NTCHITO YOITANIRA ANTHU KU CHIKUMBUTSO
Yesu Adzathetsa Zoipa Zonse
Yesu amadziwa bwino mmene munthu amamvera akamavutika chifukwa cha uchigawenga ndi zinthu zina zopanda chilungamo. Iye ananamiziridwa kuti wapalamula mlandu, anamenyedwa ngakhale kuti sanalakwe, anaimbidwa mlandu mopanda chilungamo, anamangidwa wosalakwa komanso anafa imfa yowawa kwambiri. Ngakhale kuti anali wosalakwa, iye anapereka ndi mtima wake wonse, “moyo wake dipo kuti awombole anthu ambiri.” (Mateyu 20:28; Yohane 15:13) Monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, posachedwapa, Yesu adzabweretsa chilungamo padziko lonse ndipo adzathetseratu zoipa zonse.—Yesaya 42:3.
Baibulo limafotokoza zimene zidzachitike Yesu akadzayamba kulamulira padzikoli:
“Oipa sadzakhalaponso. Udzayangʼana pamene ankakhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”—Salimo 37:10, 11.
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zonse zimene Yesu anatichitira komanso zimene adzatichitire posachedwapa? Pa Luka 22:19, Yesu anauza otsatira ake kuti azikumbukira imfa yake. N’chifukwa chake, chaka chilichonse a Mboni za Yehova amakumana pamodzi kuti achite mwambo wokumbukira imfa yake pa tsiku limene anaphedwa. Tikukuitanani kuti mudzakhale nafe Pamwambo Wokumbukira imfa yake Lamlungu pa 24 March 2024.