Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ahmad Gharabli/AFP via Getty Images

KHALANI MASO

Kodi Mayiko Angagwirizane Pothana Ndi Vuto la Kusintha Kwa Nyengo?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Mayiko Angagwirizane Pothana Ndi Vuto la Kusintha Kwa Nyengo?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Lamlungu pa 20 November 2022, mayiko anamaliza kuchita Msonkhano wa Nambala 27 wa Bungwe la United Nations Woona za Kusintha kwa Nyengo (COP27). Atsogoleri komanso akatswiri amene anapezeka pamsonkhanowu, anagwirizana kuti apereke ndalama kumayiko osauka n’cholinga choti awathandize kuthana ndi mavuto obwera chifukwa cha kusintha kwa nyengo. Komabe, anthu ambiri ananena kuti kuchita zimenezi sikungathetse mavutowo.

  •   Pa 19 November 2022, a António Guterres omwe ndi mlembi wamkulu wa United Nations, ananena kuti “Ndikugwirizana ndi zoti tikhazikitse thumba la ndalama zothandizira anthu omwe akuvutika chifukwa cha kusintha kwa nyengo. Komabe, tikudziwa kuti ndalama zimenezi sizingakwanire . . . Dziko lathuli likudwala mwakayakaya, moti lili pangozi yoti sitingathe kulikonzanso.”

  •   Pa 20 November 2022, a Mary Robinson omwe anali pulezidenti wakale wa dziko la Ireland komanso omwe anali kazembe wamkulu wa bungwe la UN woona za ufulu wa anthu, ananena kuti “Posachedwapa dziko lapansili likumana ndi mavuto aakulu okhudza kusintha kwa nyengo ndipo zimenezi zikhudza aliyense.”

 Achinyamata ndi amene ali ndi nkhawa kwambiri akaganizira za tsogolo la dzikoli. Komabe, kodi mayiko angagwirizane pothana komanso pokwaniritsa zomwe alonjeza zokhudza kusintha kwa nyengo? Kodi Baibulo limanena zotani?

Kodi mayiko angakonzedi zinthu atachita zinthu mogwirizana?

 Baibulo limatiuza kuti ngakhale maboma atayesetsa kusintha zinthu kuti athane ndi mavuto a kusintha kwa nyengo, sangakwanitse kuthetseratu mavuto amenewa. Taonani zifukwa ziwiri izi:

  •   “Chinthu chokhota sichingawongoledwe.”—Mlaliki 1:15.

     Tanthauzo lake: Maboma sangakwaniritse kuchita zonse zimene akufuna chifukwa anthu sanalengedwe kuti azitha kudzilamulira okha. (Yeremiya 10:23) Ngakhale mayiko atayesetsa kugwirizana, sizingatheke kuti athetse mavuto a padzikoli, ngakhale atachita zambiri pofuna kuthana ndi mavutowa.

  •   “Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, . . . osafuna kugwirizana ndi anzawo.”—2 Timoteyo 3:2, 3.

     Tanthauzo lake: Baibulo linalosera molondola kuti anthu ambiri masiku ano adzakhala odzikonda komanso osafuna kugwira ntchito limodzi ndi ena kuti athandize anzawo.

Chimene chimatipangitsa kukhala ndi chiyembekezo

 Tsogolo la dzikoli silidalira pa malonjezo ochokera ku maboma a anthu. Mulungu watipatsa Wolamulira wa dziko lonse lapansi yemwe ndi wabwino kwambiri, Yesu Khristu. Ponena za iye Baibulo limati:

  •   “Paphewa pake padzakhala ulamuliro. Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga Wamtendere.”—Yesaya 9:6.

 Yesu ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kapena kuti boma la kumwamba. (Mateyu 6:10) Iye ali ndi mphamvu, nzeru ndipo ndi wofunitsitsa kusamalira dzikoli komanso anthu omwe amakhalamo. (Salimo 72:12, 16) Kudzera mu ulamuliro wake, boma la kumwamba limeneli lidzawononga “amene akuwononga dziko lapansi” ndipo lidzakonzanso dzikoli kukhala labwino.—Chivumbulutso 11:18; Yesaya 35:1, 7.

 Kuti mudziwe zambiri zokhudza njira yabwino yothetsera mavuto obwera chifukwa cha kuwonongeka kwa nyengo, werengani nkhani yakuti “Zomwe Baibulo Limanena pa Nkhani Yakusintha Kwa Nyengo Komanso Tsogolo Lathu.”