Anthu ambiri amafuna zinthu zabwino zitachitika, koma sakhulupirira ndi mtima wonse kuti zidzachitikadi. Koma zimene Baibulo limalonjeza n’zosiyana ndi zimenezi. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa malonjezo a m’Baibulo ndi ochokera kwa Yehova Mulungu a mwiniwake, “amene sanganame.” (Tito 1:2) Ndi Yehova yekha amene ali ndi mphamvu zokwaniritsa malonjezo ake onse; iye amatha kuchita ‘chilichonse chimene . . . akufuna kuchita.’—Salimo 135:5, 6.

 Tikukulimbikitsani kuti muphunzire zokhudza chiyembekezo chodalirika cha m’Baibulo. Mungathe kulimbitsa chiyembekezo chanu mwa “kufufuza Malemba mosamala.” (Machitidwe 17:11) Pemphani kuti muyambe kuphunzira Baibulo kwaulere mothandizidwa ndi munthu wina wa Mboni Yehova. Yambani chaka cha 2023 muli ndi chiyembekezo cha tsogolo labwino!

a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu.—Salimo 83:18.