Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KHALANI MASO

Zachiwawa Zowombera Ndi Mfuti Zikuchitika Padziko Lonse—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Zachiwawa Zowombera Ndi Mfuti Zikuchitika Padziko Lonse—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 M’mwezi wa July 2022, manyuzipepala anatulutsa malipoti otsatirawa okhudza zachiwawa zowombera ndi mfuti zomwe zikuchitika padziko lonse:

  •   “Kuphedwa kwa Shinzo Abe yemwe anali katswiri pa nkhani zandale ku Japan, [Nduna Yaikulu yakale] kwachititsa mantha nzika za m’dzikoli komanso anthu ena padziko lonse. Izi zili chonchi chifukwa chakuti ku Japan sikuchitikachitika zachiwawa komanso kuli malamulo okhwima okhudza kugwiritsa ntchito mfuti.”—July 10, 2022, The Japan Times.

  •   “Anthu ambiri m’dziko la Denmark ali ndi mantha, munthu wina wokhala ndi mfuti atapha anthu atatu pamalo ena pomwe pali mashopu akuluakulu ku Copenhagen.”—July 4, 2022, Reuters.

  •   “Ku South Africa: Anthu okwana 15 aphedwa, anthu okhala ndi mfuti atawaombera pa bala ina ku Soweto.”—July 10, 2022, The Guardian.

  •   “Anthu opitirira 220 aphedwa atawomberedwa ndi mfuti paholide ya pa 4 July ku United States.”—July 5, 2022, CBS News.

 Kodi tiyembekezere kuti zachiwawazi zidzatha? Nanga Baibulo limanena zotani?

Zachiwawa Zidzatha

 Baibulo limati nthawi yomwe tikukhalayi ndi “masiku otsiriza” ndipo ndi nthawi imene anthu ndi oopsa, ankhanza komanso aukali. (2 Timoteyo 3:1, 3) Zachiwawazi zimachititsa kuti anthu azikhala mwamantha. (Luka 21:11) Komabe, Baibulo limalonjeza za nthawi imene zachiwawa zidzatha ndipo anthu “adzakhala pamalo amtendere ndi pamalo otetezeka. Adzakhala m’malo abata ndiponso aphee!” (Yesaya 32:18) Koma kodi zidzatha bwanji?

 Mulungu adzachotsa anthu oipa komanso adzawononga zida zankhondo.

  •   “Koma oipa adzachotsedwa padziko lapansi ndipo achinyengo adzazulidwamo.”—Miyambo 2:22.

  •   “[Mulungu] Akuletsa nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi. Wathyola uta ndi kuduladula mkondo. Ndipo watentha magaleta pamoto.”—Salimo 46:9.

 Mulungu adzachotsa chimene chimayambitsa zachiwawa pophunzitsa anthu kukhala mwamtendere.

  •   “Sizidzavulazana kapena kuwonongana m’phiri langa lonse loyera, chifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.”—Yesaya 11:9.

  •   Ngakhale masiku athu ano, Mulungu akuphunzitsa anthu padziko lonse kuti azipewa kuchita zachiwawa komanso kugwiritsa ntchito zida zankhondo. Iye akuchita zimenezi powaphunzitsa ‘kusula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo ndi mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo.’—Mika 4:3.

 Kuti mudziwe zambiri zokhudza dziko lomwe anthu adzakhalemo mopanda mantha mogwirizana ndi zomwe Baibulo limalonjeza, werengani nkhani yakuti, “Kodi N’zotheka Kukhala Mopanda Mantha?

 Kuti mudziwe mmene zachiwawa zidzathere mpaka kalekale, werengani nkhani yakuti, “Mtendere Udzabweradi Padziko Lapansi!