Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Baibulo Limanena Zotani Zokhudza Kusowa kwa Chakudya Masiku Ano?

Kodi Baibulo Limanena Zotani Zokhudza Kusowa kwa Chakudya Masiku Ano?

 “Kuthetseratu njala.” Mawu amenewa akunena za cholinga chimene atsogoleri amayiko ali nacho chofuna kuthetsa vuto lina lalikulu limene anthu padziko lonse akukumana nalo ndipo akufuna kupeza njira zothana ndi njala padziko lonse. a Koma kodi njala idzathadi padzikoli? Kodi Baibulo limanena zotani?

Baibulo linalosera za kusowa kwa chakudya padzikoli masiku ano

 Baibulo linalosera kuti m’nthawi yathu ino chakudya chizidzasowa ndipo nthawiyi imatchedwa “masiku otsiriza.” Mulungu si amene amachititsa kusowa kwa chakudya koma anatichenjeza zokhudza zimenezi. (Yakobo 1:13) Taonani maulosi awiri a m’Baibulo awa:

 “Kudzakhala njala . . . m’malo osiyanasiyana.” (Mateyu 24:7) Ulosi wa m’Baibulo umenewu unaneneratu kuti kudzakhala njala m’malo ambiri. Lipoti lina laposachedwapa lochokera kwa akatswiri oona za chakudya, linati: “Zinthu m’dzikoli sizikuyenda bwino pa nkhani yothetsa njala ndipo chakudya chopatsa thanzi chikusowa kwambiri.” b Anthu mamiliyoni ochuluka m’mayiko ambiri akulephera kupeza chakudya chokwanira. N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri akumwalira chifukwa cha njala.

 “Nditayang’ana, ndinaona hatchi yakuda. Amene anakwera pahatchiyo anali ndi sikelo m’dzanja lake.” (Chivumbulutso 6:5) Mu ulosiwu, hatchi yophiphiritsira komanso wokwerapo wake zikuimira njala imene ikuchitika m’masiku otsiriza. c Sikelo yomwe ili m’dzanja la wokwera pahatchi ntchito yake ndi kuyeza kulemera kwa chakudya choperewera n’cholinga choti chigawidwe kwa anthu kuti aliyense alandireko pang’onopang’ono. Kenako mawu anamveka olengeza kuti zinthu zidzakwera mitengo kwambiri ndipo anachenjeza anthu kuti asamale chakudya chochepa chomwe ali nacho. (Chivumbulutso 6:6) Zimenezi zikusonyeza vuto la kusowa kwa chakudya padziko lonse masiku ano ndipo anthu mabiliyoni akulephera kupeza chakudya kapenanso sangathe kukhala ndi chakudya chopatsa thanzi.

Kodi vuto la kusowa kwa chakudya lidzatha bwanji?

 Akatswiri amanena kuti dziko lapansili limatulutsa chakudya chokwanira kudyetsa aliyense. Koma n’chifukwa chiyani chakudya chikusowa? Nanga kodi Baibulo limanena kuti Mlengi wathu, Yehova, d adzachita zotani pothana ndi vuto limeneli?

 Vuto: Maboma sangathe kuthetsa umphawi komanso kusankhana pa nkhani ya zachuma zomwe zikupangitsa kuti anthu ambiri azivutika ndi njala.

 Njira yothetsera vutoli: Maboma omwe akuyendetsedwa ndi anthu opanda ungwiro adzalowedwa m’malo ndi boma labwino lomwe ndi Ufumu wa Mulungu. (Danieli 2:44; Mateyu 6:10) Masiku ano, anthu ambiri osauka akulephera kupeza chakudya, koma zimenezi zidzasintha mu Ufumu wa Mulungu. Baibulo limanena kuti Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu: “Adzapulumutsa wosauka amene akufuula popempha thandizo, komanso wonyozeka ndi aliyense amene alibe womuthandiza. Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri. Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.”​—Salimo 72:12, 16.

 Vuto: Nkhondo zimawononga zinthu komanso zimabweza m’mbuyo zachuma zomwe zimachititsa kuti anthu azivutika kupeza chakudya chomwe amafunikira.

 Njira yothetsera vutoli: “[Yehova ] akuthetsa nkhondo padziko lonse lapansi. Wathyola uta ndi kupindapinda mkondo. Ndipo wawotcha pamoto magaleta ankhondo.” (Salimo 46:9) Mulungu adzawononga zida zonse za nkhondo komanso anthu omwe amayambitsa nkhondo. Akadzachita zimenezi, aliyense adzakwanitsa kupeza chakudya chabwino mosavutikira. Baibulo limalonjeza kuti: “Wolungama zinthu zidzamuyendera bwino, ndipo padzakhala mtendere wochuluka.”​—Salimo 72:7.

 Vuto: Nyengo yovuta komanso ngozi zam’chilengedwe zikuwononga mbewu zakumunda komanso ziweto.

 Njira yothetsera vutoli: Mulungu adzathetsa zinthu zonse zimene zimachititsa kuti anthu azisowa chakudya ndipo padzikoli padzakhala chakudya chochuluka. Baibulo limati: “[Yehova] amachititsa kuti mphepo yamkuntho ikhale bata, mafunde apanyanja amadekha. . . . Chipululu amachisandutsa dambo la madzi, ndipo dziko louma amalisandutsa dera la akasupe amadzi. Amachititsa kuti anthu anjala azikhala kumeneko, . . . Anthuwo amafesa mbewu n’kulima minda ya mpesa, kuti akhale ndi zokolola.”​—Salimo 107:29, 35-37.

 Vuto: Anthu adyera komanso akatangale amapanga chakudya chosasamalika kapenanso amasunga chakudya moti anthu ena sachipeza.

 Njira yothetsera vutoli: Ufumu wa Mulungu udzachotsa anthu onse osaona mtima komanso akatangale. (Salimo 37:10, 11; Yesaya 61:8) Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu ndi “Amene amaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa anthu amene achitiridwa chinyengo, Amene amapereka chakudya kwa anthu anjala.”​—Salimo 146:7.

 Vuto: Chaka chilichonse, 30 peresenti ya chakudya cha padziko lonse chimawonongeka kapena kutayidwa.

 Njira yothetsera vutoli: Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira, anthu amene akuyang’anira chakudya azidzayendetsa bwino zinthu. Yesu ali padzikoli, ankaonetsetsa kuti chakudya chikusamalidwa kuti chisatayidwe. Mwachitsanzo, pa nthawi ina anadyetsa mozizwitsa gulu la anthu oposa 5,000. Kenako, anauza ophunzira ake kuti: “Sonkhanitsani zotsala zonse, kuti pasawonongeke chilichonse.”​—Yohane 6:5-13.

 Anthu onse adzasangalala ndi chakudya chabwino ndiponso chopatsa thanzi chifukwa Ufumu wa Mulungu udzathetsa zinthu zonse zimene zimayambitsa njala. (Yesaya 25:6) Kuti mudziwe zambiri zokhudza nthawi imene Ufumu wa Mulungu udzachite zimenezi, werengani nkhani yakuti, “Kodi Ufumu wa Mulungu Udzayamba Liti Kulamulira Dzikoli?

a Mfundo za chitukuko chokhazikika zokhudza ndondomeko za mu 2030 zovomerezedwa ndi mayiko omwe anachita mgwirizano ndi bungwe la United Nations mu 2015.

b Lipoti la bungwe la Food and Agriculture Organization of the United Nations, International Fund for Agricultural Development, United Nations Children’s Fund, United Nations World Food Programme, komanso World Health Organization.

c Kuti mudziwe zambiri zokhudza anthu 4 okwera pamahatchi, werengani nkhani yakuti, “Kodi Anthu 4 Okwera Pamahatchi Akuimira Chiyani?

d Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu (Salimo 83:18) Werengani nkhani yakuti, “Kodi Yehova Ndi Ndani?