Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Moyo Udzabwereranso Mwakale?—Mmene Baibulo Lingakuthandizireni M’nthawi ya Mliri

Kodi Moyo Udzabwereranso Mwakale?—Mmene Baibulo Lingakuthandizireni M’nthawi ya Mliri

 Mayi Angela Merkel amene ndi mtsogoleri wa dziko la Germany ananena kuti: “Tonse tikufuna moyo utabwereranso mwakale.”

 Mwina mungagwirizane ndi zimene a Merkel ananena tikaganizira mmene zinthu zilili padziko lonse chifukwa cha mliri wa COVID-19. Koma kodi zinthu zinali bwanji poyamba? Nanga anthu akuyembekezera kuti zinthu zikhala bwanji m’tsogolo muno?

  •   Kuyambiranso kuchita zinthu monga mwa nthawi zonse. Ena akulakalaka atamachezanso ndi anzawo, kuhagana komanso kupatsana moni wapamanja. Dr. Anthony Fauci a, anafotokoza kuti anthu ena amaona kuti “kukhala ndi moyo monga mwa nthawi zonse,” kukuphatikizapo “kupita ku malo odyera ndi malo ena osangalalirako.”

  •   Kutukula moyo wawo. Anthu ena akuona kuti mwina tsopano angakhale ndi “moyo wabwinoko” kuposa poyamba. Akuona kuti zinthu ngati ntchito zomwe zimafuna mphamvu ndi nthawi yambiri, kusankhana chifukwa chosiyana mtundu ndi kapezedwe ka chuma, komanso kuchuluka kwa anthu omwe akuvutika ndi matenda a maganizo, zikufunika kusintha. Mkulu amene anayambitsa bungwe la World Economic Forum, a Klaus Schwab, ananena kuti: “Mliriwu wapereka mwayi wa kanthawi kochepa woti tiganizirenso za moyo wathu komanso kusintha zinthu padzikoli.”

 Kwa anthu ena, mliriwu wawabweretsera mavuto ambiri moti akuona kuti moyo sungabwererenso mwakale. Mwachitsanzo, ena anachotsedwa ntchito, alibe malo okhala, amadwaladwala mwinanso mnzawo kapena wachibale wawo anamwalira.

 Kunena zoona, palibe amene akudziwa kuti zinthu zidzakhala bwanji mliriwu ukadzatha. (Mlaliki 9:11) Komabe, Baibulo lingatithandize kuyembekezera zinthu zabwino kutsogoloku. Lingatithandizenso kupirira mavuto aliwonse omwe tingakumane nawo. Ndipotu limatiuza motsimikiza kuti kutsogoloku zinthu zidzakhala bwino kwambiri kuposa mmene anthu akuganizira.

Kodi tiziuwona bwanji mliri wa COVID-19?

 Kalekale, Baibulo linaneneratu kuti kudzakhala matenda kapena kuti “miliri” m’nyengo ya “mapeto a nthawi ino.” (Luka 21:11; Mateyu 24:3) Choncho tikaganizira zomwe Baibulo limanenazi, mliri wa COVID-19 uli m’gulu la zinthu zapadera zomwe tikuyembekezera kuti zizichitika pokwaniritsa maulosi a m’Baibulo. Baibulo linaneneratunso kuti kudzakhala nkhondo, zivomezi zoopsa komanso njala.

 Kodi kudziwa zimenezi n’kothandiza bwanji? Ngakhale kuti mavuto omwe abwera ndi mliriwu akhoza kutha, komabe Baibulo limatiuza kuti tikukhala “nthawi yapadera komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1) Kudziwa zimenezi kumatithandiza kuti tisamayembekezere kuti zinthu zisintha n’kumangoyenda bwino m’tsogolomu.

 Baibulo limatithandiza kuona zinthu moyenera: Ngakhale kuti zinthu zikuipiraipira, koma posachedwapa zinthu zisintha kwambiri padzikoli. Kodi zisintha mwanjira yanji?

Tsogolo labwino kwambiri lomwe simumaliganizira

 Sikuti Baibulo linangolosera za mavuto omwe akuchitika pakali pano, koma linaneneratunso za zinthu zomwe zikuyembekezeka kuchitika posachedwa. Linalonjeza za tsogolo labwino kwambiri lomwe maboma a anthu sangakwanitse kulibweretsa, koma Mulungu yekha. Mulunguyo “adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.”—Chivumbulutso 21:4.

 Yehova b Mulungu akulonjeza kuti: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga n’zatsopano.” (Chivumbulutso 21:5) Iye adzathetsa mavuto padzikoli kuphatikizapo mavuto omwe abwera chifukwa cha mliriwu. Iye adzatipatsa zinthu izi:

  •   Matupi angwiro komanso athanzi ndipo palibenso amene adzadwale, kuvutika maganizo kapenanso kumwalira.—Yesaya 25:8; 33:24.

  •   Ntchito zomwe tidzasangalala nazo osati ntchito zopanikiza komanso zofuna nthawi yambiri.—Yesaya 65:22, 23.

  •   Moyo wa mwanaalirenji chifukwa sikudzakhalanso umphawi ndi njala.—Salimo 72:12, 13; 145:16.

  •   Sitidzavutikanso maganizo chifukwa cha zinthu zoipa zomwe zinatichitikira m’mbuyomo. Tidzaonanso achibale athu omwe anamwalira ataukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo.—Yesaya 65:17; Machitidwe 24:15.

 Kodi kudziwa zimenezi n’kothandiza bwanji? Baibulo limati: “Chiyembekezo chimene tili nachochi chili ngati nangula.” (Aheberi 6:19, onani mawu am’munsi) Chiyembekezo cha zinthu zabwino zomwe zikubwera m’tsogolo, chimatithandiza kuti tisamakhale ndi nkhawa. Chingatithandize kuti tizipirira mavuto omwe tikulimbana nawo panopo, kuchepetsa nkhawa komanso kuti tizikhalabe osangalala.

 Koma kodi tingakhulupiriredi zimene Baibulo limalonjezazi? Werengani nkhani yakuti: “Baibulo ndi Lodalirika Ndipo Limatiuza Choonadi.”

Mfundo za m’Baibulo zomwe zingatithandize pamene tikuyembekezera kutha kwa mliriwu

  •   Moyo ndi wamtengo wapatali

     Lemba: “Nzeru zimasunga moyo wa eni nzeruzo.”—Mlaliki 7:12.

     Mmene mungagwiritsire ntchito mfundoyi: Muzisankha zochita mwanzeru kuti mudziteteze ku matenda. Ganizirani mmene zinthu ziliri m’dera lomwe mukukhalalo. Muyenera kuganizira njira zomwe zingakuthandizeni kukhala wotetezeka, kuchuluka kwa anthu omwe akupezeka ndi matendawa m’deralo komanso kuchuluka kwa anthu omwe anamaliza kulandira katemera.

  •   Pitirizani kuchita zinthu mosamala

     Lemba: “Munthu wanzeru amachita mantha ndipo amapatuka pa choipa, koma wopusa amapsa mtima ndiponso amakhala wodzidalira.”—Miyambo 14:16.

     Mmene mungagwiritsire ntchito mfundoyi: Pitirizani kutsatira njira zodzitetezera. Akatswiri akukhulupirira kuti mliri wa koronavairasi ukhalapobe kwa nthawi yaitali.

  •   Muzigwiritsa ntchito malangizo odalirika

     Lemba: “Munthu amene sadziwa zinthu amakhulupirira mawu alionse, koma wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.”—Miyambo 14:15

     Mmene mungagwiritsire ntchito mfundoyi: Muzisankha mosamala malangizo omwe mukufuna kuyendera. Muyenera kukhala osamala chifukwa ngati mungagwiritse ntchito malangizo olakwika, mukhoza kuika moyo wanu pangozi.

  •   Muziona zinthu moyenera

     Lemba: “Usanene kuti: ‘N’chifukwa chiyani kale zinthu zinali bwino kuposa masiku ano?’ Pakuti si nzeru kufunsa funso lotere.”—Mlaliki 7:10.

     Mmene mungagwiritsire ntchito mfundoyi: Ngakhale kuti mliriwu udakalipo, koma zisakufooketseni. Musamalakelake mmene moyo unalili mliriwu usanayambe ndipo musamangokhalira kuganizira mwayi womwe munataya chifukwa cha malamulo omwe anakhazikitsidwa ndi cholinga chofuna kupewa kufalikira kwa mliriwu.

  •   Muzilemekeza anthu ena

     Lemba: “Lemekezani anthu, kaya akhale amtundu wotani.”—1 Petulo 2:17.

     Mmene mungagwiritsire ntchito mfundoyi: Anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya mliriwu komanso zotsatirapo zake. Muyenera kulemekeza maganizo awo. Komabe popanda kunyoza maganizo awowo, muyenera kutsatira mfundo zabwino zomwe munasankha kuti muziyendera. Muzichita zinthu moganizira anthu omwe sanabayitse, okalamba komanso amene omwe ali ndi mavuto aakulu m’thupi mwawo.

  •   Muzikhala oleza mtima

     Lemba: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima.”—1 Akorinto 13:4.

     Mmene mungagwiritsire ntchito mfundoyi: Muzichita zinthu mokoma mtima ena akamafotokoza nkhawa zawo chifukwa cholephera kuchita zinthu zina zomwe ankachita mliriwu kulibe. Mliriwu ukayamba kuchepa ndipo mukayambiranso kuchita zinthu zina, muzikhala oleza mtima ngati simukukwanitsa kuchita zinthu ngati poyamba.

Mmene Baibulo likuthandizira anthu kupirira pa nthawi ya mliriwu

 A Mboni za Yehova amapeza mphamvu ndi zomwe Baibulo limanena zokhudza mmene moyo udzakhalire m’tsogolo. Zimenezi zimawathandiza kuti asamaganizire kwambiri za mavuto omwe tikukumana nawo panopo. Amalimbikitsana ndi Akhristu anzawo za kufunika kosonkhana nthawi zonse kuti alambire Mulungu. (Aheberi 10:24, 25) Aliyense ndi wolandiridwa pamisonkhano ya Mboni za Yehova. Pa nthawi ya mliriwu, misonkhanoyi ikumachitika kudzera pa vidiyokomfelensi.

 Ambiri aona kuti kuchita misonkhano ndi a Mboni za Yehova kwawathandiza kwambiri pa nthawi yovutayi. Mwachitsanzo, mayi wina amene anapezeka ndi COVID-19 anavomera ataitanidwa kuti adzapezeke pamsonkhano wa Mboni za Yehova wa pa vidiyokomfelensi. Msonkhanowo unamulimbikitsa kwambiri ngakhale kuti anali akudwala. Pambuyo pake ananena kuti: “Ndayamba kuona a Mboni za Yehova ngati anthu a m’banja langa. Kuwerenga Baibulo kumandithandiza kukhala ndi mtendere wamumtima. Zimenezi zimandithandiza kuti ndiziganizira za moyo wabwino wam’tsogolo m’malo moganizira kwambiri mavuto anga. Zikomo pondithandiza kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu ndipo ndakhala ndikufunitsitsa kuchita zimenezi pa moyo wanga.”

a Mkulu wa bungwe la National Institute of Allergy and Infectious Diseases in the United States.

b Yehova ndi dzina la Mulungu lomwe limapezeka m’Baibulo.—Salimo 83:18.