NTCHITO YOITANIRA ANTHU KU CHIKUMBUTSO
Yesu Adzathetsa Nkhondo
Ali padzikoli, Yesu anasonyeza chikondi chachikulu kwa anthu onse, moti anafika popereka moyo wake kuti awawombole. (Mateyu 20:28; Yohane 15:13) Posachedwapa, adzasonyeza umboni winanso wakuti amakonda anthu onse pogwiritsa ntchito mphamvu zake monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo ‘adzathetsa nkhondo padziko lonse lapansi.’—Salimo 46:9.
Taonani zimene Baibulo limanena zokhudza zimene Yesu adzachite:
“Adzapulumutsa wosauka amene akufuula popempha thandizo, komanso wonyozeka ndi aliyense amene alibe womuthandiza. Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka, ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka. Adzawapulumutsa kuti asaponderezedwe komanso kuchitiridwa zachiwawa.”—Salimo 72:12-14.
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zonse zimene Yesu anatichitira komanso zimene adzatichitire posachedwapa? Pa Luka 22:19, Yesu anauza otsatira ake kuti azikumbukira imfa yake. N’chifukwa chake, chaka chilichonse a Mboni za Yehova amakumana pamodzi kuti achite mwambo wokumbukira imfa yake pa tsiku limene anaphedwa. Tikukuitanani kuti mudzakhale nafe Pamwambo Wokumbukira imfa yake Lamlungu pa 24 March 2024.