Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Francesco Carta fotografo/Moment via Getty Images

Anthu Ambiri Akusungulumwa​—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Anthu Ambiri Akusungulumwa​—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Kafukufuku wina yemwe anachitika posachedwapa m’mayiko ambiri padzikoli, a akusonyeza kuti munthu mmodzi pa anthu 4 alionse amasungulumwa.

  •   “Aliyense angakhale ndi vuto losowa anthu ocheza nawo posatengera msinkhu kapenanso komwe amakhala.”​—Chido Mpemba, wachiwiri kwa tcheyamani wa komiti yothandiza anthu kuti asamadzipatule yotchedwa World Health Organization’s Commission on Social Connection.

 Anthu amaganiza kuti anthu okhawo omwe amadzipatula ndi amene amasungulumwa koma zimenezi si zoona. Zoona zake n’zakuti ngakhale anthu omwe zinthu zikuwayendera bwino, omwe ali pabanja, ana komanso amene ali ndi thanzi labwino nawonso amasungulumwa. Kudzipatula komanso kusungulumwa kungawononge thanzi komanso maganizo a munthu.

  •   Dokotola wina wochita ma opaleshoni ku U.S ananena kuti: “Kusungulumwa kuli ndi mavuto ambiri. Moyo wa munthu ukhoza kukhala pa chiopsezo chifukwa chosachita zinthu ndi ena mofanana ndi munthu amene amasuta ndudu 15 pa tsiku.”​—Dr. Vivek Murthy.

Zimene Baibulo limanena

 Mlengi wathu samafuna kuti tizidzipatula. Kuyambira pachiyambi, Mulungu ankafuna kuti anthu azisangalala kuchitira zinthu limodzi ndi anzawo.

  •   Mfundo ya M’Baibulo: “Kenako Yehova Mulungu anati: “Si bwino kuti munthu azikhala yekha. Ndimupangira womuthandiza, monga mnzake womuyenerera.”​—Genesis 2:18.

 Mulungu amafuna kuti tikhale naye pa ubwenzi. Iye amalonjeza kuti adzatiyandikira, ifeyo tikamayesetsa kumuyandikira.​—Yakobo 4:8.

  •   Mfundo ya m’Baibulo: “Osangalala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu chifukwa Ufumu wakumwamba ndi wawo.”​—Mateyu 5:3.

 Mulungu amafuna kuti tizimulambira limodzi ndi anthu ena. Tikamachita zimenezi timakhala osangalala.

  •   Mfundo ya m’Baibulo: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa nkhani yosonyezana chikondi ndiponso kuchita zabwino. Tisasiye kusonkhana pamodzi, . . . Koma tiyeni tilimbikitsane.”​—Aheberi 10:24, 25.

 Kuti mudziwe mmene mungapewere kukhala osungulumwa, werengani nkhani yakuti, “Anthu Ambiri Amasungulumwa Ngakhale Kuti Pali Njira Zambiri Zolankhulirana.”

a The Global State of Social Connections, by Meta and Gallup, 2023.