Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pezani Anzanu Abwino Kuti Musamasungulumwe—Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?

Pezani Anzanu Abwino Kuti Musamasungulumwe—Kodi Baibulo Lingakuthandizeni Bwanji?

 M’chaka cha 2023, akatswiri a zaumoyo anapeza kuti kusungulumwa ndi vuto lalikulu lokhudza thanzi la munthu ndipo pakufunika kupeza njira yothetsera vutoli. Kodi n’zothekadi kuthetsa vutoli?

  •   Dr. Vivek Murthy, yemwe amapanga maopaleshoni ku United States anati: “Tikamasungulumwa komanso kumangochita zinthu patokha, tingathe kuwononga thanzi lathu n’kumangokhala okhumudwa.” Iye ananenanso kuti: “Tingathe kuchitapo kanthu. [Zimenezi zingatheke] tikamayesetsa kuchita zinthu zing’onozing’ono tsiku lililonse kuti tizicheza komanso kulimbitsa ubwenzi wathu ndi anthu ena.” a

 Si nthawi zonse pamene munthu amamva kusungulumwa chifukwa choti amakonda kukhala yekhayekha. Anthu ena amasungulumwa ngakhale pamene ali pagulu la anzawo. Kaya timasungulumwa pa zifukwa zotani, Baibulo lingatithandize kulimbana ndi vutoli. Baibulo lili ndi malangizo osonyeza zimene tingachite kuti tizicheza komanso kugwirizana ndi ena, zomwe zingatithandize kuchepetsa vuto losungulumwa.

Mfundo za m’Baibulo zomwe zingatithandize

 Muzidziwa kulankhulana bwino ndi ena. Musamangofotokoza mmene inuyo mukumvera basi koma mufunikanso kumamvetsera zimene anzanu akukufotokozerani. Mukamasonyeza kuti muli ndi chidwi ndi anzanu, mumayamba kugwirizana nawo kwambiri.

  •   Mfundo ya m’Baibulo: “Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.”​—Afilipi 2:4.

 Muzicheza ndi anthu osiyanasiyana. Muziyesetsa kucheza ndi anthu amisinkhu yosiyanasiyana kapenanso amene mumasiyana nawo zinthu zina monga kochokera, chikhalidwe kapena mayiko.

  •   Mfundo ya m’Baibulo: “Tsegulani kwambiri mitima yanu.”​—2 Akorinto 6:13.

 Kuti mudziwe zambiri zimene mungachite kuti muzigwirizana kwambiri ndi ena, werengani nkhani yakuti “Kupeza Anzathu Omwe Timalakalaka.”

a Our Epidemic of Loneliness and Isolation: The U.S. Surgeon General’s Advisory on the Healing Effects of Social Connection and Community, 2023.