Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

sinceLF/E+ via Getty Images

KHALANI MASO

Ndi Ndani Angateteze Anthu Wamba Pankhondo?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Ndi Ndani Angateteze Anthu Wamba Pankhondo?—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Mogwirizana ndi lipoti la bungwe la United Nations:

  •   Kuyambira pa 7 mpaka pa 23 October 2023, nkhondo ya pakati pa Israel ndi Gaza, inaphetsa anthu oposa 6,400 komanso kuvulaza ena okwana 15,200 ndipo ambiri anali anthu wamba. Kuwonjezera pamenepa, anthu masauzande ambiri anakakamizika kuthawa m’nyumba zawo.

  •   Pofika pa 24 September 2023, nkhondo ya pakati pa dziko la Russia ndi Ukraine inaphetsa anthu wamba a ku Ukraine okwana 9,701 komanso kuvulaza ena okwana 17,748.

 Kodi Baibulo limalonjeza zotani kwa anthu omwe akuvutika ndi nkhondo?

Chifukwa chotipangitsa kukhala ndi chiyembekezo

 Baibulo limalonjeza kuti Mulungu ‘adzathetsa nkhondo padziko lonse lapansi.’ (Salimo 46:9) Iye adzachititsa boma lakumwamba kapena kuti ufumu, kuti udzalowe m’malo mwa maboma onse a anthu. (Danieli 2:44) Ufumu wa Mulunguwu, udzathetsa mavuto onse a anthu.

 Onani zimene Yesu Khristu amene ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu adzachite:

  •   “Adzapulumutsa wosauka amene akufuula popempha thandizo, komanso wonyozeka ndi aliyense amene alibe womuthandiza. Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka. Adzawapulumutsa kuti asaponderezedwe komanso kuchitiridwa zachiwawa.”​—Salimo 72:12-14.

 Mulungu adzagwiritsa ntchito Ufumu wake pothetseratu mavuto onse amene anayamba chifukwa cha nkhondo komanso zachiwawa.

  •   “Iye adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kubuula kapena kupweteka. Zakalezo zapita.”​—Chivumbulutso 21:4.

 Posachedwapa, Ufumu wa Mulungu uyamba kulamulira dziko lonse lapansi. Baibulo linaneneratu zokhudza “nkhondo ndi malipoti a nkhondo” zomwe zikuchitika masiku ano. (Mateyu 24:6) Choncho nkhondozi ndiponso zinthu zina zonse zoipa zomwe zikuchitikazi, zikusonyeza kuti tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ a maulamuliro a anthu.​—2 Timoteyo 3:1.