Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Asayansi Afukula Zikutsimikizira Kuti Mfumu Davide Analikodi

Zimene Asayansi Afukula Zikutsimikizira Kuti Mfumu Davide Analikodi

Baibulo limasonyeza kuti Mfumu Davide anakhalapo zaka za m’ma 1000 B.C.E. ndipo ana ndi adzukulu ake analamulira kwa zaka mahandiredi ambiri. Koma anthu ena amanena kuti Davide kunalibe moti nkhani yake inangopekedwa. Koma kodi Mfumu Davide analikodi?

Mu 1993, wasayansi wina dzina lake Avraham Biran ndi anzake anafukula mwala ku Tel Dan, chakumpoto kwa dziko la Israel. Pamwalawu panalembedwa mawu onena za “Nyumba ya Davide.” Anthu anapeza kuti mawuwa analembedwa cha m’ma 800 B.C.E. Zikuoneka kuti mwalawu unali pachipilala chimene Aaramiya anamanga posangalala kuti agonjetsa Aisiraeli.

Nkhani ina ya pa intaneti inanena kuti: “Anthu ena ankaona kuti mawu opezeka pamwalawu sanali umboni wodalirika . . . Koma akatswiri ambiri a Baibulo komanso ofukula zinthu zakale amanena kuti mwala umene unapezeka ku Tel Dan umapereka umboni wamphamvu wakuti Mfumu Davide wotchulidwa m’Baibulo analikodi. Iwo amaona kuti mwalawu ndi chimodzi mwa zinthu zofunika kwambiri zimene zapezeka zomwe magazini ya BAR [Biblical Archaeology Review] inafotokozapo.”—Bible History Daily