Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pawel Gluza/500Px Plus/Getty Images

KHALANI MASO

Nyama Zakutchire Zachepa ndi 73 Peresenti Poyerekezera ndi Zaka 50 Zapitazi—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Nyama Zakutchire Zachepa ndi 73 Peresenti Poyerekezera ndi Zaka 50 Zapitazi—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Pa 9 October 2024, bungwe la World Wildlife Fund linatulutsa lipoti lomvetsa chisoni kwambiri lokhudza mmene zochita za anthu zakhudzira nyama zakutchire. Lipotili linanena kuti “m’zaka 50 zapitazi (1970-2020), chiwerengero cha nyama zakutchire chatsika ndi 73 peresenti.” Lipotili linachenjeza kuti: “Sitingakhale kuti tikukokomeza kunena kuti zomwe zichitike m’zaka 5 zikubwerazi, zikhudza tsogolo la zamoyo zonse padziko lapansili.”

 N’zomveka kuti anthu ambiri amakhudzika kwambiri ndi malipoti ngati amenewa. Timakonda dziko lathu lokongolali ndipo zimatipweteka tikamaona zamoyo zikuzunzika. Timamva choncho chifukwa Mulungu anatilenga kuti tizisamalira nyama.—Genesis 1:27, 28; Miyambo 12:10.

 Ndiye mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi tidzakwanitsadi kusamalira nyama zakutchire? Kodi Baibulo limanena zotani?’

Pali chiyembekezo

 Ngakhale titayesetsa bwanji kusamalira nyama zakutchire, ndi Mulungu yekha angakwanitse kusamalira bwino nyamazi. Pa Chivumbulutso 11:18, Baibulo linaneneratu kuti Mulungu ‘adzawononga amene akuwononga dziko lapansi.’ Vesi limeneli limatiphunzitsa zinthu ziwiri izi:

  1.  1. Mulungu sadzalola kuti anthu awonongeretu dzikoli.

  2.  2. Posachedwapa Mulungu achitapo kanthu. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi? Chifukwa kuposa kale lonse, panopa m’pamene pali chiopsezo choti anthu akhoza kuwonongeratu nyama zakutchire.

 Kodi Mulungu adzachita chiyani kuti athetse vutoli? Adzagwiritsa ntchito boma lake lakumwamba kapena kuti Ufumu wake kuti ulamulire dziko lonse lapansili. (Mateyu 6:10) Boma limeneli lidzaphunzitsa anthu omvera zimene angachite kuti azisamalira ndi kuteteza nyama zakutchire.—Yesaya 11:9.