Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

alashi/​DigitalVision Vectors via Getty Images

KHALANI MASO!

N’chifukwa Chiyani Anthu Akudana Kwambiri?​—⁠Kodi Baibulo Limanena Zotani?

N’chifukwa Chiyani Anthu Akudana Kwambiri?​—⁠Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Masiku ano nkhani zambiri zikumakhala zokhudza anthu akulankhula zinthu zosonyeza chidani, kuchita zachiwawa chifukwa cha tsankho komanso zokhudza nkhondo.

  •   “Anthu akumakonda kulankhulana mawu osonyeza chidani ndiponso zachiwawa pamalo ochezera a pa intaneti chifukwa cha nkhondo yomwe ikuchitika ku Israel ndi Gaza.”​—The New York Times, November 15, 2023.

  •   “Kungoyambira pa 7 October, anthu akhala akulankhulana mawu osonyeza chidani komanso kuchita zachiwawa chifukwa cha tsankho kuposa mmene ankachitira m’mbuyomu.”​—Dennis Francis, president of the United Nations General Assembly, November 3, 2023.

 Si zachilendo kumva anthu akulankhulana mawu osonyeza chidani, kuchita zachiwawa komanso nkhondo. Ndipotu Baibulo limafotokoza za anthu omwe kalekale “[ankakonzekera] kuponya mawu awo opweteka ngati mivi” komanso kumenya nkhondo ndi kuchita zachiwawa. (Salimo 64:3; 120:7; 140:1) Komabe, Baibulo limanena kuti chidani chomwe tikuona masiku ano chili ndi tanthauzo lofunika kwambiri.

Chidani​—Chizindikiro cha nthawi yathu ino

 Baibulo limafotokoza zifukwa ziwiri zimene anthu akudanirana kwambiri masiku ano.

  1.  1. Linalosera za nthawi yomwe “chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.” (Mateyu 24:12) M’malo mokondana, anthu azidzasonyeza makhalidwe olimbikitsa chidani.​—2 Timoteyo 3:1-5.

  2.  2. Chidani chikuchulukirachulukirabe masiku ano chifukwa cha zochita za Satana Mdyerekezi. Baibulo limanena kuti “dziko lonse lili mʼmanja mwa woipayo.”​—1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 12:9, 12.

 Komabe, Baibulo limanenanso kuti posachedwapa Mulungu athetsa zinthu zonse zimene zimayambitsa chidani. Kuwonjezera pamenepa, iye adzathetsa kuvutika konse kumene kumabwera chifukwa cha chidani. Baibulo limalonjeza kuti:

  •   Mulungu “adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kubuula kapena kupweteka. Zakalezo zapita.”​—Chivumbulutso 21:4.