Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KHALANI MASO

Anthu 6 Miliyoni Anamwalira ndi Matenda a COVID​—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Anthu 6 Miliyoni Anamwalira ndi Matenda a COVID​—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Mogwirizana ndi zomwe Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse linanena, pofika pa 23 May 2022, anthu okwana 6,270,000 anamwalira chifukwa cha COVID-19. Komabe, mogwirizana ndi lipoti lomwe linatuluka pa 5 May 2022, bungweli linati zikuoneka kuti anthu omwe anamwalira ndi mliriwu ndi ochuluka kwambiri kuposa pamenepa. Linanenanso kuti kuchoka mu 2020 kukafika mu 2021, “anthu onse omwe anamwalira chifukwa cha mliri wa COVID-19 ndi enanso omwe anamwalira ndi matendawa koma ali kale ndi mavuto ena aakulu m’thupi mwawo, . . . analipo pafupifupi 14,900,000.” Kodi Baibulo limanenapo chilichonse pa nkhani zomvetsa chisoni ngati zimenezi?

Baibulo linaneneratu kuti kudzakhala miliri yoopsa

 Ulosi umene Yesu ananenawu, ukukwaniritsidwa masiku ano. Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti “Kodi Chizindikiro cha ‘Masiku Otsiriza’ Kapena Kuti Nthawi ‘ya Mapeto’ N’chiyani?

Baibulo lili ndi uthenga wotonthoza

  •   “Mulungu amene amatitonthoza . . . amatitonthoza m’masautso athu onse.”—2 Akorinto 1:3, 4.

 Ambiri amene anaferedwa anthu omwe ankawakonda, anatonthozedwa atawerenga uthenga wa m’Baibulo. Phunzirani zambiri munkhani yakuti, “Zimene Zingakuthandizeni Mukaferedwa—Zimene Mungachite Panopa” ndi yakuti, “Mfundo Zofunika Kwambiri Kwa Anthu Omwe Aferedwa.”

Baibulo limatiuza njira yokhalitsa yothetsera vutoli

  •   “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chimodzimodzinso pansi pano”—Mateyu 6:10.

 Posachedwa “Ufumu wa Mulungu” udzaonetsetsa kuti “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’” (Maliko 1:14, 15; Yesaya 33:24) Onerani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani? kuti mudziwe zambiri zokhudza boma lakumwambali komanso zomwe lidzachite.

 Tikukupemphani kuti muphunzire zomwe Baibulo limanena n’cholinga choti inuyo limodzi ndi banja lanu, mupindule ndi malangizo komanso malonjezo othandiza ochokera kwa Mulungu.