Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Baibulo Lingathandize Amuna Amene Ali Ndi Nkhawa

Baibulo Lingathandize Amuna Amene Ali Ndi Nkhawa

 Mukaganizira za munthu yemwe akuvutika ndi nkhawa, a mwina m’maganizo mwanu mukubwera munthu yemwe ali ndi mantha kwambiri moti akuopa kudzuka, kapenanso amene amangokhalira kulankhula zinthu zodandaula.

 Anthu ena akakhala ndi nkhawa amachitadi zinthu zimenezi. Komabe, ochita kafukufuku apeza kuti anthu ena makamaka amuna amachita zosiyana ndi zimenezi akakhala ndi nkhawa. Lipoti lina linanena kuti amuna “amatha kumwa mowa kapenanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kuti athane ndi nkhawa. Choncho munthu yemwe angaoneke ngati ali ndi vuto lakumwa kwambiri mowa angakhale kuti akuvutika kwambiri ndi nkhawa. Ndipo amuna ambiri amene akuvutika ndi nkhawa sachedwa kukwiya komanso kupsa mtima.”

 Ngakhale kuti si amuna onse amene amachita zimenezi akakhala ndi nkhawa, koma zikuoneka kuti nkhawa ndi vuto lalikulu kwambiri popeza tili ‘m’masiku otsiriza [omwe ndi] nthawi yapadera komanso yovuta.’ (2 Timoteyo 3:1) Ngati inunso mukuvutika ndi nkhawa, musataye mtima chifukwa Baibulo likhoza kukuthandizani.

Mfundo za M’Baibulo Zingakuthandizeni Kuthana Ndi Nkhawa

 Baibulo lili ndi malangizo ambiri omwe angatithandize tikakhala ndi nkhawa. Taonani zitsanzo zitatu izi.

  1.  1. “Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.”​—Mateyu 6:34.

     Tanthauzo lake: Ndi nzeru kupewa kudera nkhawa kwambiri zinthu zomwe zingachitike (kapenanso zimene sizingachitike) m’tsogolo. Nthawi zambiri zinthu zomwe zimachitika sizikhala zomwe timadera nkhawa kuti zingadzachitike. Ndipotu pena timadabwa kuona kuti zomwe zachitika ndi zabwino osati zoipa.

     Yesani izi: Ganizirani nthawi inayake m’mbuyomu pomwe munkaganiza kuti zinazake zoipa zikhoza kuchitika koma sizinachitike. Ndiye ganiziraninso zinthu zomwe zikukudetsani nkhawa panopa n’kuona ngati ndi mavutodi aakulu oyenera kukudetsani nkhawa.

  2.  2. “Chitsulo chimanola chitsulo chinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.”​—Miyambo 27:17.

     Tanthauzo lake: Tikakhala ndi nkhawa anthu ena angatithandize pokhapokha ngati tawauza. Iwo angatiuze mfundo zothandiza malinga ndi zimene zinawachitikirapo. N’kuthekanso kuti angatithandize kuona zinthu m’njira yoyenera.

     Yesani izi: Ganizirani munthu wina yemwe angakupatseni malangizo abwino, mwina angakhale mnzanu amene anakwanitsa kuthana ndi mavuto amene mukukumana nawo panopa. Mufunseni kuti akuuzeni zomwe zinamuthandiza kapenanso zomwe sizinamuthandize.

  3.  3. ‘Mumutulire nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’​—1 Petulo 5:7.

     Tanthauzo lake: Mulungu amadera nkhawa kwambiri anthu onse amene akuvutika. Iye amatiuza kuti tizimuuza chilichonse chimene chikutidetsa nkhawa.

     Yesani izi: Ganizirani zinthu zonse zimene zikukudetsani nkhawa. Kenako pempherani kwa Mulungu n’kumufotokozera vuto lililonse komanso kumupempha kuti akuthandizeni kuthana ndi vutolo.

Nkhawa Zidzatheratu

 Kuwonjezera potipatsa malangizo otithandiza tikakhala ndi nkhawa, Baibulo limatilonjezanso kuti m’tsogolomu sitidzakhalanso ndi nkhawa ngakhale pang’ono. Kodi zimenezi zidzatheka bwanji?

 Ufumu wa Mulungu udzachotseratu zinthu zonse zimene zimatidetsa nkhawa. (Chivumbulutso 21:4) Ndipotu mu Ufumu umenewu sitidzakumbukiranso zinthu zodetsa nkhawa kapenanso kuziganizira.​—Yesaya 65:17.

 Moyo woterewu ndi umene “Mulungu amene amapatsa mtendere” akufuna kuti mudzakhale nawo m’tsogolomu. (Aroma 16:20) Iye akutitsimikizira kuti: “Maganizo anga kwa inu ndikuwadziwa bwino. Ndikuganizira zokupatsani mtendere osati masoka, kuti mukhale ndi chiyembekezo chabwino ndiponso tsogolo labwino.” (Yeremiya 29:11)

a M’nkhaniyi mawu akuti “nkhawa” sakugwiritsidwa ntchito ponena za matenda ovutika maganizo koma akuimira nkhawa zomwe munthu amatha kukhala nazo tsiku lililonse. Amene akudwala matenda ovutika maganizo angachite bwino kukaonana ndi adokotala.​—Luka 5:31.