Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ismail Sen/Anadolu Agency via Getty Images

KHALANI MASO

Ku Turkey ndi ku Syria Kwachitika Zivomerezi Zoopsa—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Ku Turkey ndi ku Syria Kwachitika Zivomerezi Zoopsa—Kodi Baibulo Limanena Zotani?

 Lolemba pa 6 February 2023, ku Turkey ndi ku Syria kunachitika zivomerezi zoopsa.

  •   “Lolemba, chivomerezi champhamvu chinapha anthu oposa 3,700 mbali yaikulu ya dziko la Turkey ndiponso kumpoto chakumadzulo kwa dziko la Syria. Chivomerezichi chinachitika pa nthawi yomwe kunja kunkazizira kwambiri zomwe zinawonjezera mavuto kwa anthu amene anavulala kapenanso amene nyumba zawo zinawonongeka. Zimenezi zinachititsanso kuti ntchito yopulumutsa anthu ikhale yovuta.”​—Reuters, February 6, 2023.

 Timamva kuwawa kwambiri mumtima tikamawerenga nkhani zomvetsa chisoni ngati zimenezi. Pa nthawi ngati imeneyi tiyenera kudalira kwambiri Yehova a yemwe ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.” (2 Akorinto 1:3) Iye anatipatsa ‘Malemba [amene] amatipatsa chiyembekezo . . . ndiponso amatilimbikitsa.’​—Aroma 15:4.

 Baibulo limatiphunzitsa:

  •   Zimene zinanenedweratu zokhudza zivomerezi.

  •   Kumene tingapeze chitonthozo komanso chiyembekezo.

  •   Mmene Mulungu adzathetsere mavuto onse.

 Kuti mudziwe zimene Baibulo limanena zokhudza zimenezi, werengani nkhani izi:

a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu.​—Salimo 83:18.