Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Justin Paget/​Stone via Getty Images

Vuto Losungulumwa Padziko Lonse​—Kodi Mungalimbane Nalo Bwanji?

Vuto Losungulumwa Padziko Lonse​—Kodi Mungalimbane Nalo Bwanji?
  •   Lipoti lina kukusonyeza kuti: “Pafupifupi hafu ya achinyamata ndi akuluakulu omwe ku United States, ananena kuti anasungulumwapo ndipo ambiri mwa iwo ndi azaka zapakati pa 18 ndi 25.”​—Our Epidemic of Loneliness and Isolation: The U.S. Surgeon General’s Advisory on the Healing Effects of Social Connection and Community, 2023.

  •   “[Bungwe Loona za Umoyo Padziko Lonse] lakhazikitsa komiti yothandiza anthu kuti asamadzipatule (Commission on Social Connection). Cholinga cha komitiyi ndi kuthandiza anthu kuti moyo wawo usakhale pachiopsezo chifukwa chosungulumwa, kulimbikitsa anthu kuchitira zinthu limodzi ndiponso kupeza njira zabwino zothetsera vuto losungulumwa ngakhale m’mayiko osauka.”​—World Health Organization, November 15, 2023.

 M’Baibulo muli mfundo zomwe zingatithandize kuti tisamavutike kuchita zinthu ndi ena komanso kuti tisamasungulumwe.

Mfundo za m’Baibulo zimene zingatithandize

 Muzipewa kuchita zinthu zimene zingakupangitseni kuti muzikhala nokhanokha. Zinthuzi ndi: Kuthera nthawi yambiri muli pamalo ochezera a pa intaneti. M’malomwake, muzipeza nthawi yocheza ndi anthu pamasom’pamaso komanso kupeza anzanu abwino.

  •   Mfundo ya m’Baibulo: “Mnzako weniweni amakusonyeza chikondi nthawi zonse, ndipo ndi mʼbale amene anabadwa kuti akuthandize pakagwa mavuto.”​—Miyambo 17:17.

 Muziyesetsa kuthandiza anthu ena. Kuchitira ena zinthu zabwino sikumangothandiza kuti tizigwirizana nawo basi, koma kumatichititsanso kukhala osangalala kwambiri.

  •   Mfundo ya m’Baibulo: “Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri kuposa kulandira.”​—Machitidwe 20:35.

 Fufuzani zambiri pawebusaiti yathu kuti mupeze mfundo zochokera m’Baibulo zokuthandizani kuti muzigwirizana kwambiri ndi anzanu.