Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KHALANI MASO

Kukwera Mitengo Kwa Zinthu Padziko Lonse—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kukwera Mitengo Kwa Zinthu Padziko Lonse—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Mulipoti la June 2022, mtsogoleri wa gulu la mabungwe oona za kayendetsedwe ka zachuma padziko lonse ananena kuti: “Chuma nachonso sichikuyenda bwino padziko lonse. Mitengo yazinthu ikukwera mofulumira komanso anthu alibe ndalama zokwanira zoti n’kugwiritsa ntchito.”—World Bank Group.

 Bungwe Loona Zachuma Padziko Lonse linanena kuti: “Mafuta a galimoto komanso chakudya, zakwera mtengo kwambiri ndipo izi zakhudza anthu ambiri okhala m’mayiko osauka.”

 Baibulo limafotokoza momveka bwino chifukwa chake tikukumana ndi mavuto azachuma ngati amenewa, zomwe tingachite kuti tipirire komanso chiyembekezo chomwe tingakhale nacho chofotokoza mmene vutoli lidzathere mpaka kalekale.

Kukwera mitengo kwa zinthu ‘m’masiku otsiriza’

  •   Baibulo limatchula nthawi yomwe tikukhalayi kuti “masiku otsiriza.”—2 Timoteyo 3:1.

  •   Yesu ananena kuti nthawi yathu ino, “kudzaoneka zoopsa” kapena kuti zinthu zochititsa mantha. (Luka 21:11) Anthu amachita mantha zinthu zikamakwera mitengo. Amadera nkhawa tsogolo lawo komanso mmene angasamalirire mabanja awo.

  •   Buku la Chivumbulutso linaneneratu kuti m’masiku athu ano zinthu zidzakhala zokwera mtengo. “Ndinamva chomveka ngati mawu. . .  kuti; ‘muyeso umodzi wa tirigu wa malipiro a tsiku limodzi.’”—Chivumbulutso 6:6, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero.

 Kuti mudziwe zambiri zokhudza “masiku otsiriza” komanso za ulosi wa m’buku la Chivumbulutso, onerani vidiyo yakuti, Zinthu Padzikoli Zinasintha Kuyambira mu 1914. Komanso werengani nkhani yakuti “Kodi Anthu 4 Okwera Pamahatchi Akuimira Chiyani?

Mmene mavuto azachuma adzathere

  •   “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake. Sadzamanga wina n’kukhalamo. Sadzabzala wina n’kudya.”—Yesaya 65:21, 22.

  •   “Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”—Salimo 72:16.

  •   “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa osautsika, chifukwa cha kuusa moyo kwa anthu osauka, ndidzanyamuka pa nthawiyo, ndidzawateteza.”—Salimo 12:5. a

 Posachedwa Mulungu athetsa mavuto onse azachuma, osati m’dziko limodzi lokha, koma padziko lonse. Kuti mudziwe mmene adzachitire zimenezi, werengani nkhani yakuti, “Kodi Mayiko Angathe Kuyendetsa Chuma Mokomera Aliyense?

 Komabe, ngakhale panopo Baibulo lingakuthandizeni kudziwa zomwe mungachite ndi vuto la kukwera mitengo kwa zinthu. Lingakuthandizeni bwanji? Lili ndi malangizo omwe angakuthandizeni kuti muzigwiritsa ntchito ndalama zanu mwanzeru. (Miyambo 23:4, 5; Mlaliki 7:12) Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti, “Muzisamala Ndalama” komanso yakuti, “Zimene Mungachite Ngati Mukupeza Ndalama Zochepa.”

a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu.—Salimo 83:18.