KHALANI MASO
Kodi Mungakhulupirire Ndani?—Zimene Baibulo Limanena?
Anthu amakhumudwa zikakhala kuti anthu amene amawaona kuti ndi odalirika awagwiritsa fuwa la moto. Zimenezi zachititsa kuti ambiri asiye kukhulupirira . . .
atsogoleri andale amene amaika zofuna zawo patsogolo osati za anthu amene amawaimira.
ofalitsa nkhani amene amalephera kufalitsa nkhani molondola komanso mosakondera.
asayansi amene sachita zinthu zokomera anthu.
atsogoleri achipembezo amene amalowerera kwambiri zochitika za ndale m’malo mogwira ntchito ya Mulungu.
Anthu samalakwitsa kukhala osamala pa nkhani ya amene akuyenera kuwakhulupirira. Baibulo limachenjeza kuti:
“Musamakhulupirire atsogoleri, palibe munthu amene angathe kukupulumutsani.”—Salimo 146:3, Good News Translation.
Amene mungamukhulupirire
Baibulo limatchula winawake amene mungamukhulupirire, Yesu Khristu. Sikuti iye anangokhala munthu wabwino amene anakhalapo zaka zambiri zapitazo. Mulungu anamuika kuti ‘adzalamulire monga Mfumu . . . ndipo Ufumu wake sudzatha.’ (Luka 1:32, 33) Yesu ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, boma limene panopa likulamulira kuchokera kumwamba.—Mateyu 6:10.
Kuti mudziwe chifukwa chake mungakhulupirire Yesu, werengani nkhani yakuti “Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu Ndi Ndani?” komanso “Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?”