Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

kovop58/stock.adobe.com

KHALANI MASO

Kodi Masewera a Olimpiki Angathandizedi Anthu Kukhala Ogwirizana?—Zimene Baibulo Limanena

Kodi Masewera a Olimpiki Angathandizedi Anthu Kukhala Ogwirizana?—Zimene Baibulo Limanena

 Anthu pafupifupi 5 biliyoni aonera masewera a Olimpiki a 2024, omwe aseweredwe ndi akatswiri ochokera m’mayiko 206. Thomas Bach, yemwe ndi pulezidenti wa bungwe loyang’anira masewerawa la International Olympic Committee, ananena kuti: “Tikuchita masewera amene amagwirizanitsa anthu padziko lonse komanso kulimbikitsa mtendere. Tiyeni tisangalale ndi masewerawa mwamtendere, monga anthu amodzi komanso ogwirizana ngakhale kuti timasiyana pa zinthu zina.”

 Kodi masewera a Olimpiki angathandizedi anthu kuchita zomwe amafunazi? Kodi zingatheke kuti padzikoli anthu adzakhale mwamtendere komanso mogwirizana?

Kodi masewerawa angathandizedi anthu kukhala mwamtendere komanso mogwirizana?

 Pa Olimpiki ya chaka chino pachitika zambiri kuwonjezera pa masewera. Nkhani zimene zimakambidwa kwambiri ndi zokhudza ndale komanso zina zimene zimagawanitsa anthu. Zimenezi ndi monga zokhudza ufulu wachibadwidwe, kusankhana mitundu, kusalana pa nkhani ya zipembedzo ndiponso tsankho.

 Anthu amasangalala pa nthawi ya masewera a mayiko monga masewera a Olimpiki. Komabe, pa masewerawa pamachitikanso zinthu zomwe zimachititsa anthu kugawikana, m’malo mowathandiza kukhala mwamtendere komanso mogwirizana.

 Baibulo linaneneratu kuti anthu adzakhala ndi makhalidwe omwe akuchititsa kuti masiku ano zikhale zovuta kuti padzikoli pakhale mgwirizano. (2 Timoteyo 3:1-5) Kuti mudziwe zambiri zokhudza ulosi wa m’Baibulowu, werengani nkhani yakuti “Kodi Baibulo Linaneneratu za Mmene Anthu Adzidzaganizira ndi Kuchitira Zinthu Masiku Ano?

N’chiyani chingathandizedi anthu padziko lonse kukhala mwamtendere komanso mogwirizana?

 Baibulo limatiuza chimene chidzathandize anthu padziko lonse kukhala mwamtendere komanso mogwirizana. Limalonjeza kuti anthu onse padzikoli adzakhala ogwirizana akamadzalamuliridwa ndi boma lakumwamba, lomwe limatchedwa “Ufumu wa Mulungu.”—Luka 4:43; Mateyu 6:10.

 Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu ya Ufumu umenewu, adzabweretsa mtendere padziko lonse. Baibulo limati:

  •   “Wolungama zinthu zidzamuyendera bwino.”—Salimo 72:7.

  •   “Adzapulumutsa wosauka amene akufuula popempha thandizo . . . Adzawapulumutsa kuti asaponderezedwe komanso kuchitiridwa zachiwawa.”—Salimo 72:12, 14.

 Ngakhale masiku ano, zimene Yesu anaphunzitsa zathandiza anthu mamiliyoni ochokera m’mayiko 239 kukhala ogwirizana. Akhristu a Mboni za Yehova padziko lonse aphunzira kukhala anthu amtendere. Kuti mudziwe chimene chimawathandiza, werengani Nsanja ya Olonda yamutu wakuti “Kodi N’zotheka Kuthetsa Chidani?.”