Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KHALANI MASO

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yopembedza Zizindikiro

Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani Yopembedza Zizindikiro

 Nyuzipepala ina ya Katolika, inanena zomwe zinachitika pamwambo womwe unachitika ku St. Peter’s Basilica pa 25 March 2022. Inafotokoza kuti mwambowu Papa Francis anaima patsogolo pa chifaniziro cha Mariya “atatsinzina komanso ataweramitsa mutu wake n’kumapemphera mwakachetechete.” Iye “ankapemphera kwa Mariya” kuti kukhale mtendere. (Catholic News Service) Nyuzipepala ina ya ku Vatican inawonjezera kuti: “Papa wapempherera mwapadera anthu a ku Russia ndi Ukraine kwa Mariya wa Mtima Woyera.”—Vatican News.

 Inuyo mukuganiza bwanji? Kodi ndi zoyenera kuti tizipemphera kwa zifaniziro kapenanso kuzigwiritsa ntchito popembedza? Taganizirani mavesi a m’Baibulo awa:

  •   “Usadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso cham’madzi a padziko lapansi. Usaziweramire kapena kuzitumikira, chifukwa ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha.”—Ekisodo 20:4, 5. a

  •   “Mafano awo ndi opangidwa ndi siliva ndi golide, Ntchito ya manja a munthu wochokera kufumbi. Pakamwa ali napo koma salankhula, Maso ali nawo koma saona. Makutu ali nawo koma satha kumva. Mphuno ali nayo koma sanunkhiza. Manja ali nawo, koma sakhudza kanthu. Mapazi ali nawo koma sayenda. Satulutsa mawu ndi mmero wawo. Amene amawapanga adzafanana nawo. Onse amene amawakhulupirira adzakhala ngati mafanowo.”—Salimo 115:4-8.

  •   “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli, ndipo sindidzapereka ulemu wanga kwa wina aliyense kapena kupereka ulemerero wanga kwa zifaniziro zogoba.”—Yesaya 42:8.

  •   “Thawani kupembedza mafano.”—1 Akorinto 10:14.

  •   “Pewani mafano.”—1 Yohane 5:21.

 Kuti mudziwe zambiri zomwe Baibulo limanena pa nkhani yogwiritsa ntchito zifaniziro popembedza, werengani nkhani yakuti “Zimene Baibulo Limanena—Zifaniziro” kapena onerani vidiyo yakuti Kodi Mulungu Amafuna Kuti Anthu Azigwiritsa Ntchito Zizindikiro Pomulambira?

 Mwina mungakondenso kumva zomwe Baibulo limanena pa nkhani izi:

Photo credit: Vincenzo Pinto/AFP via Getty Images

a Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Werengani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?