Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Katangale Adzatha M’Boma?

Kodi Katangale Adzatha M’Boma?

 Pafupifupi kulikonse padzikoli, akuluakulu aboma amachita zakatangale ndipo zimenezi zikuchititsa mavuto aakulu. a Mwachitsanzo, pa nthawi ya mliri wa COVID-19, m’mayiko ambiri, akuluakulu aboma ankadzudzulidwa chifukwa choba ndalama zomwe zikanagwiritsidwa ntchito pothandiza anthu omwe anakhudzidwa ndi mliriwu. Zimenezi zinachititsa kuti anthu ambiri avutike komanso kufa chifukwa sanakwanitse kupeza chithandizo choyenera chakuchipatala.

 Katangale wafika poipa kwambiri m’boma. Nduna yaikulu yakale ya boma la United Kingdom, a David Cameron ananena kuti: “Nkhani zakatangale zafika poipa kwambiri moti mayiko onse akukhudzidwa ndi vutoli.”

 Komabe ndife otsimikiza kuti posachedwa zakatangale zonse zomwe zimachitika m’boma zidzatha. N’chifukwa chiyani tikutero? Onani zimene Baibulo limanena pofotokoza zomwe Mulungu adzachite.

Chifukwa chake tingakhale otsimikiza kuti Mulungu adzathetsa zakatangale

 M’Baibulo muli mawu awa omwe Mulungu ananena: “Ndimakonda chilungamo. Ndimadana ndi zauchifwamba ndi kupanda chilungamo.” b (Yesaya 61:8) Anthu akamavutika chifukwa cha zinthu zachinyengo zomwe anthu ena amachita, Mulungu amaona. (Miyambo 14:31) Iye akulonjeza kuti: “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa osautsika, . . . Ndidzanyamuka pa nthawiyo, ndidzawateteza.”—Salimo 12:5.

 Kodi Mulunguyo adzachita chiyani? M’malo mongosintha zina ndi zina m’maboma omwe alipowa, iye adzawachotsa n’kukhazikitsapo boma lake lakumwamba lomwe limatchedwa kuti “Ufumu wa Mulungu.” (Maliko 1:14, 15; Mateyu 6:10) Baibulo limati: “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa Ufumu umene . . . udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.” (Danieli 2:44) Mmenemu ndi mmene Mulungu adzathetsere zachinyengo zonse zomwe zikuchitika masiku ano.

Boma lopanda zakatangale

 Kodi timadziwa bwanji kuti boma la Ufumu wa Mulungu lidzakhala lopanda zakatangale? Taganizirani izi.

  1.  1. Mphamvu. Ufumuwo uzidzalandira mphamvu zake kuchokera kwa Mulungu Wamphamvuyonse.—Chivumbulutso 11:15.

     Kudziwa zimenezi n’kothandiza bwanji? Kuti maboma a anthu akwanitse kuyendetsa zinthu, amadalira ndalama zomwe nzika zawo zimapereka. Nthawi zambiri zimenezi zimapereka mwayi woti anthu ena azichita zachinyengo komanso kuba. Mosiyana ndi zimenezi, Ufumuwu uzidzathandizidwa ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Choncho nthawi zonse udzakwanitsa kupatsa nzika zake zinthu zofunikira.—Salimo 145:16.

  2.  2. Wolamulira. Mulungu anasankha Yesu Khristu kuti akhale Wolamulira wa Ufumu wake.—Danieli 7:13, 14.

     Kudziwa zimenezi n’kothandiza bwanji? Ngakhale munthu amene anali wolamulira wabwino poyamba, amatha kusintha chifukwa chosokonezedwa ndi anthu ena. (Mlaliki 7:20) Mosiyana ndi anthu, Yesu anasonyezeratu kuti sangalandire ziphuphu. (Mateyu 4:8-11) Kuwonjezera pamenepo, iye amakonda anthu omwe ndi nzika za Ufumu wake komanso ndi wofunitsitsa kuwathandiza.—Salimo 72:12-14.

  3.  3. Malamulo. Malamulo a Ufumu wa Mulungu ndi angwiro komanso anthu omwe amawatsatira amakhala osangalala.—Salimo 19:7, 8.

     Kudziwa zimenezi n’kothandiza bwanji? Nthawi zambiri malamulo opangidwa ndi anthu amakhala ovuta kuwamvetsa, olemetsa komanso amagwiritsidwa ntchito molakwika ndipo amapereka mwayi woti pazichitika zachinyengo. Mosiyana ndi zimenezi, malamulo a Mulungu amakhala omveka bwino komanso othandiza. (Yesaya 48:17, 18) Kuwonjezera pamenepo, malamulowa amakhudzanso zochita za anthu komanso mmene amaganizira. (Mateyu 22:37, 39) Komanso chifukwa chakuti Mulungu amadziwa zamumtima mwathu, iye amaonetsetsa kuti malamulowo akutsatiridwa chifukwa chotikonda.—Yeremiya 17:10.

 Dziwani zambiri zokhudza malonjezo a m’Baibulo a m’tsogolo onena za boma lopanga chinyengo lomwe lidzalamulire dzikoli.

a Mogwirizana ndi dikishonale ina, mawu akuti “katangale,” amatanthauza kugwiritsa ntchito molakwika udindo womwe uli nawo ndi cholinga chofuna kupeza phindu.

b Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Werengani nkhani yakuti, “Kodi Yehova ndi Ndani?