Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mulungu Anapereka Mfundo Zokhudza Ukhondo Asayansi Asanazitulukire

Mulungu Anapereka Mfundo Zokhudza Ukhondo Asayansi Asanazitulukire

Patangotsala nthawi yochepa kuti Aisiraeli alowe m’Dziko Lolonjezedwa, zomwe ndi zaka zoposa 3,500 zapitazo, Mulungu anawauza kuti adzawateteza ku “matenda onse oipa” omwe anali ku Iguputo. (Deuteronomo 7:15) Njira imodzi yomwe Mulungu anagwiritsa ntchito ndi kuwapatsa malangizo omveka bwino okhudza ukhondo komanso mmene angapewere kufalitsa matenda. Mwachitsanzo:

  • Malamulo ena ankawauza kuti azisamba komanso kuchapa zovala zawo.—Levitiko 15:4-27.

  • Pa nkhani ya chimbudzi cha munthu, Mulungu ananena kuti: “Muzikhala ndi malo obisika kunja kwa msasa kumene muzipita. Uzikhalanso ndi chokumbira pamodzi ndi zida zako. Ndiyeno podzithandiza kunja kwa msasa, uzikumba dzenje ndi chokumbiracho ndipo ukamaliza kudzithandiza uzitembenuka ndi kufotsera zoipazo.”—Deuteronomo 23:12, 13.

  • Anthu omwe anali ndi matenda opatsirana ankawaika kwaokha mpaka atachira. Asanabwerere, ankayenera kuchapa zovala zawo komanso kusamba n’cholinga choti akhale ‘oyera.’—Levitiko 14:8, 9.

  • Munthu amene wakhudza mtembo ankaikidwanso kwayekha.—Levitiko 5:2, 3; Numeri 19:16.

Malamulo amene Aisiraeli ankayendera akugwirizana ndi mfundo za umoyo komanso ukhondo zomwe anthu a pa nthawiyo anali asanazitulukire.

Nthawi imeneyo mitundu yambiri siinkadziwa mfundo zokhudza ukhondo. Mwachitsanzo:

  • Zonyansa zinkangotayidwa m’misewu. Madzi oipa, zakudya zowonongeka, komanso zinyalala zosasamalidwa zinkachititsa kuti matenda azifalikira kwambiri komanso kuti ana ambiri azimwalira.

  • Madokotala a nthawi imeneyo sankadziwa zambiri zokhudza tizilombo toyambitsa matenda. Munthu akadwala, anthu a ku Iguputo ankagwiritsa ntchito magazi a buluzi, zitosi za mbalame, makoswe akufa, mkodzo komanso buledi wochita nkhungu ngati mankhwala. Nthawi zambiri ankagwiritsanso ntchito ndowe komanso chimbudzi cha munthu pothandiza odwala.

  • Anthu a ku Iguputo ankadwala chifukwa cha tizilombo ta m’madzi oipa a mumtsinje wa Nailo komanso m’ngalande zomwe ankazigwiritsa ntchito pothirira. Nawonso ana ambiri ankamwalira chifukwa cha matenda otsekula m’mimba komanso matenda ena obwera chifukwa cha zakudya zosasamalika bwino.

Ngakhale zinali choncho, Aisiraeli zinthu zinkawayendera bwino ndipo sankadwaladwala chifukwa choti ankatsatira Malamulo a Mulungu okhudza ukhondo.