Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

E+/taseffski/via Getty Images (Stock photo. Posed by model.)

KHALANI MASO

Achinyamata Ambiri Akuvutika Ndi Matenda Amaganizo—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Achinyamata Ambiri Akuvutika Ndi Matenda Amaganizo—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Lolemba pa 13 February 2023, bungwe loona za umoyo la ku United States (Centers for Disease Control and Prevention, CDC) linatulutsa lipoti lokhudza achinyamata am’dzikoli omwe ali ndi vuto la matenda amaganizo. Zikuoneka kuti 40 peresenti ya ana a kusekondale amakhala okhumudwa komanso opanda chiyembekezo.

 Dr. Kathleen Ethier yemwe ndi mkulu wa bungwe la CDC ndi Division of Adolescent and School Health (DASH), ananena kuti: “Tapeza kuti vuto la matenda amaganizo pakati pa achinyamata lawonjezereka kwambiri pa zaka 10 zapitazo. Koma kuposa kale lonse, vutoli lakula kwambiri pakati pa atsikana ndipo pali atsikana ambiri amene akumaganiza zodzipha kapena kuyesa kudzipha.”

 Lipoti la pa 13 February 2023, linanena kuti:

  •   Atsikana oposa 14 pa 100 aliwonse, azaka zoyambira 13 mpaka 18, amakakamizidwa kuchita chiwerewere. Dr. Ethier ananena kuti: “Zimenezi n’zokhumudwitsa chifukwa pa atsikana 10 aliwonse, mmodzi kapena kuposa pamenepo anagwiriridwapo.”

  •   Pafupifupi mtsikana mmodzi pa atatu aliwonse, azaka zoyambira 13 mpaka 18, anaganizirapo kwambiri zofuna kudzipha.

  •   Pafupifupi atsikana atatu pa 5 aliwonse, azaka zoyambira 13 mpaka 18, amangokhala okhumudwa kapena opanda chiyembekezo.

 Malipotiwa ndi okhudza mtima kwambiri. Nthawi imene munthu ali wachinyamata amafunika azisangalala. Ndiyeno n’chiyani chomwe chingathandize achinyamata kuti azitha kupirira mavuto amenewa? Kodi Baibulo limanena zotani?

M’Baibulo muli malangizo othandiza achinyamata

 Baibulo limafotokoza momveka bwino kuti tizikumana ndi zinthu zambiri zodetsa nkhawa. Ndipo linanena kuti, ‘tidzakhala m’nthawi yapadera komanso yovuta.’ (2 Timoteyo 3:1-5) Komabe, Baibulo limapereka malangizo othandiza achinyamata mamiliyoni padziko lonse kulimbana ndi mavuto amene akukumana nawo. Taonani nkhani zotsatirazi zochokera m’Baibulo.

 Mfundo zothandiza achinyamata omwe ali ndi maganizo ofuna kudzipha

 Mfundo zothandiza achinyamata kulimbana ndi matenda amaganizo, kukhumudwa kapena maganizo olakwika

 Mfundo zothandiza achinyamata akamavutitsidwa ndi anzawo

 Mfundo zothandiza achinyamata omwe akukumana ndi nkhanza zokhudza kugonana

Baibulo limapereka malangizo othandiza kwa makolo

 Baibulo limaperekanso malangizo kwa makolo kuti azithandiza ana awo kupirira mavuto omwe akukumana nawo. Taonani nkhani zotsatirazi zochokera m’Baibulo.