KHALANI MASO!
Mungakhale Ndi Chiyembekezo Chabwino mu 2024—Kodi Baibulo Limanena Zotani?
Anthu ambiri akuona kuti mavuto amene tingakumane nawo mu 2024 sangathe. Komabe, n’zotheka kukhala ndi chiyembekezo chakuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo. Kodi zimenezi zingatheke bwanji?
Baibulo limatipatsa chiyembekezo
Baibulo limatilonjeza kuti Mulungu adzathetsa mavuto onse amene akuchititsa kuti tisamakhale ndi chiyembekezo. Posachedwapa, Mulungu “adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kubuula kapena kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.
Kuti mudziwe zambiri zokhudza zimene Baibulo limalonjeza za tsogolo lathu, werengani nkhani yakuti “Tiziyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo.”
Mmene Baibulo lingakuthandizireni panopa
Baibulo limatipatsa chiyembekezo cha tsogolo lomwe lingakuthandizeni kuti musamade nkhawa kwambiri ndi kuyamba kuona zinthu moyenera. (Aroma 15:13) Malangizo a m’Baibulo angakuthandizeninso kulimbana ndi mavuto amene mukukumana nawo panopa monga umphawi, kupanda chilungamo ndi matenda.
Onani mmene Baibulo linathandizira bambo wina kukhala ndi mtendere komanso chimwemwe ngakhale kuti anakula movutika. Onerani vidiyo yakuti Juan Pablo Zermeño: Yehova Anandithandiza Kukhala ndi Moyo Watanthauzo.
Onani mmene Baibulo lingakuthandizireni kulimbana ndi mavuto monga kudziimba mlandu, kumva chisoni, nkhawa komanso imfa ya munthu yemwe mumamukonda. Werengani nkhani yakuti “Kodi M’Baibulo Mungapezeke Mawu Omwe Angandilimbikitse?”
Onani mmene mayi wina yemwe anali msilikali “wovuta komanso wosasamala za ena” anasinthira moyo wake chifukwa chophunzira Baibulo. Onerani vidiyo yakuti Ndinasiya Usilikali.
Yesetsani kuchita zomwe mungathe kuti moyo wanu ndi wa banja lanu ukhale wabwino m’chaka chino cha 2024. Phunzirani zambiri kuti muone mmene Baibulo lingakuthandizireni. Yeserani kuphunzira Baibulo mochita kukambirana kwaulere. Phunzirani kuti muone mmene Mulungu angakupatsireni “mtendere” panopa komanso “tsogolo labwino ndi chiyembekezo chabwino.”—Yeremiya 29:11.