Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Rui Almeida Fotografia/Moment via Getty Images

KHALANI MASO

Padziko Lonse Pakuchitika Zachiwawa Zokhudza Ndale—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Padziko Lonse Pakuchitika Zachiwawa Zokhudza Ndale—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Zachiwawa zokhudza ndale zikuchitika padziko lonse.

  •   Ku Mexico, andale 39 anaphedwa komanso kunachitika zachiwawa zina zokhudza ndale ndipo zimenezi zinasokoneza zisankho za m’chaka cha 2023-2024 m’dzikoli.

  •   Chaposachedwapa ku Europe kwakhala kukuchitika ziwawa zambiri zokhudza ndale, kuphatikizapo anthu omwe ankafuna kupha nduna yaikulu ya ku Slovakia pa 15 May, 2024.

  •   Ku United States anthu ali ndi mantha chifukwa pa 15 September, 2024, zikuoneka kuti munthu winanso amafuna kupha Donald Trump, yemwe ndi pulezidenti wakale wa dzikoli.

 N’chifukwa chiyani padzikoli pakuchitika zachiwawa zambiri zokhudza ndale? Kodi zachiwawazi zidzatha? Kodi Baibulo limanena zotani?

Baibulo linaneneratu kuti anthu adzagawanika chifukwa cha ndale

 Baibulo linaneneratu kuti m’nthawi yathu ino, yomwe imadziwika kuti “masiku otsiriza,” anthu ambiri adzakhala ndi makhalidwe omwe amalimbikitsa zachiwawa komanso kusagwirizana.

  •   “Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Anthu adzakhala . . . osayamika, osakhulupirika, . . . osafuna kugwirizana ndi ena, . . . oopsa, . . . ochitira anzawo zoipa, osamva za ena [ndiponso] odzitukumula chifukwa cha kunyada.”—2 Timoteyo 3:1-4.

 Baibulo linaneneratunso kuti anthu ambiri azidzaukira maboma komanso kuchita zipolowe pazifukwa za ndale. (Luka 21:9, mawu a m’munsi) Komabe zachiwawa zomwe zikuchitika pazifukwa za ndale komanso kusagwirizana zitha posachedwapa.

Zachiwawa zomwe zikuchitika pazifukwa za ndale zidzatha

 Baibulo limafotokoza kuti Mulungu adzachotsa maboma onse a anthu n’kubweretsa boma lake lakumwamba.

  •   “Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene . . . udzaphwanya nʼkuthetsa maufumu ena onsewa ndipo ndi ufumu wokhawu umene udzakhalepo mpaka kalekale.”—Danieli 2:44.

 Ufumu wa Mulungu udzathandiza anthu kukhala ogwirizana komanso kuti padziko lonse pakhale mtendere.

  •   Wolamulira wake Yesu Khristu, amatchulidwa kuti “Kalonga wa Mtendere,” ndipo adzaonetsetsa kuti padzikoli padzakhale “mtendere [womwe] sudzatha.”—Yesaya 9:6, 7.

  •   Ngakhale panopa, anthu omwe ndi nzika za Ufumuwu akuphunzira zimene angachite kuti azikhala mwamtendere. Ndipo akuchita zomwe Baibulo limanena kuti: “Adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo, ndipo mikondo yawo adzaisula kuti ikhale zida zosadzira mitengo. Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:3, 4.

 Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti, “Kodi Ufumu wa Mulungu Udzachita Chiyani?” ndiponso onerani vidiyo yakuti Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?