Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Surasak Suwanmake/Moment via Getty Images

KHALANI MASO

Nyengo Yotentha Modabwitsa M’chaka cha 2023—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Nyengo Yotentha Modabwitsa M’chaka cha 2023—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Padziko lonse lapansi, anthu akupirira kutentha komwe sikunachitikepo m’mbuyomu zomwe zikupangitsa ngozi zina zam’chilengedwe chifukwa cha kutentha kodabwitsa kumeneku. Tiyeni tione malipoti otsatirawa:

  •   “Mwezi wa June watentha kwambiri padzikoli, kungochokera pamene anthu anayamba kuwerengera kutentha kapena kuzizira kwa nyengo, zaka 174 zapitazo.”​—National Oceanic and Atmospheric Administration, U.S. Department of Commerce, July 13, 2023.

  •   Mayiko a Italy, Spain, France, Germany ndi Poland akhudzidwa ndi vuto la kutentha kwambiri moti kutenthaku kukuyembekezereka kufika pa madigiri 48 kuzilumba za Sicily ndi Sardinia. N’kutheka kuti kutenthaku kukuposa nyengo zonse zomwe zinakhalapo ku Europe.”​—European Space Agency, July 13, 2023.

  •   “Pamene dzikoli likutentha kwambiri, tiziyembekezera kuti kugwa mvula yochuluka ndiponso pafupipafupi, zomwe zichititse kuti madzi asefukire kwambiri.”​—Stefan Uhlenbrook, mkulu woyang’anira zanyengo kubungwe la World Meteorological Organization, July 17, 2023.

 Kodi malipoti amenewa akukudetsani nkhawa? Tiyeni tione zimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi.

Kodi nyengo ikamasintha chonchi ndiye kuti zikukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo?

 Inde. Kutentha kumene kukuchitika padziko lonse komanso mitundu ina ya kusintha kwa nyengo, ndi chizindikiro cha zimene Baibulo linaneneratu kuti zidzachitika masiku ano. Mwachitsanzo, Yesu analosera kuti “kudzaoneka zoopsa ndipo kumwamba kudzaoneka zizindikiro zodabwitsa.” (Luka 21:11) Kutentha kumene kukuchitika padzikoli kukuchititsa mantha ambiri moti akumaganiza kuti padzikoli sipadzakhalanso chamoyo chilichonse.

Kodi padzikoli padzakhala popanda chamoyo chilichonse?

 Ayi. Mulungu analenga dzikoli kuti tizikhalamo mpaka kalekale; sadzalola kuti anthu aliwonongeretu. (Salimo 115:16; Mlaliki 1:4) Yehova walonjeza kuti adzawononga “amene akuwononga dziko lapansi.””​—Chivumbulutso 11:18.

 Baibulo limanena kuti Mulungu adzateteza dzikoli ku ngozi zam’chilengedwe.

  •   “[Mulungu] amachititsa mphepo yamkuntho kukhala bata, moti mafunde a panyanja amadekha” (Salimo 107:29) Mulungu ali ndi mphamvu zolamulira zinthu zam’chilengedwe. Iye angathe kukonza mavuto amene akuchitika panopa m’chilengedwechi omwe akuchititsa kuti anthu azivutika ndi kusintha kwa nyengo.

  •   “Mwatembenukira dziko lapansi kuti mulipatse zinthu zochuluka, mwalilemeretsa kwambiri.” (Salimo 65:9) Mulungu adzadalitsa dzikoli ndipo lidzakhala paradaiso.

 Kuti muphunzire zambiri zimene Baibulo limalonjeza zokhudza kukonza zinthu zachilengedwe zimene zawonongeka m’dzikoli, werengani nkhani yakuti, “Kodi Ndi Ndani Amene Adzapulumutse Dzikoli?