Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

hadynyah/E+ via Getty Images

KHALANI MASO

Vuto la Kusowa kwa Chakudya Padziko Lonse Chifukwa cha Nkhondo ndi Kusintha kwa Nyengo—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Vuto la Kusowa kwa Chakudya Padziko Lonse Chifukwa cha Nkhondo ndi Kusintha kwa Nyengo—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Nkhondo ya ku Ukraine ikupitiriza kuwonjezera vuto la kusowa kwa chakudya padziko lonse kuphatikizapo mavuto obwera chifukwa cha kusintha kwa nyengo. Zimenezi zikuchitika makamaka m’mayiko ongotukuka kumene omwe anthu ambiri akuvutika kupeza chakudya chokwanira.

  •   “Nkhondo, kusintha kwa nyengo, komanso kukwera mitengo kwa katundu ndi zinthu zina zikuchititsa kuti kupanga chakudya kuzikhala kovuta komanso chakudya chizisowa.”​—António Guterres, mlembi wamkulu wa bungwe la UN, July 17, 2023.

  •   “Akatswiri akunena kuti zimene dziko la Russia lachita potuluka mumgwirizano wotumiza chakudya kumayiko ena zichititsa kuti vuto la kusowa kwa chakudya padziko lonse likule kwambiri komanso zichititsa kuti m’mayiko osauka chakudya chizikwera mitengo, makamaka ku North Africa komanso ku Middle East.”​—Atalayar.com, July 23, 2023.

 Kodi Baibulo limati chiyani pa nkhani ya kusowa kwa chakudya komanso mmene zinthu zidzakhalire m’tsogolomu?

Baibulo linaneneratu zokhudza vuto la kusowa kwa chakudya

  •   Yesu analosera kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina. Kudzakhala njala ndi zivomezi m’malo osiyanasiyana.”​—Mateyu 24:7.

  •   Buku la Chivumbulutso limafotokoza za okwera pamahatchi 4 ophiphiritsa. Wokwera pahatchi wina akuimira nkhondo. Kenako panabwera wokwera pahatchi wina yemwe akuimira njala, kutanthauza kuti chakudya chizidzakhala chochepa komanso chokwera mitengo. “Nditayang’ana, ndinaona hatchi yakuda. Wokwerapo wake anali ndi sikelo m’dzanja lake. Kenako ndinamva mawu . . . Mawuwo anali akuti: “Kilogalamu imodzi ya tirigu, mtengo wake ukhala dinari imodzi, ndipo makilogalamu atatu a balere, mtengo wake ukhala dinari imodzi. Koma musawononge mafuta a maolivi ndi vinyo.”​—Chivumbulutso 6:5, 6.

 Maulosi a m’Baibulo amenewa okhudza kusowa kwa chakudya akukwaniritsidwa panopa monga mmene Baibulo linaneneratu kuti tikukhala “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1) Kuti muphunzire zambiri zokhudza “masiku otsiriza” komanso okwera pamahatchi 4 otchulidwa m’buku la Chivumbulutso, onerani vidiyo yakuti Dzikoli Lasintha Kwambiri Kuyambira mu 1914 ndiponso werengani nkhani yakuti “Kodi Anthu 4 Okwera Pamahatchi Akuimira Chiyani?

Kodi Baibulo lingakuthandizeni bwanji?

  •   M’Baibulo muli malangizo amene angatithandize kuti tipirire mavuto athu kuphatikizapo kukwera mitengo kwa chakudya kapenanso kusowa kwa chakudya. Onani zitsanzo zina munkhani yakuti “Zimene Mungachite Ngati Mukupeza Ndalama Zochepa.”

  •   Baibulo limatipatsanso chiyembekezo kuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo. Limatilonjeza kuti “padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri” ndipo aliyense adzakhala ndi chakudya chokwanira. (Salimo 72:16) Kuti mudziwe zambiri zokhudza chiyembekezo chimenechi komanso chifukwa chake muyenera kukhulupirira zimenezi, werengani nkhani yakuti “Tiziyembekezera Kuti Zinthu Zidzakhala Bwino M’tsogolo.”