Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KHALANI MASO

N’chifukwa Chiyani Ndale Zimagawanitsa Kwambiri Anthu?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

N’chifukwa Chiyani Ndale Zimagawanitsa Kwambiri Anthu?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Padziko lonse, anthu ambiri sagwirizana pa nkhani za ndale. Bungwe la Pew Research Center linachita kafukufuku mu 2022 m’mayiko 19, ndipo linapeza kuti “65 peresenti ya akuluakulu m’mayikowa ananena kuti pamakhala kutsutsana kwambiri pakati pa anthu amene amatsatira zipani zosiyana.”

 Kodi mwaona kuti m’dera limene mukukhala anthu akugawanika kwambiri chifukwa chosiyana pa nkhani za ndale? N’chifukwa chiyani zili choncho? Kodi pali njira yothetsera vutoli? Taonani zimene Baibulo limanena.

Zimene zimapangitsa anthu kugawanika

 Baibulo linaneneratu kuti m’nthawi yathu ino, yomwe imatchedwa kuti “masiku otsiriza” anthu ambiri adzakhala ndi makhalidwe omwe azidzawapangitsa kuti asamagwirizane.

  •   “Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, . . . osafuna kugwirizana ndi anzawo.”​—2 Timoteyo 3:1-3.

 Ngakhale kuti anthu ambiri amachita khama kuthandizira maboma kuti aziyenda bwino, komabe zimenezi sizimatheka. Zimakhala zovuta kwa anthu amene ali ndi maganizo osiyana kuti agwire ntchito limodzi ndi anzawo pothetsa mavuto ndipo nthawi zina sizitheka n’komwe. Ndiye zotsatirapo zake zimapereka umboni wa zimene Baibulo linaneneratu kalekale.

  •   “Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.”​—Mlaliki 8:9.

 Komabe Baibulo linaneneratu njira yothetsera vutoli. Pali boma lolamuliridwa ndi winawake amene adzachotse mavuto onse omwe amapangitsa anthu kuti azivutika.

Mtsogoleri woyenerera yemwe amasamala za anthu

 Baibulo limanena kuti mtsogoleri woyenerera yemwe angathetseretu mavuto onse ndi Yesu Khristu. Iye ali ndi mphamvu, ulamuliro komanso ndi wofunitsitsa kubweretsa mgwirizano ndi mtendere kwa anthu onse.

  •   “M’masiku ake, wolungama adzaphuka, ndipo padzakhala mtendere wochuluka.”​—Salimo 72:7.

  •   “Mitundu yonse ya anthu idzamutumikira.”​—Salimo 72:11.

 Yesu ndi mtsogoleri wabwino ndipo amasamala za anthu komanso akufuna kuwathandiza, makamaka omwe akuchitiridwa zinthu zopanda chilungamo.

  •   “Adzalanditsa wosauka amene akufuula popempha thandizo, wosautsika ndi aliyense wopanda womuthandiza. Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka. Adzawombola miyoyo yawo ku chipsinjo ndi chiwawa.”​—Salimo 72:12-14.

 Dziwani zambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu lomwe ndi boma la kumwamba lotsogoleredwa ndi Yesu. Dziwani zimene mungachite kuti mupeze madalitso komanso mmene mungathandizire Ufumu wake.