Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Photo by Zhai Yujia/China News Service/VCG via Getty Images

KHALANI MASO

Madzi Osefukira—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Madzi Osefukira—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Padziko lonse lapansi, anthu ambiri akhudzidwa ndi vuto la madzi osefukira. Tiyeni tione malipoti otsatirawa:

  •   “Masiku angapo apitawa, kulikulu la dziko la China kunagwa mvula yamphamvu kwambiri kuposa mvula imene yakhala ikugwa m’zaka zosachepera 140 zapitazo. Mvulayi inagwa kuyambira Loweruka mpaka Lachitatu ndipo inali yochuluka mamilimita 744.8.”​—AP News, August 2, 2023.

  •   “Lachinayi, mphepo yamkuntho yotchedwa Typhoon Khanun inachititsa kuti kum’mwera kwa dziko la Japan kugwe mvula komanso mphepo yamphamvu yomwe inapha anthu osachepera awiri . . . . Zikuoneka kuti mphepoyi ichititsa kuti mvula yochuluka mamita 0.6 igwe m’chigawo chapakati cha m’madera okwera m’dziko la Taiwan.”​—Deutsche Welle, August 3, 2023.

  •   “Kumapeto kwa mlungu wathawu, mvula yamphamvu yomwe inagwa m’mphepete mwa nyanja ya Atlantic ku Canada inabwera chifukwa cha madzi osefukira [am’chigawo cha Nova Scotia] ndipo inali yamphamvu kwambiri kuposa imene yakhala ikugwa m’zaka 50 zapitazo.”​—BBC News, July 24, 2023.

 Kodi Baibulo limati chiyani pa zochitika ngati zimenezi?

Chizindikiro cha “masiku otsiriza”

 Baibulo limanena kuti tikukhala m’nthawi imene imatchedwa “masiku otsiriza.”(2 Timoteyo 3:1) Yesu ananeneratu kuti munthawi yathu ino, ‘tiziona zoopsa’ kapena kuti zinthu zochititsa mantha. (Luka 21:11)Kusintha kwa nyengo n’kumene kukuchititsa kuti kunja kuzisintha nthawi ndi nthawi, mosayembekezereka komanso modabwitsa.

Chifukwa chake tiyenera kukhala ndi chiyembekezo

 Baibulo limatiuza kuti zinthu zambiri zochititsa mantha zomwe zikuchitika masiku ano zimatithandiza kukhala ndi chiyembekezo. Chifukwa chiyani? Yesu ananena kuti: “Mukadzaona zimenezi zikuchitika, mudzadziwe kuti Ufumu wa Mulungu wayandikira.”​—Luka 21:31; Mateyu 24:3.

 Zochitika zimene tikuonazi zikusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu watsala pang’ono kuthetsa mavuto onse okhudza chilengedwe monga kusefukira kwa madzi komanso mphepo zamkuntho.​—Yobu 36:27, 28; Salimo 107:29.

 Kuti mudziwe zambiri zokhudza zimene Ufumu wa Mulungu udzachite pokonzanso dzikoli kuti likhale labwino, werengani nkhani yakuti “Kodi Ndi Ndani Amene Adzapulumutse Dzikoli?