Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kim Steele/The Image Bank via Getty Images

NTCHITO YAPADERA YOLALIKIRA

Mavuto Azachuma—Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?

Mavuto Azachuma—Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Zotani?

 Anthu ambiri padziko lonse akuvutika kwambiri kupeza ndalama zokwanira kugula zinthu zofunika pa moyo.

  •   Lipoti lina lapadziko lonse laposachedwapa, a linanena kuti “ndalama zimene anthu amapeza pamwezi sizikumakwanira kugulira zinthu zofunikira chifukwa cha kuchepa mphamvu kwa ndalama.” Lipotili linachenjeza kuti vutoli likapanda kuthetsedwa “pakhala kusiyana kwakukulu pakati pa anthu olemera ndi osauka ndipo mabanja azivutika kwambiri kupeza zinthu zofunika pa moyo.”

 Kodi maboma angakwanitse kuthetsa mavuto azachuma amenewa kapena kuwachepetsako?

 Baibulo limanena kuti pali boma limene lingakwanitse kuthetsa mavuto onse azachuma komanso kusiyana kwa anthu pa nkhani ya kapezedwe ka zinthu zofunika pa moyo. Limanena kuti “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu,” womwe ndi boma limene lizidzayendetsa zinthu zonse padzikoli. (Danieli 2:44) Boma limeneli likamadzalamulira palibe aliyense amene adzaiwalidwe kapena kunyalanyazidwa. (Salimo 9:18) Anthu amene adzalamuliridwe ndi Ufumu wa Mulungu adzakhala ndi chilichonse chomwe chidzawathandize kukhala osangalala. Aliyense adzasangalala mokwanira ndi ntchito ya manja ake.​—Yesaya 65:21, 22.

a International Labour Organization Global Wage Report 2022-23